Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Sept. 1
“Kodi mukuganiza kuti tingapeze kuti malangizo odalirika pakakhala nkhani yaikulu yofunika kuti tisankhe chochita? [Yembekezani ayankhe. Werengani Miyambo 3:5, 6.] Nkhani iyi ikutsindika kuti ndi nzeru kuyamba taganizira kaye zotsatira zake tisanasankhe zochita.” Asonyezeni nkhani imene ili patsamba 8.
Galamukani Sept.
“Kodi mukuganiza kuti chinali cholinga cha Mulungu kuti anthu azivutika ndi njala imene ili padziko lonse lapansi? [Yembekezani ayankhe.] Taonani mmene iye adzathetsere vutoli. [Werengani Salmo 72:16.] Nkhani iyi ikufotokoza mmene Mulungu adzabweretsere Paradaiso padziko lapansi.” Asonyezeni nkhani imene ili patsamba 7.
Nsanja ya Olonda Oct. 1
“M’nthawi zovuta zino, anthu ambiri akuda nkhawa akaganiza za m’tsogolo. Kodi chimene chimakuthandizani inuyo kukhala wolimba mtima n’chiyani? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo limalonjeza. [Werengani Yesaya 65:17.] Magazini iyi ikupereka zifukwa zomveka zokhalira ndi chiyembekezo.”
Galamukani Oct.
“Intaneti ndi yothandiza kwambiri, koma ili ndi mavuto akenso kwa ana. Kodi mukuganiza kuti tingawateteze bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Taonani mfundo iyi. [Werengani ndi kufotokoza Miyambo 18:1.] Mfundo imeneyi ndi ina mwa mfundo 6 za m’Baibulo zimene zili m’nkhani iyi, zothandiza makolo kuteteza ana awo.” Asonyezeni nkhani imene ili patsamba 8.