Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 1/15 tsamba 10-15
  • Phunzitsani Poyera ndi Kunyumba ndi Nyumba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Phunzitsani Poyera ndi Kunyumba ndi Nyumba
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Njira ya Atumwi
  • Palibe Chouloŵa Mmalo
  • Akulu Afunikira Kutsogolera
  • Aliyense Ayenera Kukhala Mboni
  • Kulalikira ku Nyumba ndi Nyumba
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • N’chifukwa Chiyani Utumiki wa ku Nyumba ndi Nyumba Uli Wofunika Kwambiri Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kunyumba ndi Nyumba Mosalekeza
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • “Mbiri Yabwino Iyenera Kulalikidwa Choyamba”
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 1/15 tsamba 10-15

Phunzitsani Poyera ndi Kunyumba ndi Nyumba

“Sindinazengereze . . . kukuphunzitsani poyera ndi kunyumba ndi nyumba.”​—MACHITIDWE 20:20, “Byington.”

1. Kodi ndimotani mmene wansembe Wachikatolika anathirira ndemanga pa kubala zipatso kwauminisitala wa kunyumba ndi nyumba wa Mboni za Yehova?

“AKATOLIKA Amaupereka Uthenga Wabwino Kukhomo ndi Khomo.” Unalembedwa tero mutu wankhani mu The Providence Sunday Journal ya pa October 4, 1987. Nyuzipepalayi inasimba kuti cholinga chachikulu cha ntchitoyi chinali cha “kuitana agulupa awo ena osakangalika kuti abwerere kuumoyo wokangalika wa ntchito yaugulupa.” Wansembe John Allard, mtsogoleri wa Ofesi ya Ulaliki mu Diocese of Providence, anagwidwa mawu kukhala akunena kuti: “Ndithudi, adzatisuliza kwambiri. Anthu adzati, ‘Awoneni ukamwendomnjira, mongadi Mboni za Yehova.’ Komatu Mboni za Yehova zimabala zipatso, kodi sitero? Ndingakhokherane nanu kuti mukaloŵe m’Nyumba Yaufumu iriyonse mumzindawu [wa Rhode Island, U.S.A.,] ndipo mudzapeza kuti mipingo njodzala ndi anthu omwe kale adali Akatolika.”

2. Kodi ndifunso liti limene ladzutsidwa moyenerera?

2 Inde, Mboni za Yehova nzotchuka ndi uminisitala wawo wobala zipatso wa kunyumba ndi nyumba. Koma kodi iwo amapitiranji kunyumba ndi nyumba?

Njira ya Atumwi

3. (a) Kodi Yesu Kristu anawapatsa ntchito yotani ophunzira ake? (b) Kodi ndim’njira yaikulu iti imene atsatiri oyambirira a Kristu anachitira ntchito yawo?

3 Yesu Kristu anawapatsa atsatiri ake lamulo lodzala ndi tanthauzo ili: ‘Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la mwana, ndi la mzimu woyera: ndikuŵaphunzitsa asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimariziro cha nthaŵi ya pansi pano.’ (Mateyu 28:19, 20) Njira yaikulu yomwe ntchitoyi ikachitidwiramo inatsimikiziridwa mofulumira pambuyo pa tsiku la Pentekoste wa 33 C.E. ‘Masiku onse, m’kachisi ndi [kunyumba ndi nyumba, NW] sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.’ (Machitidwe 5:42) Zaka 20 pambuyo pake, mtumwi Paulo anadziloŵetsa muuminisitala wakunyumba ndi nyumba, popeza kuti anawakumbutsa akulu Achikristu ali mumzinda wa ku Efeso kuti: ‘Sindinakubisirani zinthu zopindulitsa, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m’nyumba m’nyumba.’​—Machitidwe 20:20.

4. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti Machitidwe 5:42 ndi Machitidwe 20:20 akutanthauza kuti kulalikira kwa atsatiri a Yesu kunagaŵiridwa kunyumba ndi nyumba?

