Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda July 15
“Anthu ambiri aona kuti anthu ochuluka ali ndi khalidwe losafuna kucheza ndi anzawo. Kodi mukuganiza kuti limeneli ndi khalidwe labwino? [Yembekezani ayankhe.] Taonani mawu anzeru awa onena za kufunika kocheza ndi ena. [Ŵerengani Mlaliki 4:9, 10.] Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chimene tonsefe timafunira anzathu ndiponso mmene tingathetsere vuto losafuna kucheza ndi ena.”
Galamukani! July 8
“Anthu ambiri akusoŵa mtendere ndi kuchuluka kwa chiwawa chomwe ena amachita popanda cholinga chenicheni. [Tchulani chitsanzo chodziŵika kumeneko, ndipo yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikulongosola zinthu zina zimene zikuchititsa kuti pakhale chiwawa chankhanza chotere. Ikulongosolanso momwe Mulungu adzathetsere upandu ndi chiwawa moti sizidzakhalakonso.” Ŵerengani Salmo 37:10, 11.
Nsanja ya Olonda Aug. 1
“Kodi mukudziŵa kuti lipoti lina linati anthu oposa theka padziko lonse lapansi amagwiritsa ntchito ndalama zosakwana madola aŵiri patsiku? Kodi mukuganiza kuti pali china chilichonse chimene chingachitike kuti zimenezi zithe? [Yembekezani ayankhe.] Magazini ya Nsanja ya Olonda iyi ikutchula njira yopezeka m’Baibulo yothetseratu umphaŵi.”—Ŵerengani Salmo 72:12, 13, 16.
Galamukani! July 8
“Anthu ambiri akudera nkhaŵa chilengedwe. Kodi mukuganiza kuti zidzatheka kuteteza nkhalango za m’madera amene kumagwa mvula yambiri? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza zimene anthu akuchita masiku ano pofuna kuteteza nkhalango za m’madera amene kumagwa mvula yambiri. Ikufotokozanso momwe lonjezo labwino la Mulungu ili lidzakwaniritsidwire.” Ŵerengani Yesaya 11:9.