Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Aug. 15
“Masiku ano, anthu amafufuza malangizo okhudza ukwati ndi kaleredwe ka ana kumalo osiyanasiyana. Kodi mukuganiza kuti malangizo abwino tingawapeze kuti? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ya Nsanja ya Olonda ikufotokoza ena mwa malangizo anzeru operekedwa ndi Mlengi wathu okhudza moyo wa banja.” Ŵerengani Salmo 32:8.
Galamukani! Sept. 8
“Kodi mukuganiza kuti atate afunika azithandiza kulera ana awo? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ya Galamukani! ikufotokoza vuto lalikulu la atate amene ngakhale amakhala panyumba, sacheza ndi ana awo. Ikufotokozanso mmene atate angathandizire ana awo.” Ŵerengani Miyambo 13:1.
Nsanja ya Olonda Sept. 1
“Aliyense amafuna kukhala wachimwemwe. Kodi mukuganiza kuti zinthu zimene azitchula apazi zingabweretsedi chimwemwe? [Ŵerengani Mateyu 5:4a, 6a, 10a. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza tanthauzo la mawu ameneŵa onenedwa pa Ulaliki wa pa Phiri wodziŵika bwino ndipo ikufotokoza zina zimene tingachite kuti tikhale achimwemwe.”
Galamukani! Sept. 8
“Zikuoneka kuti munthu mmodzi mwa anthu anayi adzadwala matenda a maganizo nthaŵi inayake. Mwina mukudziŵapo winawake amene akuvutika ndi matendaŵa. [Tsegulani pamene pali nkhaniyo.] Nkhani iyi ili ndi mfundo zothandiza. Ikunena zimene tingachite ngati winawake amene timam’konda ali ndi vuto limeneli.”