Mbiri Yateokrase
Cyprus: Anafikira chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 1,626 mu February. Msonkhano wawo wapadera wa tsiku limodzi unali ndi opezekapo okwanira 2,249.
Ethiopia: Ofalitsa ochitira lipoti m’mwezi wa February anali 4,587. Chimenechi chinali chiŵerengero chapamwamba chatsopano. Nyumba Zaufumu zatsopano ziŵiri zinapatuliridwa m’mweziwo.
Philippines: Anachitira lipoti chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 119,549 mu February.
Rwanda: Posachedwapa anachita Msonkhano Wachigawo wa “Mantha Aumulungu” m’timagulu tating’ono ndipo chiwonkhetso cha opezekapo chinali 6,062, ndipo 178 anabatizidwa.
Trinidad: Anachitira lipoti chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 6,786 mu February.