4 Pa Machitidwe 5:42 mawu akuti “kunyumba ndi nyumba” atembenuzidwa kuchokera ku liwu lakuti kat’ oiʹkon. Panopa ka·taʹ lagwiritsiridwa ntchito mlingaliro “logaŵira.” Chotero, kulalikira kwa ophunzirawo kunagawiridwa kuchokera panyumba imodzi kunka ku ina. Pothirira ndemanga pa Machitidwe 20:20, Randolph O. Yeager analemba kuti Paulo anaphunzitsa “ponse paŵiri pamisonkhano yapoyera [de·mo·siʹa] ndi kunyumba ndi nyumba (liwu logawira [ka·taʹ] lolumikizidwa ndi ntchitoyo). Paulo anathera zaka zitatu ali mu Efeso. Iye anaichezera nyumba iriyonse, kapena kuti iye analalikira pafupifupi kwa anthu onse (vesi 26). Pano pakupezeka ukumu wa m’malemba wa ulaliki wa kunyumba ndi nyumba limodzinso ndi wochitidwira m’misonkhano yapoyera.”

5. Pa Machitidwe 20:20, kodi nchifukwa ninji Paulo sankasonya kwakukulukulu ku maulendo okacheza a akulu kapena kumaulendo aubusa?

5 Kugwiritsira ntchito ka·taʹ kofananako kukupezeka pa Luka 8:1, [NW] imene imamfotokoza Yesu kukhala akulalikira “kumzinda ndi mzinda ndi kumudzi ndi mudzi.” Paulo anagwiritsira ntchito liwu lochulukitsa lakuti kat’ oiʹkous pa Machitidwe 20:20. Panopa matembenuzidwe ena a Baibulo amaŵerengedwa kuti “m’nyumba zanu.” Koma mtumwiyo sankasonya kwakukulukulu kumaulendo a akulu okacheza kapena maulendo aubusa onka m’nyumba za akhulupiriri anzawo. Mawu ake otsatira amasonyeza kuti iye ankalankhula za uminisitala wa kunyumba ndi nyumba kwa osakhulupirira, pakuti anati: ‘Ndikuchitira umboni Ayuda ndi Ahelene wa kutembenuza mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Kristu.’ (Machitidwe 20:21) Akhulupiriri anzake adali atatembenuka mtima kale nasonyeza chikhulupiriro mwa Yesu. Chotero, onse aŵiri Machitidwe 5:42 ndi Machitidwe 20:20 akunena za kukalalikira kwa osakhulupirira “kunyumba ndi nyumba,” kapena kukhomo ndi khomo.

Palibe Chouloŵa Mmalo

6. Kodi nchiyani chomwe chanenedwa ponena za mtundu wa ntchito yolalikira ya Paulo mu Efeso?

6 Pothirira ndemanga pamawu a Paulo opezeka pa Machitidwe 20:20, Abiel Abbot Livermore analemba mu 1844 kuti: “Iye sanakhutiritsidwe ndi kupereka nkhani zokha m’misonkhano yapoyera, ndikugaŵira kupyolera m’zipangizo zina, koma anailondola mwachangu ntchito yake mseri, kunyumba ndi nyumba, ndipo kwenikweni anapereka chowonadi cha kumwamba kunyumba za padziko lapansi ndi m’mitima ya Aefeso.” Posachedwapa kwenikweni, kwazindikiridwa kuti: “Kuwanditsa uthenga wabwino kunyumba ndi nyumba nkomwe kunazindikiritsa Akristu a m’zaka za zana loyamba kuchokera pachiyambi (yerekezerani ndi Machitidwe 2:46; 5:42). . . . [Paulo] analichita mokwana thayo lake kwa onse aŵiri Ayuda ndi Akunja mu Efeso, ndipo analibe chodzikhululukira ngati akadafera m’machimo awo.”​—The Wesleyan Bible Commentary, Volyumu 4, masamba 642-3.

7. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti Mulungu amavomereza uminisitala wa kunyumba ndi nyumba wa Mboni za Yehova?

