Kodi Nchifukwa Ninji Timabwererako?
1 Kodi munadzifunsapo funso limenelo, mwinamwake pamene munali kukonzekera kuthera tsiku mu utumiki? Kwina kumene timafola gawo lathu kaŵirikaŵiri, eni nyumba ambiri amatizindikira msanga ndipo amatikanira mobwerezabwereza. Oŵerengeka chabe ndiwo amavomereza. Komabe, pali zifukwa zabwino zambiri zimene timabwerererako.
2 Choyamba, timalamulidwa kulalikirabe uthenga wa Ufumu mpaka mapeto atafika. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Mneneri Yesaya anafunsa kuti ntchito yake yolalikirayo adzaipitirizabe mpaka liti. Yankho lomwe analandira lalembedwa pa Yesaya 6:11. Palibe kukayikira—anamuuza kuti azipitabe kwa anthuwo ndi uthenga wa Mulungu. Mofananamonso lero, Yehova amafuna kuti tiziwafikirabe anthu okhala m’dera lathu, ngakhale amatikanira. (Ezek. 3:10, 11) Umenewu ndi udindo wopatulika umene anatiikizira.—1 Akor. 9:17.
3 Chifukwa china chimene timabwererako nchakuti kutero kumatipatsa mpata wosonyeza ukulu wake wa chikondi chathu pa Yehova. (1 Yoh. 5:3) Ndiponso, pamene tikulingalira zimene zikudikira anthu mtsogolomu, tingalekerenji kuyesa kuwachenjeza anansi athu mwachikondi? (2 Tim. 4:2; Yak. 2:8) Kukhulupirika kwathu pogwira ntchitoyi kumawapatsa mipata yambiri yolabadira uthenga wa Mulungu wachipulumutso, kuti asadzathe kunena kuti sitinawachenjeze.—Ezek. 5:13.
4 Ndiponso, sitingadziŵe pamene anthu ena adzasintha maganizo awo. Chimene chingachititse chingakhale kusintha kwa mikhalidwe yawo, tsoka m’banja lawo, kapena zochitika m’dziko zimene zimawachititsa kuganiza kwambiri za mtsogolo. Ndiyeno, kanthu kena kamene tinganene pakhomo lawo kangawalase mtima. (Mlal. 9:11; 1 Akor. 7:31) Ndiponso, anthu amasamuka. Tingapeze anthu atsopano m’dera lathu omwe adzamvetsera uthenga wabwino—kapena achinyamata amsinkhu amene tsopano akukhala okha ndipo akuganiza mozama za cholinga cha moyo wawo.
5 Kodi tizibwererakobe? Inde! Malemba amatisonkhezera kwambiri kumabwererabe kwa anthuwo. Kumapeto, titaimaliza ntchito yolalikirayi, Yehova adzatidalitsa chifukwa cha khama lathu mu utumiki, ndipo adzadalitsanso aja amene alabadira uthenga wabwino wa Ufumu.—1 Tim. 4:16.