Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Sept. 15
“Kodi mukuganiza bwanji pa zimene lemba ili likunena? [Werengani Deuteronomo 32:4.] Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti ngati Mulungu ndi wamphamvu yonse ndiponso wolungama, n’chifukwa chiyani m’dzikoli muli zoipa ndipo anthu akuvutika kwambiri? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chimene Mulungu walolera zoipa kupitirira mpaka lero.”
Galamukani! Sept.
“Ambirife timafuna kukhala ndi thanzi labwino ndi moyo wautali. Kodi mukuganiza kuti kukhala wosangalala kungatithandize kukhala ndi thanzi labwino? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Miyambo 17:22.] Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chake kukhala wosangalala kumathandiza.” Sonyezani nkhani imene ili pa tsamba 26.
Nsanja ya Olonda Oct. 1
“Kodi munayamba mwanong’onezapo bondo? [Yembekezani ayankhe.] Onani zimene lemba ili likunena za chifukwa chake tonsefe timachita zinthu zimene pambuyo pake timadzazindikira kuti tinalakwitsa. [Werengani Yeremiya 10:23.] Magazini iyi ikufotokoza mmene malangizo a m’Baibulo angatithandizire kuti tizichita zinthu mwanzeru.”
Galamukani! Oct.
“Kodi mukuganiza kuti masiku ano ana ali pa ngozi kuposa kale? [Yembekezani ayankhe.] Anthu ambiri akuganiza kuti tikukhala mu nthawi imene ikufotokozedwa mu lemba ili. [Werengani 2 Timoteyo 3:1-5.] Magazini iyi ikupereka malangizo abwino a mmene makolo angatetezere ana awo kwa anthu ogona ana.”