Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/07 tsamba 7-8
  • Chifukwa Chake Timapita Mobwerezabwereza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chake Timapita Mobwerezabwereza
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Nkhani Yofanana
  • “Tafola Gawo Lathu Kambirimbiri!”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Musaleme Pakuchita Zabwino
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi N’chifukwa Chiyani Tifunika Kupitiriza Kulalikira?
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Kodi Nchifukwa Ninji Timabwererako?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 7/07 tsamba 7-8

Chifukwa Chake Timapita Mobwerezabwereza

1. Kodi pali funso lotani lonena za ntchito yathu yolalikira?

1 M’madera ambiri, timafola magawo athu kawirikawiri. Mobwerezabwereza, timapitabe ku nyumba zimodzimodzi ngakhale kuti mwina eninyumbazo amatiuza kuti alibe chidwi. N’chifukwa chiyani timapitabe kwa anthu amene sanasonyeze chidwi m’mbuyomu?

2. Kodi chifukwa chachikulu chimene timapitirizira kulalikira n’chiyani?

2 Kukonda Yehova Ndiponso Anthu: Chifukwa chachikulu chimene timapitirizira kulalikira n’choti timakonda Yehova. Mtima wathu umatilimbikitsa kuti tipitirize kuuza anthu ena za Mulungu wathu wamkulu. (Luka 6:45) Popeza kuti timakonda kwambiri Yehova, timamvera malamulo ake ndipo timathandiza anthu ena kuti atero. (Miy. 27:11; 1 Yoh. 5:3) Kaya anthu amvetsere kapena ayi, ife timapirirabe mokhulupirika pantchito imeneyi. Ngakhale pamene Akhristu oyambirira anazunzidwa, anapitirizabe kulalikira “mwakhama.” (Mac. 5:42) Anthu akamakana kumvetsera, sitilola zimenezi kutifooketsa koma timapitirizabe m’ntchito yathu ndipo timasonyeza kuti ndife odzipereka kwa Yehova ndiponso timam’konda kwambiri.

3. Kodi kukonda anthu kungatithandize bwanji kuti tipitirize kulalikira?

3 Timapitirizanso kulalikira chifukwa choti timakonda anansi athu. (Luka 10:27) Yehova safuna wina aliyense akawonongeke. (2 Pet. 3:9) Ngakhale m’magawo amene timafola kawirikawiri, timapezabe anthu amene akufuna kutumikira Yehova. Mwachitsanzo, kuzilumba za Guadeloupe kumene munthu mmodzi pa anthu 56 alionse ndi wa Mboni za Yehova, anthu 214 anabatizidwa chaka chatha. Anthu pafupifupi 20,000 anafika pa Chikumbutso, kutanthauza munthu mmodzi pa anthu 22 aliwonse a pazilumbazi.

4. Kodi magawo amasintha motani?

4 Zinthu Zimasintha M’gawo: Zinthu zimasinthasintha m’magawo athu. Tikapitanso ku nyumba imene anthu sanamvetsere, mwina munthu wina wa m’banjamo, yemwe sanamvepo uthenga wathu, angatilandire ndi kumvetsera uthengawo. Kapena tingapeze anthu atsopano amene angolowa kumene m’nyumbayo omwe ali ndi chidwi. Ndiponso ana amene makolo awo amakana kumvetsera, amakula ndi kukakhala paokha. Ana amenewa angafune kumvetsera uthenga wa Ufumu.

5. Kodi anthu angayambe kumvetsera uthenga wathu chifukwa cha zinthu zotani?

5 Anthunso amasintha. Mtumwi Paulo panthawi ina anali “wonyoza ndi wozunza ndiponso wachipongwe.” (1 Tim. 1:13) N’chimodzimodzinso ndi anthu ambiri amene akutumikira Yehova masiku ano, kale analibe chidwi ndi choonadi. Ena kale mwina ankatsutsa kwambiri uthenga wabwino. Zinthu m’dzikoli zikamasintha, anthu otsutsa kapena amene kale analibe chidwi angayambe kumvetsera uthenga wathu. Ena angayambe kutero atakumana ndi mavuto monga imfa ya munthu wa m’banja lawo, kuchotsedwa pa ntchito, mavuto a zachuma, kapena matenda.

6. N’chifukwa chiyani tifunikira kupitirizabe kulalikira mwakhama?

6 Ngakhale kuti dongosolo la zinthuli lidzatha posachedwapa, ntchito yathu yolalikira ndi kuphunzitsa ikupitabe patsogolo kwambiri. (Yes. 60:22) Choncho timapitirizabe kulalikira mwakhama ndi kukhala ofunitsitsa kugwira ntchito imeneyi. Mwina munthu yemwe tingadzam’lalikire angamvetsere uthenga wathu. Tifunikira kupitirizabe kulalikira ndipo ‘potero, tidzadzipulumutsa ife eni ndi aja otimvera ife.’—1 Tim. 4:16.

(Yapitirizidwa pa tsa. 8, danga 1)

Mobwerezabwereza (Yapitirizidwa)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena