Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Aug.15
“Tingakonde kumva maganizo anu pa nkhani inayake imene Yesu ananena. [Werengani Mateyu 5:5.] Kodi mukuganiza kuti lonjezo limeneli likadzakwaniritsidwa, zinthu padziko pano zidzakhalabe ngati mmene zililimu? [Yembekezani ayankhe.] Pogwiritsa ntchito Baibulo, magazini iyi ikufotokoza mmene Yesu adzasinthire dziko lapansili. Ikufotokozanso kuti ndi ndani amene adzalandire dziko lapansi.”
Galamukani! Aug.
“Kodi mukuganiza kuti n’zotheka kudzaonananso ndi okondedwa athu amene anafa? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Yesu analonjeza zokhudza anthu akufa. [Werengani Yohane 5:28, 29.] Nkhani iyi ikufotokoza kuchokera m’Baibulo zimene zimachitika tikafa.” Sonyezani nkhani yomwe yayambira patsamba 28.
Nsanja ya Olonda Sept. 1
“Anthu ambiri masiku ano alibenso chidwi ndi chipembedzo. Kodi mukuganiza kuti kupembedza kungamuthandize munthu kukhala wabwino? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo linaneneratu zokhudza zinthu zimene anthu ena adzafune m’chipembedzo masiku otsiriza. [Werengani 2 Timoteo 4:3, 4.] Magazini iyi ikufotokoza mmene chipembedzo choona chimalemekezera Mulungu ndi ubwino wake kwa ife.”
Galamukani! Sept.
“Anthu ambiri amakayikira ngati kukhulupirira kuti kuli Mulungu kuli kogwirizana ndi sayansi. Inu mumaganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Ahebri 3:4.] Magazini yapadera iyi ya Galamukani! ikufotokoza zimene zachititsa kuti asayansi ena ayambe kukhulupirira kuti kunja kuno kuli Mlengi.”