Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Aug. 15
“Anthu ambiri amafuna kukhala ndi mbiri yabwino. Ena amadera nkhaŵa kuti anthu adzakumbukira chiyani za iwowo akadzafa. Kodi inu munaganizapo zimenezi? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Mlaliki 7:1.] Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza mmene tingakhalire ndi mbiri yabwino kwa anthu ndiponso kwa Mulungu.”
Galamukani! Aug. 8
“Anthu ambiri akuda nkhaŵa ndi kuchuluka kwa zithunzi zolaula. Kodi mukuganiza kuti zimenezi ndi zodetsa nkhaŵa? [Yembekezani ayankhe.] Malangizo othandiza a m’Baibulo akhoza kutiteteza. [Ŵerengani Aefeso 5:3, 4.] Magazini iyi ikusonyeza mmene tingadzitetezere ku vuto loopsa limeneli.”
Nsanja ya Olonda Sept. 1
“Anthu ambiri amaganiza kuti zipembedzo zosiyanasiyana zangokhala njira zosiyanasiyana zopita ku malo amodzi. Ena amakhulupirira kuti pali chipembedzo choona chimodzi chokha. Kodi inu munaganizirapo nkhani imeneyi? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza fanizo lakale limene limamveketsa bwino nkhani imeneyi.” Ŵerengani Mateyu 13:24-30.
Galamukani! Aug. 8
“M’zaka zaposachedwapa, kwachitika masoka oopsa kwambiri chifukwa cha kusintha kwa nyengo padziko lonse lapansi. Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chimene chingathetse mavuto amene masoka ameneŵa amabweretsa? [Yembekezani ayankhe.] Maganizi iyi ikufotokoza vuto la kusintha kwa nyengo komanso njira yopezeka m’Baibulo yothetsera vutoli.”—Ŵerengani Yesaya 35:1.