Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/95 tsamba 4
  • Gwiritsirani Ntchito Mabrosha Osiyanasiyana Mu Utumiki Wanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Gwiritsirani Ntchito Mabrosha Osiyanasiyana Mu Utumiki Wanu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Lengezani Uthenga Wabwino wa Ufumu ndi Mabrosha
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Tsanzirani Yehova mwa Kusamalira Ena Moona Mtima
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Gwiritsani Ntchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Kabuku Katsopano Kamene Tidzagawira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 7/95 tsamba 4

Gwiritsirani Ntchito Mabrosha Osiyanasiyana Mu Utumiki Wanu

1 Anthu lerolino amafuna kumva nkhani zosiyanasiyana. Pamene muli mu utumiki wakumunda mkati mwa July, mungakhale ndi mabrosha osiyanasiyana, mukumagwiritsira ntchito imene anthu a m’gawolo angakonde. Kumbukiraninso kugaŵira buku lakuti Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe kwa eninyumba pamene mugaŵira mabroshawo. Mungasankhe nkhani imodzi m’bukulo imene imagwirizana bwino ndi brosha limene mukuligaŵira. Mwinamwake mungakonde kuyesa umodzi wa maulaliki aŵa:

2 Pogaŵira brosha lakuti “Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso,” mungafunse kuti:

◼ “Kodi muganiza dziko lingakhale lotani ngati lingalamuliridwe ndi Mulungu yekha? [Yembekezani yankho.] Kuti Mulungu atenge ulamuliro wa dziko lonse lapansi nzimene kwenikweni timapempha pamene timapemphera Pemphero la Ambuye, kapena la Atate Wathu, limene Yesu anatiphunzitsa. [Tsegulani patsamba 3, ndi kuŵerenga ndime yoyamba, imene imagwira mawu Mateyu 6:10.] Ngati mufuna kukhala m’dziko longa limenelo, muyenera kuŵerenga brosha limeneli.” Ligaŵireni.

3 Brosha lakuti “Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira” lingagaŵiridwe motere:

◼ “Kodi muganiza kuti kudzakhala tsiku pamene aliyense wa ife sadzatayanso wokondedwa wake mu imfa? [Yembekezani yankho.] Brosha lolembedwa bwino kwambiri limeneli latonthoza anthu ambirimbiri ndi lonjezo lotsimikizirika la Baibulo lakuti tsikulo lidzafika posachedwapa. [Tsegulani patsamba 5, ndi kuŵerenga ndime yachisanu, kuphatikizapo 1 Akorinto 15:21, 22. Ndiyeno sonyezani chithunzithunzi cha patsamba 30.] Pano chithunzithunzi chikusonyeza chisangalalo chimene tingakhale nacho polandira okondedwa athu pachiukiriro. Koma kodi chochitika chosangalatsa chimenecho chidzachitikira kuti? Brosha limeneli lidzakusonyezani yankho la Baibulo pa funso limeneli.” Ngati broshalo lilandiridwa, mungawonjezere kuti: “Ndingakonde kubweranso kuti tidzakambitsirane zowonjezereka pankhaniyi.”

4 Mungagaŵire brosha lakuti “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano,” mwa njira yachindunji yoyambira phunziro la Baibulo motere:

◼ Anthu ambiri ali ndi mafunso onena za Baibulo. Mwinamwake mwalingalirapo za yankho pa imodzi ya ameneŵa. [Tsegulani patsamba 30.] Funso lomalizira ili lakondweretsa ambiri: ‘Kodi mungakonzekere motani kukhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso?’” Ngati mukambitsirana ndime 57-8 pamasamba 29-30 ndi kuŵerenga Chivumbulutso 21:3, 4, mudzakhala mutayala maziko oyambira phunziro la Baibulo. Malizani mwa kusiya brosha ndi kupangana za kubweranso pamene mudzakambitsirana ena a mafunsowo.

5 Mwina mungafune kuyesa ulaliki wosavuta uwu ndi brosha lakuti “Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha”:

◼ “Chimodzi cha zinthu zimene ndinaphunzira choyamba m’Baibulo ndicho dzina la Mulungu. Kodi mumalidziŵa? [Yembekezani yankho.] Lekani ndikusonyezeni. Lilimo m’Baibulo pa Salmo 83:18. [Ŵerengani.] Brosha limeneli limasonyeza mmene Dzina la Mulungu, Yehova, limapezekera m’zinenero zosiyanasiyana. [Sonyezani bokosi patsamba 8.] Ngati mungakonde kuphunzira zowonjezereka ponena za Yehova ndi zifuno zake, muyenera kuŵerenga brosha limeneli.” Perekani broshalo kwa mwininyumba.

6 Pokhala ndi mabrosha ogwiritsira ntchito osiyanasiyana, ndithudi tili okonzekera bwino ‘kulalikira mawu abwino kwa ofatsa.’—Yes. 61:1.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena