Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/09 tsamba 1
  • Adzamva Bwanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Adzamva Bwanji?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Kulengeza Uthenga Wabwino Mosaleka
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Chifukwa Chake Timapita Mobwerezabwereza
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Pitirizani Kulalikira Ufumu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Lalikirani Mwakhama
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 1/09 tsamba 1

Adzamva Bwanji?

1. Kodi n’chifukwa chiyani nthawi zina ntchito yolalikira ingakhale yovuta, koma n’chifukwa chiyani timalimbikirabe kulalikira?

1 Popeza kuti tsiku la Yehova likuyandikira kwambiri, tifunika kuchita changu kuti tithandize anthu ambiri kudziwa Mulungu molondola ndi cholinga chake chokhudza anthu. (Yoh. 17:3; 2 Pet. 3:9, 10) Nthawi zina zimenezi zingakhale zovuta popeza anthu ambiri sakhala ndi chidwi ndipo ena amatinyoza chifukwa cha ntchito yathu yolalikira. (2 Pet. 3:3, 4) Ngakhale zili choncho, tili ndi zifukwa zokhulupirira kuti m’gawo lathu mudakali anthu ena omwe titawalalikira, angamvetsere uthenga wabwino. Ndiye kodi anthu amenewa angamve bwanji popanda wina kuwalalikira?—Aroma 10:14, 15.

2. Kodi chitsanzo cha mtumwi Paulo chikutilimbikitsa kuchita chiyani?

2 Kupirira Chitsutso: Popeza pali anthu amene akufuna kumva uthenga wa Ufumu, sitiyenera kusiya kulalikira. Ku Ulaya, mzinda umene unali woyamba kumva mtumwi Paulo akulalikira uthenga wabwino unali wa Filipi. Anthu kumeneko ananenera Paulo ndi Sila mabodza, ndipo anawakwapula ndi zikoti ndi kuwaponya m’ndende. (Mac. 16:16-24) Komabe Paulo sanachite mantha ndi zimenezi n’kusiya kulalikira. Atafika ku Tesalonika, mzinda wotsatira paulendo wake waumishonale, ‘analimba mtima mwa Mulungu.’ (1 Ates. 2:2) Chitsanzo cha Paulo chikusonyeza chifukwa chake ifenso sitiyenera ‘kuleka’ kulalikira.—Agal. 6:9.

3. N’chifukwa chiyani anthu ena amene kale analibe chidwi angasinthe maganizo awo n’kuyamba kumvetsera?

3 Anthu ambiri amene kwa zaka zambiri akhala akukana uthenga wathu asintha maganizo awo. Zimenezi zachitika mwina chifukwa cha mavuto azachuma, kudwala, imfa ya wachibale, kapena chifukwa cha nkhani zodetsa nkhawa zimene amva zikuchitika padzikoli. (1 Akor. 7:31) Ena amene makolo awo sankawalola kumvetsera, akula ndipo akufunitsitsa kumvetsera. Tikamapitirizabe kulalikira, timapereka mwayi kwa anthu amenewa “woitana pa dzina la Yehova” nthawi isanathe.—Aroma 10:13.

4. Kodi n’chiyani chimatilimbikitsa kupitirizabe kulalikira?

4 Tisaleke Kulalikira: Chikondi chathu pa Mulungu ndiponso anthu chimatilimbikitsa kupitirizabe kugwira nawo ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira, mofanana ndi atumwi. (Mac. 5:42) Anthu ambiri masiku ano “akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse” zimene zikuchitika. (Ezek. 9:4) Anthu amenewa akamva uthenga wabwino, amakhala ndi chiyembekezo ndipo amapeza mpumulo. Malemba amatitsimikizira kuti Yehova amakondwera ndi khama lathu ngakhale pamene anthu ambiri akukana kumvetsera.—Aheb. 13:15, 16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena