Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda July 15
“Kwa zaka masauzande ambiri, anthu akhala ndi zikhulupiriro zosiyanasiyana. Kodi mukuganiza kuti n’zotheka kudziwa zikhulupiriro zimene zili zoona ndiponso zimene zili zabodza? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikutchula kumene mungapeze ziphunzitso zoona zimene Mulungu amakondwera nazo.” Werengani 2 Timoteo 3:16.
Galamukani! Aug. 8
“Zimapweteka mtima kwambiri kuona anthu akuvutika chifukwa cha masoka achilengedwe. [Tchulani chitsanzo chimene chikudziwika bwino kwanuko.] Kodi mukuganiza kuti masoka ngati amenewa akuwonjezereka? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikuyankha funso limeneli. Ilinso ndi mawu otonthoza kwa awo amene okondedwa awo anafa ndi masoka ngati amenewa.” Werengani Yohane 5:28, 29.
Nsanja ya Olonda Aug. 1
“Anthu ambiri masiku ano akuvutika maganizo podziona ngati anthu opanda pake. Kodi mukuganiza kuti pangafunike kuchitanji kuti tiwathandize? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza mmene Baibulo lingathandizire anthu oterowo kupeza chimwemwe chenicheni.” M’sonyezeni malemba akuda kwambiri olembedwa mopendekeka m’nkhani yakuti “Baibulo Lingakuthandizeni Kukhala Osangalala.”
Galamukani! Aug. 8
“Anthu ambiri akukhala mwamantha. Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani anthu akukhala mwamantha chonchi? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ili ndi mfundo zothandiza kwambiri za mmene tingadzitetezere ku zinthu zofala zimene zimachititsa anthu kukhala mwamantha. Ikufotokozanso zimene Baibulo limalonjeza zoti dziko lidzakhala lopanda zoopsa.” Werengani Yesaya 11:9.