7 Chinkana kuti kulalikira kwapoyera kuli ndi malo ake m’kulengeza mbiri yabwino, iko sindiko choloŵa mmalo kufikira munthu mwini pakhomo. Pamfundoyi, katswiri wotchedwa Joseph Addison Alexander anati: “Tchalitchi sichinatumbebe njira iriyonse yoloŵa mmalo kapena kuchotsapo chiyambukiro cha kulalikira kwa eninyumba kochitidwa ndi tchalitchi.” Monga mmene katswiri O. A. Hills akufotokozera motere: “Kuphunzitsa poyera ndi kuphunzitsa kunyumba ndi nyumba ziyenera kuchitidwira pamodzi.” Mboni za Yehova zimapereka malangizo kupyolera m’nkhani zoperekedwa pa Misonkhano yawo Yapoyera ya mlungu ndi mlungu. Iwo alinso ndiumboni wowonekera wakuti njira yogwiritsiridwa ndi atumwi kufalitsa chowonadi cha Baibulo kunyumba ndi nyumba imabala zipatso. Ndipo Yehova amaivomerezadi, popeza kuti monga chotulukapo cha uminisitala woterowo, iye akupangitsa zikwi zambiri kuthamangira kukulambira kwake kokwezedwa chaka chirichonse.​—Yesaya 2:1-4; 60:8, 22.

8. (a) Kodi nchiyani chimene chanenedwa kukhala chifukwa chimene kulalikira kwa kunyumba ndi nyumba kuliri kobala zipatso? (b) Kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova zingayerekezedwere kwa Paulo m’kulalikira kwapakhomo ndikuchitira umboni kwina?

8 Bukhu lina lati: “Anthu amakumbukira mwamsanga zinthu zomwe zinaphunzitsidwa pakhomo pawo kuposa paguwa latchalitchi.” Eya, Paulo ananka m’makomo mokhazikika, nakhazikitsa chitsanzo chabwino monga minisitala. “Iye sanakhutiritsidwe ndikuphunzitsa ndi kupereka nkhani m’sunagoge ndi pamsika,” analemba tero katswiri wa Baibulo Edwin W. Rice. “Iye nthaŵi zonse anali wakhama ‘kuphunzitsa’ ‘kunyumba ndi nyumba.’ Kunali kupikisana ndi adani kunyumba ndi nyumba, pafupi mpafupi, kopenyana maso ndi maso, kufuna kutembenuzira anthu kwa Kristu, kumene iye anamenyera mu Efeso.” Mboni za Yehova zimadziŵa kuti kukambirana mwachindunji ndi munthu pakhomo kumabala zipatso. Kuwonjezera apa, izo zimapanga maulendo obwereza ndipo zimasangalala ngakhale kulankhula ndi otsutsa ngati anthuwa angavomereze kuti pakhale kukambirana kwabwino. Ndimofananadi ndi Paulo chotani nanga! Pofotokoza za iye, F. N. Peloubet analemba kuti: “Ntchito ya Paulo sinachitidwire yonse m’misonkhano. Mosakaikira iye anakachezera anthu ambiri mwiniyekha m’nyumba zawo atazindikira kuti munali munthu yemwe anafuna kumva, kapena wokondweretsedwa kwambiri kapena ngakhale wotsutsa kufuna kulankhula za chipembedzo.”

Akulu Afunikira Kutsogolera

9. Kodi Paulo anaŵakhazikitsira chitsanzo chotani akulu anzake?

9 Kodi Paulo anakhazikitsa chitsanzo chotani kwa akulu anzake? Iye anawasonyeza kuti ayenera kukhala alengezi olimba mtima ndi osatopa a mbiri yabwino kunyumba ndi nyumba. Mu 1879, J. Glentworth Butler analemba kuti: “[Akulu a ku Efeso] anadziŵa kuti m’kulalikira [kwa Paulo] iye sanawopsedwe nkomwe ndi kulingalira zangozi yomchitikira kapena kutchuka; ndikuti sanabise chowonadi chofunikira chirichonse; ndikuti sanasankhe mpang’ono pomwe, kukonda mbali yozizwitsa yokha kapena yotchuka ya chowonadi, koma anasonkhezera zinthu zokha ndi zonse zomwe zidali zopindulitsa ‘kuzigwiritsira ntchito kudyetsa,’ kapena kumangirira: kuyera kwa uphungu wonse wa Mulungu mokwanira! Ndipo ‘kuwusonyeza’ kokhulupirikaku, ‘kuphunzitsa’ kogomeka maganizoku kwa chowonadi Chachikristu ndiko kunali ntchito yake, osati m’masukulu a Turano okha ndi m’malo osonkhanira ena a ophunzirawo, koma ndi m’banja lirilonse lofikirika. Kunyumba ndi nyumba, ndi kwa munthu ndi munthu, iye analengeza mbiri yabwino tsiku ndi tsiku ndichikhumbo ndi chilakolako chonga cha Kristu. M’magulu onse ndi mafuko, kwa Ayuda achidani ndi Agiriki onyodola, mutu wake umodzi​—umene, utagogomezeredwa mokwanira, umaphatikizapo zowonadi zina zonse zopulumutsa​—udali kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro mwa Ambuye wathu Yesu Kristu.”

10, 11. (a) Ponena za uminisitala Wachikristu, kodi Paulo anayembekezera chiyani kwa akulu a ku Efeso? (b) Mofanana ndi Paulo, kodi ndimtundu wanji wa kulalikira umene Mboni za Yehova, kuphatikizapo akulu, ayenera kudzilowetsamo?

10 Pamenepo, nchiyani kwenikweni, chimene Paulo anayembekezera akulu a ku Efeso kuchita? Katswiri E. S. Young analongosola mwachidule mawu a mtumwiwo motere: “Sindinalankhule poyera pokha, koma ndinagwira ntchito kunyumba ndi nyumba, ndi magulu onse, onse aŵiri Ayuda ndi Akunja. Mutu wa uminisitala wanga ku magulu onse udali ‘kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu ndi chikhulupiriro mwa Ambuye wathu Yesu Kristu.’” Kufotokoza mawu a Paulo m’njira ina, W. B. Riley analemba motere: “Tanthauzo lomvekera lidali ili: ‘Ndikukuyembekezerani kupitiriza ndi zimene ndinayamba, ponse paŵiri kuzichita ndi kuziphunzitsa ndipo ndikukuyembekezerani kutsutsa monga mmene ndinatsutsira; kuphunzitsa ponse paŵiri mseri ndi poyera monga mmene ndinachitira m’makwalala ndikunyumba ndi nyumba, kuchitira umboni mofananamo kwa Ayuda ndi kwa Agiriki kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu ndi chikhulupiriro mwa Ambuye wanthu Yesu Kristu, pakuti izi ndizo zazikulu!’”

11 Mwachiwonekere, m’Machitidwe mutu 20, Paulo ankasonyeza akulu anzake kuti ankayembezeredwa kukhala mboni za kunyumba ndi nyumba za Yehova. Pamfundoyi, akulu a m’zaka za zana loyamba anafunikira kutsogolera, kukhazikitsira ziŵalo zina za mpingo chitsanzo chabwino. (Yerekezerani ndi Ahebri 13:17.) Pamenepo, mofanana ndi Paulo, Mboni za Yehova zimalalikira kunyumba ndi nyumba, zikumauza anthu a mitundu yonse ponena za Ufumu wa Mulungu, kutembenuka mtima kulinga kwa Iye, ndi chikhulupiriro mwa Yesu Kristu. (Marko 13:10; Luka 24:45-48) Ndipo m’ntchito ya kunyumba ndi nyumba yoteroyo, akulu oikidwa pakati pa Mboni zamakono amayembekezeredwa kutsogolera.​—Machitidwe 20:28.

12. Kodi nchiyani chimene akulu ena akale anakana kuchita, koma kodi akulu amatsogolera m’chiyani lerolino?

12 Mu 1879, Charles Taze Russell anayamba kufalitsa Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence, yomwe tsopano imatchedwa Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova. Russell ndi Ophunzira Baibulo ena analengeza uthenga wa Ufumu m’njira ya atumwi. Komabe, m’zaka zapambuyo pake, akulu ena a m’mipingo sanalabadire mathayo awo ochitira umboni. Mwachitsanzo, Mboni ina inalemba kuti: “Zinthu zonse zinachitika bwino kufikira pamene chilengezo chinapangidwa chakuti onse akhalemo ndi phande m’kuchitira umboni kwa kunyumba ndi nyumba ndi mabuku ndipo makamaka ntchito ya kunyumba ndi nyumba ya pa Sande​—umu munali mu 1927. Akulu athu osankhidwa anachitsutsa ndipo anayesa kukhumudwitsa gulu lonse kusaichita kapena kusakhala ndi phande mu iriyonse ya ntchito yoteroyo.” M’kupita kwanthaŵi, amuna amene sanadziphatike m’kulalikira kwa kunyumba ndi nyumba sanapatsidwenso mwaŵi wa kutumikira monga akulu. Lerolinonso, awo otumikira monga akulu ndi atumiki otumikira amayembekezeredwa kutsogolera m’kuchitira umboni kunyumba ndi nyumba ndi mitundu ina ya uminisitala Wachikristu.

Aliyense Ayenera Kukhala Mboni

13. (a) Kodi tiyenera kuchitanji ngakhale ngati anthu samvetsera kuuthenga Waufumu? (b) Kodi Paulo wayerekezeredwa motani ndi Ezekieli?

13 Ndi thandizo la Yehova, Akristu ayenera kulengeza uthenga Waufumu kunyumba ndi nyumba, ngakhale ngati sukulandiridwa moyamikira. Monga mlonda wa Mulungu, Ezekieli anafunikira kuŵachenjeza anthu mosasamala kanthu kuti anamumvetsera kapena ayi. (Ezekieli 2:5-7; 3:11, 27; 33:1-6) Poika kufanana pakati pa Ezekieli ndi Paulo, E. M. Blaiklock analemba kuti: “Kuchokera [m’ndemanga za Paulo m’Machitidwe mutu 20] mumawonekera chithunzi chabwino chauminisitala mu Efeso. Tamvani zotsatirazi: Choyamba, kukhulupirika kofulumira kwa Paulo. Iye sanafunefune kutchuka kapena kuvomerezedwa ndi anthu. Iye anadzikhazika ku ntchito yaulonda mofanana ndi Ezekieli, anaichita ntchito yake ndi changu chowona mtima ndi mkhalidwe wochilikiza mawu ake. Chachiŵiri, kumverera chisoni kwake kwachikondi. Iye sanali munthu wolengeza mawu achiwonongeko popanda kumva chifundo. Chachitatu, unali ulaliki wake wosatopa nawo. Iye analalikira uthenga wabwino poyera ndi kunyumba ndi nyumba, mumzinda ndi m’dera lonselo.”

14. Kodi nchifukwa ninji kuchitira umboni kuli thayo la munthu aliyense amene apanga kudzipereka kwa Yehova Mulungu m’pemphero kupyolera mwa Yesu Kristu?

14 Dalitso lochuluka la Mulungu pa atumiki ake amakono limachotsapo kukaikira kuti iye ngwosangalatsidwa kuwalola kutchedwa ndi dzina lakuti Mboni za Yehova. (Yesaya 43:10-12) Kuwonjezera apa, iwo ndiwonso mboni za Kristu, popeza kuti Yesu anawauza motere ophunzira ake: ‘Mudzalandira mphamvu, mzimu woyera utadza pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.’ (Machitidwe 1:8) Chotero kuchitira umboni ndiko thayo la munthu aliyense yemwe apanga kudzipereka kwa Yehova Mulungu m’pemphero kupyolera mwa Yesu Kristu.

15. Kodi nchiyani chomwe chanenedwa ponena za ntchito yochitira umboni ya Akristu oyambirira?

15 Ponena za kuchitira umboni kwanenedwa kuti: “Iko kunaphatikiza tchalitchi chonse. Ntchito yaumishonale ya tchalitchi choyambirira siinali thayo la Women’s Missionary Society kapena Foreign Mission Board lokha. Ndipo ntchito ya kuchitira umboni siinasidwire kwa anthu okhala ndi maudindo okha monga ngati akulu, adikoni, kapena ngakhale atumwi. . . . M’masiku oyambirirawo tchalitchi chinali ntchito. Programu yaumishonale ya tchalitchi choyambirira inazikidwa pa zinthu ziŵiri izi: (1) Ntchito yaikulu ya tchalitchi inali kulengeza padziko lonse. (2) Thayo la kuchita ntchitoyi linali la Akristu onse.”​—J. Herbert Kane.

16. Kodi olemba nkhani a m’Chikristu Chadziko nawonso amavomerezadi motani ponena za Akristu ndi kuchitira umboni?

16 Chinkana kuti olemba nkhani amakono a Chikristu Chadziko samavomerezana ndi uthenga wa Ufumu, ena amavomereza kuti Akristu ali ndi thayo la kuchitira umboni. Mwachitsanzo, m’bukhu lakuti Everyone a Minister, Oscar E. Feucht anati: “Palibe pasitala amene angakwaniritse yekha uminisitala umene Mulungu anaupereka kwa wokhulupirira aliyense. Mwatsoka kulingalira kolakwika kwa zaka mazana ambiri m’tchalitchi kwapangitsa ntchito ya agulupa 500 kukhala ntchito ya pasitala mmodzi. Sizinali tero m’tchalitchi choyambirira. Anthu amene anakhulupirira ananka kulikonse kulalikira Mawu.”

17. Kodi chinganenedwe nchiyani ponena za malo amene kuchitira umboni kunatenga m’miyoyo ya Akristu oyambirira?

17 Kuchitira umboni kunali chinthu chachikulu m’miyoyo ya Akristu oyambirira, mongadi mmene kuliri kwa Mboni za Yehova lerolino. “Kufotokoza mwachisawawa,” analemba tero Edward Caldwell Moore wa pa Harvard University kuti, “zaka mazana atatu zoyambirira za gulu la Chikristu zinazindikiridwa ndi kutenthedwa maganizo kwakukulukulu kaamba ka kuwanditsa chikhulupiriro. Chifundo Chachikristu chinasonyezedwa m’kulengeza, kufotokozera ena uthenga wa chiwombolo. . . . Komabe, kufalitsa chisonkhezero ndi ziphunzitso za Yesu kunachitidwa m’nyengo yoyambirira, mwapang’ono ndi amuna omwe tiyenera kuwatcha amishonale. Uku kunafikiridwa ndi amuna a maluso ndi ntchito iriyonse ndi aliyense m’chitaganya. [Iwo] anachifalitsa chinsinsi chimenecho cha munthu wamkati kumalekezero akutali a ufumu wa [Roma], mkhalidwe watsopano umenewo kulinga kudziko, umene malinga ndi zokumana nazo zawo unaphatikizapo chipulumutso. . . . [Chikristu choyambirira] chinakhutiritsidwa mwakuya za kuyandikira kwa mapeto a dongosolo lamakono ladziko. Icho chinakhulupirira m’kukhazikitsidwa kwamwadzidzidzi ndi kozizwitsa kwa dongosolo latsopano ladziko.”

18. Kodi nchiyembekezo chachikulu chotani chimene chimaposa maloto a atsogoleri andale zadziko?

18 M’kuchitira umboni kunyumba ndi nyumba ndi mitundu ina yauminisitala wawo, Mboni za Yehova zimatsogoza amvetseri awo mwachimwemwe kudziko latsopano limene Mulungu walonjeza. Madalitso ake onenedweratu a moyo wosatha amasiyana kwambiri ndi maloto okondedwa ndi anthu amakono omwe amalingalira kuti ndiwo adzapanga dongosolo la dziko latsopano. (2 Petro 3:13; Chibvumbulutso 21:1-4) Chinkana kuti kungawonedwe kuti aliyense adzafuna kukhala ndi moyo m’dziko labwino latsopano la Mulungu, ichi sichidzakhala tero. Komabe, tiyeni chotsatira tilingalire njira zopindulitsa zimene atumiki a Yehova angaphunzitsire ofunafuna moyo wosatha.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti Machitidwe 5:42 ndi Machitidwe 20:20 amatanthauza kuti atsatiri a Yesu ayenera kulalikira kunyumba ndi nyumba?

◻ Kodi timadziŵa motani kuti Mulungu amavomereza uminisitala wa kunyumba ndi nyumba wa Mboni za Yehova?

◻ Ponena za uminisitala, kodi chimafunikira nchiyani kwa akulu ndi atumiki otumikira?

◻ Kodi kuchitira umboni kuyenera kukhala ndi malo otani m’moyo wa Mkristu?

[Chithunzi patsamba 10]

Mu 33 C.E., ophunzira a Yesu anachitira umboni kunyumba ndi nyumba osaleka

[Chithunzi patsamba 13]

Paulo anaphunzitsa ‘kunyumba ndi nyumba.’ Mtundu umenewu wa uminisitala ukuchitidwa ndi Mboni za Yehova lerolino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena