Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Aug. 15
“Ndikufuna kumva maganizo anu pa zimene lembali limanena. [Werengani Aheberi 3:4.] Kodi mukuvomereza kuti chilengedwe chonse chili ndi Mlengi wake? [Yembekezani ayankhe.] Magaziniyi ikufotokoza mmene mfundo yoti Mlengi aliko ilili yogwirizana ndi sayansi.”
Galamukani! Aug.
Mukakumana ndi wachinyamata munganene kuti: “Anthu ambiri a msinkhu wako akhumudwa kwambiri chifukwa cha miseche imene anthu ena anafalitsa. Kodi iwe zinakuchitikirapo? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo lili ndi malangizo amene angatithandize pamene anthu ena akufalitsa miseche yonena za ife. Limasonyezanso mmene ifeyo tingapewere kufalitsa miseche.” Musonyezeni nkhani yomwe ikuyambira pa tsamba 12, ndipo werengani lemba limodzi la m’nkhaniyi.
Nsanja ya Olonda Sept. 1
“Ambiri amaganiza kuti ‘Chipangano Chakale’ chimafotokoza mbiri yakale yothandiza. Koma amakayikira ngati malangizo ake ali othandiza masiku ano. Nanga inu mukuona bwanji? [Yembekezani ayankhe, kenako werengani Aroma 15:4.] Magazini iyi ikusonyeza kuti ‘Chipangano Chakale’ chili ndi malangizo othandiza pa moyo ndiponso chiyembekezo chenicheni cha zinthu zabwino m’tsogolo.”
Galamukani! Sept.
“Kodi mukuganiza kuti Mulungu ndiye amachititsa masoka achilengedwe? [Yembekezani ayankhe kenako werengani Deuteronomo 32:4.] Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chake Mulungu walola kuti masoka achilengedwe azichitika ndiponso mmene mungatetezere banja lanu.”