Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Sept. 15
“Anthu ambiri amatchula mawu odziŵika bwino awa m’mapemphero awo. [Ŵerengani Mat. 6:10.] Kodi mukuganiza kuti moyo ukanakhala wotani ngati kufuna kwa Mulungu kukanachitika mokwanira bwino pano padziko lapansi? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza kwambiri za tanthauzo la mbali iliyonse ya Pemphero la Ambuye, kuphatikizapo mbali imene tangoŵerenga kumeneyi.”
Galamukani! Oct. 8
“Anthu ambiri ndi okhudzidwa ndi vuto limene likukula pakati pa achinyamata la kumwa mwauchidakwa. Kodi inunso vutoli mwaliona? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Miyambo 20:1.] Kumwa mwauchidakwa kumaika achinyamata pangozi zosiyanasiyana. Nkhani iyi ili ndi mfundo zimene zingawathandize mmene angapeŵere kumwa moŵa mwauchidakwa.”
Nsanja ya Olonda Oct. 1
“Aliyense wa ife amafuna ataona umbanda, chiwawa, ndi nkhondo zitatha. Kodi mukuganiza kuti mawu awa adzakwaniritsidwa? [Ŵerengani Salmo 37:11. Ndiyeno yembekezani kuti ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza kugwirizana kwa lonjezo limeneli ndi mmene Mulungu anafunira pachiyambi kuti anthu akhalire ndi mmene ife tingapezere zimenezi.”
Galamukani! Oct. 8
“Kodi si zomvetsa chisoni kuti chaka chilichonse atsikana ang’onoang’ono ambirimbiri amatenga mimba? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza njira zimene angatsatire pothana ndi mavuto ambiri amene angakumane nawo monga mayi wachichepere. Ikunenanso za mmene makolo angathandizire ana awo kupeŵa vutoli asanakumane nalo.” Ŵerengani 2 Timoteo 3:15.