Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/06 tsamba 4
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 9/06 tsamba 4

Zomwe Munganene Pogawira Magazini

Nsanja ya Olonda Sept.15

Tchulani nkhani yomwe yangochitika kumene yomwe anthu akuda nayo nkhawa m’dera lanu. Kenaka funsani kuti: “Kodi mukuganiza kuti vesi la m’Baibulo ili likufotokoza molondola zomwe zikuchitika masiku athu ano? [Werengani 2 Timoteo 3:1, ndipo yembekezani ayankhe.] Nkhani iyi ikufotokoza umboni woti tikukhala m’masiku otsiriza ndipo ikusonyeza zomwe tiyenera kuchita.”

Galamukani! Sept.

“Anthu ambiri amaona kuti tinachita kulengedwa. Ena amaganiza kuti tinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Inu mumaganiza bwanji pa nkhani imeneyi? [Yembekezani ayankhe.] Taonani malangizo awa otithandiza kuzindikira zoona zake za nkhani imeneyi. [Werengani Yobu 12:7, 8.] Magazini yapadera iyi ya Galamukani! ikufotokoza zomwe tingaphunzire poona nzeru ndi kupangidwa mwaluso kwa zinthu zamoyo.”

Nsanja ya Olonda Oct. 1

“Akatswiri a sayansi ya zamoyo akuyesetsa kuthetsa matenda ndi kutalikitsa moyo wathu. Kodi mukuganiza kuti zidzatheka kukhala ndi moyo wosatha m’tsogolo muno? [Yembekezani ayankhe.] Taonani chifukwa chomwe timafunira kukhala ndi moyo wotalikirapo. [Werengani Mlaliki 3:11.] Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chake Mulungu anatipatsa mtima wofuna kukhala ndi moyo wosatha.”

Galamukani! Oct.

“Pafupifupi aliyense amakonda kuonera TV. Koma kodi mukuganiza kuti tizionera zinthu zilizonse zimene akuonetsa? [Yembekezani ayankhe. Kenaka werengani Miyambo 13:20.] Magazini iyi ikufotokoza momwe TV imakhudzira moyo wathu, ndipo ikupereka malangizo otithandiza kuonera TV mosamala.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena