Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/02 tsamba 8
  • Kodi N’chifukwa Chiyani Tifunika Kupitiriza Kulalikira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi N’chifukwa Chiyani Tifunika Kupitiriza Kulalikira?
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Nkhani Yofanana
  • Pitirizani Kulalikira Ufumu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • “Tsopano Uwauze” Mawu Awa
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Chifukwa Chake Timapita Mobwerezabwereza
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • “Pitani Mukaphunzitse Anthu a Mitundu Yonse”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
Onani Zambiri
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 2/02 tsamba 8

Kodi N’chifukwa Chiyani Tifunika Kupitiriza Kulalikira?

1 Kodi ntchito yolalikira Ufumu yakhala ikuchitika m’dera lanu kwa nthaŵi yaitali? (Mat. 24:14) Ngati ndi choncho, mungaganize kuti anthu alalikira mokwanira m’gawo la mpingowo. Mwinamwake panopa mukamalalikira, anthu ambiri amene mumapezana nawo amaoneka amphwayi ndi uthenga wa Ufumu. Ngakhale zitakhala choncho, onani zimene buku la Ulosi wa Yesaya Gawo 2 tsamba 141, likunena za ophunzira oona a Yesu. Limati: “M’malo ena, zotsatira za utumiki wawo zingaoneke kukhala zosanunkha kanthu poyerekeza ndi ntchito imene agwira komanso kuyesetsa kumene anachita. Komabe, iwo amapirira.” Koma kodi n’chifukwa chiyani tikufunika kupitiriza kulalikira?

2 Kumbukirani Yeremiya: Kupirira kwathu mokhulupirika mu ntchito yolalikira kusamadalire pa kumvetsera kapena kusamvetsera kwa anthu. Yeremiya analalikira mu mzinda umodzimodzi womwewo kwa zaka 40 ngakhale kuti oŵerengeka okha ndi amene anamvetsera uthenga wake ndipo ambiri ankatsutsa. N’chifukwa chiyani Yeremiya anapirira? Chifukwa chakuti ankagwira ntchito imene Mulungu anam’lamulira kuti agwire ndipo kudziŵa zimene zinali kutsogolo kunam’limbikitsa kupitirizabe kulankhula molimba mtima.—Yer. 1:17; 20:9.

3 Zimenezi zilinso chimodzimodzi kwa ife. Yesu “anatilamulira ife tilalikire kwa anthu, ndipo tichite umboni kuti Uyu ndiye amene aikidwa ndi Mulungu akhale woweruza amoyo ndi akufa.” (Mac. 10:42) Uthenga umene timalalikira ndi nkhani ya moyo ndi imfa kwa amene akumva. Anthu adzaweruzidwa malingana ndi momwe akuchitira ndi uthenga wabwino. Popeza zili choncho, ntchito yathu ndiyo kuchita zomwe tatumidwa. Ngakhale anthu asamvetsere, kupitiriza kuchita zimene tatumidwa kumatipatsa mpata wosonyeza kukula kwa chikondi chimene tili nacho pa anthu komanso kudzipereka kwathu kwa Yehova. Komabe pali zina zambiri.

4 Tikupindula: Kuchita chifuniro cha Mulungu, mosasamala kanthu za momwe anthu akuchitira m’gawo, kumatipatsa mtendere wa mumtima, chikhutiro, ndi chimwemwe, zimene sitingazipeze mwa njira ina iliyonse. (Sal. 40:8) Moyo wathu umakhala watanthauzo. Kutenga nawo mbali mokwanira mu utumiki, kumachititsa mitima ndi maganizo athu kukhala pa chiyembekezo ndi chimwemwe chimene tidzakhale nacho m’dziko latsopano la Mulungu. Kuganizira malonjezo a m’Malemba ameneŵa kumawonjezera kukula kwathu mwauzimu ndipo kumalimbitsa unansi wathu ndi Yehova.

5 Ngakhale zotsatira za ntchito yathu yolalikira zisaonekere nthaŵi yomweyo, mbewu ya choonadi ingakhale itabzalidwa mu mtima mwa munthuyo imene idzamere m’nthaŵi yoikika ya Yehova. (Yoh. 6:44; 1 Akor. 3:6) Palibe wina wa ife amene akudziŵa kuti mwa ntchito imene anthu a Yehova akugwira, ndi anthu ena angati amene adzaphunzire za Ufumu m’dera lawo kapena padziko lonse.

6 Koposa kale lonse, timvere langizo la Yesu lakuti: “Yang’anirani, dikirani, pempherani: pakuti simudziŵa nthaŵi yake. Ndipo chimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, dikirani.” (Marko 13:33, 37) Choncho, tiyenitu tonse tipitirize kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu, tisangalatse mtima wa Yehova pamene tikuyeretsa nawo dzina lake lalikulu ndi loyera.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena