“Tafola Gawo Lathu Kambirimbiri!”
1 Kodi munayamba mwalingalirapo kuti gawo lanu lafoledwa kwambiri moti simungapezekenso anthu onga nkhosa? Mwina munaganizapo kuti: ‘Ndikudziŵa zimene anthu akanene. Ndivutikirenji kupita kwa anthu opanda chidwi?’ N’zoona kuti magawo ambiri akufoledwa kaŵirikaŵiri. Komabe, tione zimenezi ndi malingaliro oyenera osati olakwika. Chifukwa chiyani tiyenera kutero? Onani zifukwa zinayi zili m’munsizi.
2 Mapemphero Athu Ayankhidwa: Yesu anati: “Zinthu zichuluka, koma antchito achepa; potero pemphani Mwini zinthu, kuti akankhe antchito kukututa kwake.” (Luka 10:2) Tam’pempha Yehova kwa zaka zambiri kuti atipatse antchito ochuluka. Tsopano m’madera ambiri, muli antchito ochuluka amene timafuna, ndipo tikufola magawo pafupipafupi kwambiri. Kodi si zosangalatsa kuti Yehova wayankha mapemphero athu?
3 Khama Lipindula: Ngakhale m’magawo ofoledwa kaŵirikaŵiri, anthu akulabadira uthenga wa Ufumu ndipo akudziŵa choonadi. Choncho, tipitirize kuwayendera mobwerezabwereza, ndi chiyembekezo chakuti tidzapeza anthu ambiri oona mtima. (Yes. 6:8-11) Monga anachitira atumwi a Yesu oyambirira, ‘pitanibe’ kwa anthu a m’gawo lanu, yesetsani kuwachititsa chidwi ndi Ufumu wa Mulungu.—Mat. 10:6, 7.
4 Ku Portugal mipingo yambiri imamaliza kufola magawo awo mlungu uliwonse, koma akupezabe anthu onga nkhosa. Makamaka mlongo wina ali ndi malingaliro abwino kwambiri. Akuti: “Mmawa uliwonse asananyamuke kupita ku ulaliki, amapempha Yehova kuti am’thandize kupeza munthu wofuna kuphunzira Baibulo.” Tsiku lina anakonza zokaphunzira ndi ogwira ntchito m’shopu yometa tsitsi. Koma munthu mmodzi yekha ndiye anabwera kudzaphunzira. Munthuyo anamuuza mlongoyo kuti: “Ena onse sakufuna.” Isanathe miyezi iŵiri anali kuchititsa maphunziro a Baibulo aŵiri. Kenako anabatizidwa, ndipo anayamba utumiki waupainiya!
5 Ntchito Ikutha: Uthenga wabwino ukulalikidwa, monga Yesu ananenera. (Mat. 24:14) Ngakhale m’madera amene anthu safuna ‘kumvetsera,’ akuchenjezedwa mwa ntchito yolalikira. Timayembekezera ena kukana kapena kutsutsa choonadi. Komabe, anthu ameneŵa afunika kuwachenjeza za chiŵeruzo cha Yehova chikubweracho.—Ezek. 2:4, 5; 3:7, 8, 19.
6 Sitinathe: Si ife ofunika kunena polekezera ntchito yolalikira. Yehova ndiye akudziŵa polekezera pake penipeni. Akudziŵa ngati m’gawo lathu muli amene angamvetsere uthenga wabwino. Lerolino, anthu ena amati alibe chidwi, koma chifukwa cha zochitika mwadzidzidzi m’moyo wawo monga kuchotsedwa ntchito, matenda akayakaya, imfa ya munthu amene amam’konda—angamvetsere kwambiri nthaŵi ina. Chifukwa cha tsankho kapena chifukwa chotanganidwa kwambiri, anthu ambiri sanamvebe bwinobwino zimene timalalikira. Kuwayendera mwaubwenzi mobwerezabwereza kudzawathandiza kuzindikira ndiponso kumvetsera.
7 Amene akula posachedwapa ndipo tsopano ali ndi mabanja awo akuona moyo mwauchikulire kwambiri ndipo akufunsa zimene Mawu a Mulungu okha ndiwo angayankhe. Mayi wina wachitsikana anaitana Mboni ziŵiri kunyumba kwake ndipo anati: “Ndili mwana, sindinkadziŵa chifukwa chake mayi ankathamangitsa Mboni n’kuziuza kuti alibe chidwi, pomwe izo zinkabwerera kukambirana za m’Baibulo basi. Ndinaganiza kuti ndikadzakula, n’kukwatiwa, ndiponso ndikadzakhala ndi nyumba yanga, ndidzaitana Mboni za Yehova kunyumba kwanga kuti zikandifotokozere Baibulo.” Ndizo anachita, ndipo izi zinasangalatsa Mboni zimene zinam’fikira.
8 Kodi Mungakhale Wogwira Mtima Kwambiri? Sikuti nthaŵi zonse amene amapangitsa kuti kufola gawo pafupipafupi kukhale kovuta ndi anthu amene timawafikira ayi. Nthaŵi zina ndife amene timapangitsa. Kodi timapita tili ndi malingaliro oipa? Zimenezo zidzakhudza mtima wathu, mawu athu ndi nkhope yathu. Khalani ndi malingaliro abwino ndiponso nkhope yachimwemwe. Yesani kufika mwanjira ina. Sinthani ulaliki wanu ndipo yesetsani kuwongolera. Mukhoza kusintha funso lanu loyamba kapena kugwiritsa ntchito lemba lina pokambirana. Funsani abale ndi alongo ena zimene apeza kuti n’zothandiza pofola gawo. Yendani mu utumiki ndi ofalitsa komanso apainiya osiyanasiyana, ndipo onani zimene zimapangitsa utumiki wawo kukhala wogwira mtima.
9 Yehova wavomereza komanso akudalitsa ntchito yolalikira Ufumu, ndipo kugwira nawo ntchitoyi kumasonyeza kuti timam’konda ndiponso kuti timakonda anansi athu. (Mat. 22:37-39) Choncho tigwire ntchito yathu mpaka kumaliza, tisatope kufola gawo mobwerezabwereza.