Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda July 15
“Ngati zochitika monga izi [zimene azisonyeza pa chikuto akanazilengeza pankhani lerolino, mwinamwake anthu ambiri sakanakhulupirira. Inu mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Marko 4:39.] Kodi ndi umboni wotani umene umasonyeza kuti zozizwitsa zimene Yesu anazichita zinalidi zenizeni? Magazini iyi ya Nsanja ya Olonda ikuyankha funso limeneli.”
Galamukani! Aug. 8
“M’dzikoli, anthu ochita za chinyengo akuyesetsa kupeza njira zatsopano zobera anthu amene sakudziŵa chilichonse. Kodi zimenezi zikukukhudzani? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ya Galamukani! ikufotokoza zina mwa njira zofunika zimene zikhoza kutinthandiza kuti tidziteteze kwa anthu onyenga.” Ŵerengani Miyambo 22:3.
Nsanja ya Olonda Aug. 1
“Chifukwa cha kugaŵikana kwa anthu, ena amaganiza kuti njira yokha imene dziko lapansi lingakhalire pamtendere ndiyo kukhala ndi boma limodzi lolamulira padziko lonse lapansi. Kodi mukuganiza kuti zimenezi n’zotheka? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Danieli 2:44.] Magazini iyi ikunena zimene panopa Ufumu wa Mulungu ukuchita ndi mmene posachedwapa udzabweretsera dziko lamtendere.”
Galamukani! Aug. 8
“Tonsefe timamva chisoni tikamamva za mmene ana akuzunzidwira. Mwinamwake munadzifunsapo kuti, ‘Kodi Mulungu amawaganiziradi ana?’ [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Salmo 72:12-14.] Nkhani iyi ikufotokoza mmene Mulungu amaonera ana ndi mmene adzabweretsera mpumulo wachikhalire posachedwapa kwa onse amene akuzunzidwa.”