Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/02 tsamba 8
  • Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
Onani Zambiri
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 9/02 tsamba 8

Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini

Nsanja ya Olonda Sept.15

“Anthu ambiri zedi amakhulupirira kuti anthu ‘oyera mtima’ ali ndi mphamvu yapadera ndiponso kuti n’kwabwino kupemphera kudzera mwa iwo. Kodi inu mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Yesu Kristu ananena. [Ŵerengani Yohane 14:6.] Zimenezi zimapangitsa ena kusadzera mwa anthu ‘oyera mtima’ popemphera. Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza nkhani yofunika imeneyi.”

Galamukani! Sept. 8

“Kodi munayamba mwadandaulapo kuti vuto loipitsa malo tsopano lafika poipa? [Yembekezani ayankhe.] Chimene chimachititsa kwenikweni vutoli ndi kutaya zinthu. Yesu anaphunzitsa otsatira ake kusataya zinthu. [Ŵerengani Yohane 6:12.] Magazini iyi ikusonyeza momwe kutsatira mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo kungathandizire mabanja kupeŵa khalidwe lokonda kutaya zinthu.”

Nsanja ya Olonda Oct. 1

“Anthu ambiri amadabwa ngati mavuto onse amene timaona monga nkhondo, upandu ndi uchigaŵenga zidzathe. Kodi inu mumaona bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limatitsimikizira izi. [Ŵerengani Salmo 37:10, 11.] Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chake Mulungu sanathetsebe kuipa ndi kuvutika kumene kumachitika chifukwa cha zimenezi.”

Galamukani! Sept. 8

“Anthu ambiri masiku ano sadziŵa momwe zinthu ziyendere m’moyo wawo. [Ŵerengani Mlaliki 9:11.] Kodi malangizo odalirika angapezeke kuti? [Yembekezani ayankhe.] Anthu ena amakhulupirira kuti manambala ali ndi matanthauzo enaake obisika. Kodi manambala angakuthandizeni kudziŵa zimene zidzakuchitikireni? Kodi mungapeze kuti mfundo zodalirika zofotokoza za m’tsogolo? Galamukani! iyi ikuyankha zimenezi.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena