Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda July 15
“Kodi mukuganiza kuti lidzapezekapo boma loti n’kuthetsa mavuto onse a anthu. [Yembekezani ayankhe.] Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kupempherera boma loterolo m’mawu ake amene timawerenga pa Mateyu 6:9, 10. [Werengani.] Magazini iyi ikufotokoza mmene Ufumu wa Mulungu umaposera maboma a anthu ndipo ikufotokozanso madalitso amene udzabweretse.”
Galamukani! July
Mukakumana ndi wachinyamata, munganene kuti: “Ambiri amsinkhu wanuwu akuganizira zokwatira. Kodi n’kuti kumene mukuganiza kuti kungapezeke malangizo odalirika pa nkhani ya ukwati? [Yembekezani ayankhe.] Tiyeni tione kuti ndani amene anayambitsa ukwati. [Werengani Mateyu 19:6.] Magazini iyi ili ndi mfundo za m’Baibulo zoti n’kutithandiza kukhala ndi banja lachimwemwe.”
Nsanja ya Olonda Aug. 1
“Masiku ano n’zofala kuona anthu akuchitira anzawo nkhanza. Kodi mukuganiza kuti zinthu zikadasintha ngati anthu ambiri akanamamvera mawu a Yesu awa? [Werengani Mateyu 7:12. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza kuchokera m’Baibulo mmene anthu adzayambire kulemekeza ufulu wa anthu ena.”
Galamukani! Aug.
“Tonsefe timafuna kuti munthu akadwala alandire chithandizo chabwino. Kodi mukudziwa kuti madokotala ambiri masiku ano amachita mantha kuika anthu odwala magazi. [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chake. Ikufotokozanso kuchokera m’Baibulo chifukwa chomwe Mulungu amaonera magazi kukhala amtengo wapatali kwambiri.” Werengani Levitiko 17:11.