Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/94 tsamba 1
  • Kunyumba ndi Nyumba Mosalekeza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kunyumba ndi Nyumba Mosalekeza
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa Chiyani Utumiki wa ku Nyumba ndi Nyumba Uli Wofunika Kwambiri Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kulalikira ku Nyumba ndi Nyumba
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Phunzitsani Poyera ndi Kunyumba ndi Nyumba
    Nsanja ya Olonda—1991
  • “Mbiri Yabwino Iyenera Kulalikidwa Choyamba”
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
km 7/94 tsamba 1

Kunyumba ndi Nyumba Mosalekeza

1 Mu Israyeli wakale, nsembe zinkaperekedwa tsiku ndi tsiku. (Eks. 29:38-42) Moto wa paguwa la nsembe unkayakabe; utsi wokwera kumwamba unali “fungo lokoma” limene linakondweretsa Yehova. (Eks. 29:18) Lerolino, timafulumizidwa ‘kupereka chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.’ (Aheb. 13:15) Mmalo mwa kugwiritsira ntchito nsembe zofotokozedwa ndi Chilamulo, timalambira Yehova mwa kuonetsa matamando ake mosalekeza.—Yes. 43:21; Mac. 5:42.

2 Yesu Kristu, Mboni yaikulu koposa imene inayenda padziko lapansi, anatiphunzitsa mmene tingachitire kulambira koyera mwa kupereka nsembe zachitamando. Anaphunzitsa ophunzira ake kuti uthenga umene ankalalikira unali wofulumira. Iye anadziŵa kuti njira yogwira mtima koposa yofikira anthu ndi mbiri yabwino inali kulankhula nawo mwachindunji m’nyumba zawo. (Mat. 10:7, 12) Chotero timaona kuti atumwi anatsatira chilangizo chake chouziridwa mwaumulungu cha kulalikira kunyumba ndi nyumba.—Mac. 20:20.

3 Sizosiyana lerolino. Monga ophunzira a Yesu, Akristu oona amatsatira chitsanzo chake mwa kulalikira mbiri yabwino kunyumba ndi nyumba. Ngakhale kuti tingasulizidwe ndi kuzunzidwa pachifukwa chimenecho, mamiliyoni aphunzira choonadi ndipo zikwi mazanamazana za ophunzira atsopano zikuloŵa pamzera wa khamu lalikulu chaka chilichonse, zikumapereka umboni wakuti iyi ndiyo njira ya Yehova yokwaniritsira chifuniro chake. Nchifukwa chake timachita khama muutumiki wathu.

4 Mapindu a Kulalikira Kunyumba ndi Nyumba: “Mulungu alibe tsankhu . . . Wakumuwopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Mac. 10:34, 35) Kupita mwachindunji kunyumba iliyonse m’gawo lathu kumasonyeza bwino lomwe kupanda tsankhu, kukumapatsa aliyense mpata wa kumva uthenga wa Ufumu mokhazikika. Ndiyeno okhala ndi khutu lomvetsera amalandira chithandizo cha iwo okha molingana ndi zosoŵa zawo.

5 Pafupifupi ofalitsa onse, kuphatikizapo achichepere, achikulire, ndipo ngakhale awo amene ali atsopano, angatengemo mbali m’ntchito yakunyumba ndi nyumba. Mwanjira imeneyi aliyense angapange “chilengezo chapoyera cha chipulumutso.” (Aroma 10:10, NW) Kutengamo mbali ndi ena muutumiki wakunyumba ndi nyumba kumatigwirizanitsa m’zomangira za chikondi ndi umodzi. Panthaŵi imodzimodziyo, timapatsidwa mpata wakusonyeza chipiriro chathu pamene tikumana ndi mphwayi kapena chitsutso. Kusonyeza poyera chikhulupiriro kumeneku kumatipangitsa kukhala “choonetsedwa,” chimene chimathandiza oona mtima kuzindikira kuti tili ndi makonzedwe olinganizika ophunzitsira Baibulo ndi kuti angapindule nawo. (1 Akor. 4:9) Zonse zikusonyeza bwino lomwe kuti Yehova akudalitsa ntchito yakunyumba ndi nyumba ndi kuigwiritsira ntchito kusonkhanitsira khamu lalikulu ku “nyumba” ya kulambira koyera.—Yes. 2:2-4.

6 Tsopano lino kuposa nthaŵi ina iliyonse m’mbiri, anthu afunikira kumva uthenga wa Ufumu. Tiyeni tipitirizebe kulalikira kunyumba ndi nyumba mosalekeza kufikira pamene Yehova adzati zakwanira. (Yes. 6:11) Mwa kutero, tidzafupidwa ndi chimwemwe chimene chimadza chifukwa cha kukhala ndi phande muutumiki wofunika ndi wopindulitsa wakunyumba ndi nyumba m’nthaŵi ino ya mapeto.—1 Akor. 15:58.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena