Mbiri Yateokrase
Angola: anafikira chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 35,034.
Bangladesh: Pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Kukhulupirira Mawu a Mulungu” panapezeka anthu 142, ndipo obatizidwa anali 14. Chiŵerengero chimenecho chinaŵirikiza nkuposa ziŵerengero zina za anthu amene anabatizidwapo ku Bangladesh pachochitika chimodzi.
Benin: Chiŵerengero chonse cha omwe anapezeka pa Misonkhano Yachigawo yakuti “Kukhulupirira Mawu a Mulungu” chinafika 15,633, ndipo obatizidwa anali 403. Lipoti la December linasonyeza chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 5,351.
Liberia: Mu December munali msonkhano wabwino ku Monrovia, omwe anapezekapo anali 5,158. Anapereka lipoti la mwezi womwewo la chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 2,127.
Madagascar: Mu December ofalitsa anawonjezeka ndi 11 peresenti kuposa avareji ya chaka chatha, ndipo okwana 9,226 anagwira ntchito mu utumiki wakumunda.
St. Maarten: Chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 265 anapereka lipota mu December—kunali kuwonjezeka ndi 10 peresenti kuposa avareji ya chaka chatha. Anachititsa maphunziro a Baibulo a panyumba 310.