Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/13 tsamba 2
  • Kodi Mungapemphe Gawo Lanulanu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungapemphe Gawo Lanulanu?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Muli ndi Gawo Lanulanu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Njira Zolalikirira Uthenga Wabwino
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Misonkhano Yokonzekera Utumiki Wakumunda
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Mmene Tingalalikirire M’gawo la Malonda
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
km 1/13 tsamba 2

Kodi Mungapemphe Gawo Lanulanu?

1. N’chifukwa chiyani mungachite bwino kuganizira zokhala ndi gawo lanulanu?

1 N’chifukwa chiyani mungachite bwino kuganizira zokhala ndi gawo lanulanu? Ngati mpingo wanu uli ndi gawo lalikulu, mungapemphe gawo lanulanu loti muzilalikirako, mwina pafupi ndi kumene mukukhala. Buku la Gulu patsamba 103 limati: “Kukhala ndi gawo kufupi ndi kwanu kudzakuthandizani kugwiritsa ntchito bwino nthawi imene mungachitire utumiki wa kumunda. Ndiponso, mukhoza kuuza wofalitsa wina kuti akalalikire nanu limodzi m’gawo lanulo.”

2. Kodi kukhala ndi gawo lanulanu kungathandize bwanji kagulu kanu ka utumiki?

2 Mumathandiza Kagulu Kanu ka Utumiki: Ngati mutapempha gawo lanulanu pafupi ndi kuntchito kwanu kapena malo amene mumachitira malonda, mukhoza kumalalikira pa nthawi yopuma masana kapena mukangoweruka. Mwina mungagwirizane ndi wofalitsa wina kuti muzikhala awiri. Ndipo ngati mungapemphe gawo lanulanu pafupi ndi kunyumba kwanu, ndiye kuti inuyo kapena anthu ena a m’banja mwanu akhoza kumalalikira mosavuta m’gawolo madzulo. Komabe, ngati mukupita kokalalikira m’gawo lanulanu, m’poyenera kuti muzipemphera kwa Yehova kuti akutsogolereni musanayambe kulalikira. (Afil. 4:6) Kuwonjezera pamenepa, muyenera kugawa bwino nthawi yanu kuti muzithanso kulowa mu utumiki ndi kagalu kanu ka utumiki. Makamaka Loweruka ndi Lamlungu, pamene magulu ambiri a utumiki amakumana kuti alowe mu utumiki, ndi bwino kuti muzilowa mu utumiki ndi kagulu kanu.

3. Kodi kukhala ndi gawo lanulanu kuli ndi ubwino wotani?

3 Ubwino Wake: Ngati muli ndi gawo lanulanu, mukhoza kumalalikira pa nthawi iliyonse imene muli ndi mpata. Komanso mukhoza kumathera nthawi yambiri mu utumiki chifukwa simungafunikire kuyenda ulendo wautali kupita kugawo lanu. Zimenezi zimathandiza ofalitsa ena kuchita upainiya wothandiza kapena wokhazikika. Popeza anthu amene mumawalalikira amakhala m’dera lanu lomwelo, zimakhala zosavuta kuchita maulendo obwereza komanso kuchititsa maphunziro a Baibulo. Ofalitsa ambiri amene amalalikira m’gawo lawolawo amaona kuti kulalikirako kumawathandiza kudziwana bwino ndi anthu ambiri a m’gawolo. Zimenezi zimatheka makamaka ngati wofalitsa atalalikira gawo lonselo maulendo angapo, asanabweze gawolo kumpingo kuti ofalitsa enanso alipemphe. Choncho mungachite bwino kupempha gawo lanulanu chifukwa zimenezi zingathandize inuyo pamodzi ndi anthu a m’banja mwanu kuti muzikwaniritsa mbali zonse za utumiki wanu.—2 Tim. 4:5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena