Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/96 tsamba 1
  • Kulengeza Uthenga Wabwino Mosaleka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulengeza Uthenga Wabwino Mosaleka
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Adzamva Bwanji?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Kunyumba ndi Nyumba Mosalekeza
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Lalikirani Mwakhama
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Kulalikira Komanso Kuphunzitsa N’kofunika Kwambiri Kuti Tipange Ophunzira
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 8/96 tsamba 1

Kulengeza Uthenga Wabwino Mosaleka

1 Akristu oyambirira anaona utumiki wawo mwamphamvu. Luka anati: “Masiku onse, m’kachisi ndi m’nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira [uthenga wabwino wa, NW] Kristu Yesu.” (Mac. 5:42) Palibe chimene chinatha kuwaletsa, osati ngakhale chizunzo! (Mac. 8:4) Analankhula ndi ena ponena za choonadi tsiku lililonse.

2 Bwanji ponena za ife? Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikuzindikira kufulumira kwa nthaŵi? Kodi ndili wofunitsitsa kupitirizabe kulengeza uthenga wabwino mosaleka?’

3 Zitsanzo Zamakono za Kulalikira Mosaleka: Mlongo wina, wodwala polio, anaikidwa pa makina othandiza kupuma. Sankatha kupita ku Nyumba ya Ufumu kapena kupita kumsonkhano wadera. Koma anali wotanganitsidwa kwambiri ndi kulengeza uthenga wabwino. Mkati mwa zaka zake 37 za kukhala pa makinawo, anatha kuthandiza anthu 17 kuphunzira choonadi! Kodi anazichita motani zimenezo? Ngakhale kuti sanathe kupita kukhomo ndi khomo, tsiku lililonse anapeza njira ya kuchita umboni wamwamwaŵi kwa awo amene anaonana naye.

4 Abale athu ku Bosnia akhala akuyang’anizana ndi nkhondo ndi kusoŵa kwa zinthu. Komabe, iwo akupitiriza kulalikira kwa ena. Ku Sarajevo ofalitsa akhala akuchita avareji ya maola 20 mwezi uliwonse kulankhula ndi ena ponena za uthenga wabwino, ndipo amachititsa avareji ya maphunziro a Baibulo aŵiri aliyense. Mosasamala kanthu za mkhalidwe wawo woipa kwambiriwo, iwo amalalikira ndi kuphunzitsa mosaleka.

5 Achichepere nawonso akusonyeza changu cha mu utumiki. Banja lina la Mboni ku Rwanda linaikidwa m’chipinda mmene asilikali anafuna kuwaphera. Banjalo linapempha chilolezo kuti apemphere choyamba. Anawalola, ndipo mwana wamkazi wamng’onoyo, Deborah, anapemphera momveka kuti: “Yehova, mlungu uno ine ndi Atate tagaŵira magazini asanu. Kodi tidzabwerera motani kwa anthuwa kukawaphunzitsa choonadi ndi kuwathandiza kupeza moyo?” Chifukwa cha chikhulupiriro chake cholimba ndi chikondi chake cha utumiki, banja lonselo silinaphedwe.

6 Lerolino, pali kufunika kwa kufunafuna mpata wa kuchitira umboni kwa ena ndi kufunafuna aja “ofuna moyo wosatha.” (Mac. 13:48, NW) Mogwirizana ndi mkhalidwe wa kumaloko, akulu a mumpingo amapanga makonzedwe a ulaliki wa kagulu wa panthaŵi yabwino, kaya mmaŵa, masana, kapena madzulo. Nkhani za mu Utumiki Wathu Waufumu ndi mbali za pa Msonkhano wa Utumiki, misonkhano yadera, ndi misonkhano yachigawo zimapereka njira za panthaŵi yake ndi chilimbikitso zosonyeza mmene tingakhalire ndi phande pamodzi ndi ena m’mbali zosiyanasiyana za umboni wa Ufumu. Kuwonjezera pa zimenezi, oyang’anira madera ndi oyang’anira zigawo amaphunzitsa ofalitsa ulaliki wa m’khwalala, amasonyeza mogwirira ntchito m’gawo la malo a malonda, ndipo amasonyezanso njira zina zochitira umboni kulikonse kumene kuli anthu. Zonsezi zimalimbikitsa: kusaleka kulengeza uthenga wabwino!

7 Atumwi a Yesu analengeza molimba mtima kuti: “Sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.” Kodi iwo analimbika motani mosasamala kanthu za zopinga zonse? Anapempha Yehova kuti awathandize, ndipo anaterodi, ndipo iwo “anadzazidwa onse ndi mzimu woyera, nalankhula mawu a Mulungu molimbika mtima.” (Mac. 4:20, 29, 31) Si aliyense amene angadalitsidwe ndi zokumana nazo zabwino kwambiri za mu utumiki, koma ngati timakhumbadi kulengeza uthenga wabwino mosaleka ndipo ngati timayesetsa kuchita motero ngakhale tsiku ndi tsiku, Yehova adzatithandiza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena