Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/06 tsamba 4
  • Kulalikira ku Nyumba ndi Nyumba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulalikira ku Nyumba ndi Nyumba
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Nkhani Yofanana
  • Phunzitsani Poyera ndi Kunyumba ndi Nyumba
    Nsanja ya Olonda—1991
  • N’chifukwa Chiyani Utumiki wa ku Nyumba ndi Nyumba Uli Wofunika Kwambiri Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kusonyeza Chiyamikiro Kaamba ka Zisonyezero Ziŵiri Zazikulu Kwambiri za Chikondi
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kunyumba ndi Nyumba Mosalekeza
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 9/06 tsamba 4

Kulalikira ku Nyumba ndi Nyumba

1. Kodi ndi funso lotani lomwe limabwera tikaganizira za kulalikira ku nyumba ndi nyumba, ndipo limabwera chifukwa chiyani?

1 “Anthu amene akudziwa bwino njira zosiyanasiyana zofalitsira Choonadi angavomereze kuti kulalikira ku nyumba ndi nyumba pogwiritsa ntchito buku la MILLENNIAL DAWN n’kumene kuli njira yabwino kwambiri yolalikira Choonadi panopa kuposa njira ina iliyonse.” Mawu amenewo, omwe analembedwa mu Zion’s Watch Tower ya July 1, 1893, anasonyeza kufunika kwa utumiki wa ku nyumba ndi nyumba. Anthu padziko lonse lapansi amaona kuti ntchito imeneyi ndiyo chizindikiro cha Mboni za Yehova. Popeza tsopano m’mayiko ena zikukhala zovuta kwambiri kupeza anthu panyumba, kodi njira imeneyi ndi yothandizabe?

2. Kodi pali maziko otani a m’Malemba olalikirira ku nyumba ndi nyumba?

2 N’kogwirizana ndi Malemba Ndiponso N’kofunika: Kulalikira ku nyumba ndi nyumba kuli ndi maziko a m’Malemba. Yesu anauza ophunzira ake 70 kuti apite awiriawiri ku nyumba za anthu. (Luka 10:5-7) Ponena za ophunzira ake Yesu atangofa kumene, Baibulo limati: “Masiku onse, m’Kachisi ndi m’nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira.” (Mac. 5:42) Mtumwi Paulo nayenso ankaphunzitsa mwachangu ku nyumba ndi nyumba.—Mac. 20:20.

3. Kodi ubwino wolalikira ku nyumba ndi nyumba ndi wotani?

3 Kulalikira ku nyumba ndi nyumba kukadali njira yofunika yofalitsira uthenga wabwino masiku ano. Kumatithandiza ‘kufufuza’ mwadongosolo anthu oyenerera. (Mat. 10:11, NW) Anthu nthawi zambiri amakhala omasuka akakhala panyumba. Kulankhula nawo pamaso m’pamaso, kumva mawu awo, kuona nkhope zawo, ndi kuona mmene malo awo akuonekera, kumatithandiza kuzindikira zokonda zawo ndi nkhawa zawo. Nthawi zambiri kumatipatsa mpata wabwino kwambiri wolankhula nawo nthawi yaitali.

4. Kodi tingatani kuti ulaliki wa ku nyumba ndi nyumba ukhale wopindulitsa?

4 Sinthani Ndandanda Yanu: Mtumwi Paulo anali wokonzeka kusintha ulaliki wake “chifukwa cha Uthenga Wabwino.” (1 Akor. 9:23) Mwina tikhoza kusintha ndandanda yathu kuti tizilalikira nthawi imene anthu ambiri amakhala pakhomo, monga masana, Loweruka ndi Lamlungu, kapena masiku a tchuthi. Muzilemba nyumba zomwe simunapezepo anthu, ndipo muzipitakonso tsiku lina kapena nthawi ina.

5. Kodi anthu amene ali ndi thanzi lofooka tingawathandize bwanji kuti achite nafe limodzi ulaliki wa ku nyumba ndi nyumba?

5 Ngakhale anthu amene ali ndi thanzi lofooka akhoza kulalikira nawo ku nyumba ndi nyumba. Mwina tikhoza kupita nawo limodzi anthu amenewa ku nyumba zoti atha kukwanitsa kufikako, n’kuwalola kuti azilalikira m’njira imene angakwanitse. Mlongo wina anali ndi vuto lopuma mwaphuma, zimene zinachititsa kuti pa mphindi 30 zilizonse, azilalikira pa nyumba imodzi yokha. Komabe, iye anali wosangalala kwambiri kulalikira limodzi ndi gulu la ofalitsa ena.

6. N’chifukwa chiyani kulalikira ku nyumba ndi nyumba kuyenera kukhala mbali ya utumiki wathu yomwe timachita nthawi zonse?

6 M’ntchito yathu ya ku nyumba ndi nyumba, tikupitirizabe kupeza anthu ambiri onga nkhosa. Wofalitsa wina atagogoda pakhomo anauzidwa kuti: “Lowani, ndakudziwani. Ndinali kupemphera kwa Mulungu kuti anditumizire munthu adzandithandize, kenaka m’pamene ndimamva kugogoda pakhomo. Mulungu wamva pemphero langa n’kukutumizani.” Zotsatirapo za ntchito imeneyi zikusonyeza kuti Yehova akudalitsa njira imeneyi yolalikirira. (Mat. 11:19) Yesetsani kuti kulalikira ku nyumba ndi nyumba kukhale mbali ya utumiki wanu yomwe mumachita nthawi zonse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena