Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda July 15
“Timamva chisoni kwambiri munthu yemwe timamukonda akamwalira. Kodi mukuganiza kuti chinachake chimatuluka mwa iye n’kukhalabe ndi moyo? [Yembekezani ayankhe.] Yesu analonjeza zinthu zolimbikitsa izi. [Werengani Yohane 5:28, 29.] Popeza Yesu ananena kuti nthawi ‘idzafika’ imene akufa adzaukitsidwa, magazini iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena za komwe akufa ali panopo.”
Galamukani! July
“Anthu ambiri amayesetsa kuchita zabwino ndipo amaona kuti n’kofunika kukhala munthu wabwino. Kodi inunso mumatero? [Yembekezani ayankhe.] Taonani ngozi yomwe imakhalapo ngati zimene timaona kuti n’zabwino n’zosiyana ndi zimene Mulungu amaona kuti n’zabwino. [Werengani Miyambo 14:12.] Nkhani iyi ikufotokoza kuti ndi munthu wotani yemwe Mulungu amamuona kukhala wabwino.” Sonyezani nkhani yomwe ikuyambira pa tsamba 20.
Nsanja ya Olonda Aug. 1
“Ndingakonde kumva maganizo anu pa mawu awa omwe Yesu ananena. [Werengani Mateyo 5:3.] Kodi mukuona kuti moyo wauzimu ndi wofunika kuti munthu akhale wosangalala? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena za moyo wauzimu weniweni ndiponso mmene munthu angakhalire wauzimu.”
Galamukani! Aug.
“Kodi mukuganiza n’kuti kumene makolo angapezeko malangizo amene angawathandizedi? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo likutilonjeza. [Werengani 2 Timoteyo 3:16.] Magazini iyi ikufotokoza mmene Baibulo lingathandizire makolo kulera ana awo kuti akhale achimwemwe.”