Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • od mutu 9 tsamba 87-104
  • Njira Zolalikirira Uthenga Wabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njira Zolalikirira Uthenga Wabwino
  • Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KULALIKIRA KUNYUMBA NDI NYUMBA
  • KUFUFUZA ANTHU OYENERERA
  • KUPANGA MAULENDO OBWEREZA
  • KUCHITITSA MAPHUNZIRO A BAIBULO
  • KUTHANDIZA ANTHU ACHIDWI KUTI ADZIWE GULU LA YEHOVA
  • KUGWIRITSA NTCHITO MABUKU OTHANDIZA POPHUNZIRA BAIBULO
  • KULALIKIRA MWAMWAYI
  • GAWO
  • KULALIKIRA ANTHU AZINENERO ZONSE
  • KULALIKIRA M’MAGULU
  • Kukhazikitsa Gawo la Chinenero China
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Zimene Tingachite Tikapeza Mwininyumba Wolankhula Chinenero China
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Tizichita Zinthu Mogwirizana Tikamalalikira M’gawo la Zinenero Zambiri
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Muzifunafuna Anthu Olankhula Chinenero China
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
Onani Zambiri
Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
od mutu 9 tsamba 87-104

MUTU 9

Njira Zolalikirira Uthenga Wabwino

YESU anapereka chitsanzo chabwino kwa otsatira ake pa nkhani yolalikira uthenga wabwino mwakhama. Iye ankapita kunyumba za anthu komanso m’malo omwe munkapezeka anthu ambiri kuti akawauze uthenga wabwino wa Ufumu. (Mat. 9:35; 13:36; Luka 8:1) Yesu ankalalikira kwa anthu m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, ankatha kuphunzitsa munthu mmodzi payekha, kuphunzitsa ophunzira ake okha komanso kulalikira gulu lalikulu la anthu. (Maliko 4:10-13; 6:35-44; Yoh. 3:2-21) Ankagwiritsa ntchito mpata uliwonse kulankhula mawu olimbikitsa ndi opereka chiyembekezo kwa anthu. (Luka 4:16-19) Ankalalikira ngakhale pa nthawi imene ankafunikira kupuma. (Maliko 6:30-34; Yoh. 4:4-34) Atumwi ankafunitsitsa kumutsanzira. Nafenso tikamawerenga nkhani za m’Baibulo zokhudza utumiki wa Yesu, timafunitsitsa kumutsanzira.​—Mat. 4:19, 20; Luka 5:27, 28; Yoh. 1:43-45.

2 Tiyeni tione njira zimene Akhristu masiku ano amatsatira pogwira ntchito imene Yesu Khristu anaiyambitsa zaka pafupifupi 2,000 zapitazo.

KULALIKIRA KUNYUMBA NDI NYUMBA

3 Monga Mboni za Yehova, timazindikira kufunika kolalikira mwadongosolo uthenga wabwino wa Ufumu kunyumba ndi nyumba. Timagwiritsa ntchito kwambiri njira imeneyi polalikira uthenga wabwino moti yangokhala chizindikiro chathu. Kulalikira kunyumba ndi nyumba ndi njira yabwino kwambiri chifukwa imatithandiza kulalikira kwa anthu ambiri m’nthawi yochepa. (Mat. 11:19; 24:14) Imeneyinso ndi njira yosonyezera kuti timakonda Yehova ndi anthu anzathu.​—Mat. 22:34-40.

4 Kulalikira kunyumba ndi nyumba sikuti kwayamba ndi Mboni za Yehova za masiku ano. Mtumwi Paulo ananena kuti ankalalikira m’nyumba za anthu. Pofotokoza za utumiki wake kwa akulu a ku Efeso, iye anati: “Kuchokera tsiku loyamba limene ndinaponda m’chigawo cha Asia, . . . sindinakubisireni chilichonse chopindulitsa, ndipo sindinaleke kukuphunzitsani . . . kunyumba ndi nyumba.” (Mac. 20:18, 20, 21) Pogwiritsa ntchito njira imeneyi ndi njira zinanso, Paulo ‘anachitira umboni mokwanira kwa Ayuda ndi kwa Agiriki omwe, kuti alape ndi kutembenukira kwa Mulungu, komanso kuti akhale ndi chikhulupiriro mwa Ambuye wathu Yesu.’ (Mac. 20:18, 20, 21) Pa nthawi imeneyo olamulira achiroma ankalimbikitsa anthu kulambira mafano ndipo anthu ambiri ‘ankaopa kwambiri milungu.’ Choncho kunali kofunika kwambiri kuti anthu ayambe kufunafuna “Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemu,” yemwe pa nthawiyo ‘ankauza anthu kwina kulikonse kuti onse alape.’​—Mac. 17:22-31.

5 Masiku ano m’pofunika kulalikira uthenga wabwino mwamsanga kuposa kale chifukwa mapeto a dziko loipali ali pafupi kwambiri. Choncho tiyenera kuchita khama kwambiri pa ntchito yolalikira. Palibenso njira ina yabwino kwambiri yofufuzira anthu amene ali ndi njala ya choonadi kuposa yolalikira kunyumba ndi nyumba yomwe ndi njira imene yagwiritsidwa ntchito kwa nthawi yaitali. Mpaka pano njirayi ndi yothandiza kwambiri ngati mmene inalili m’nthawi ya Yesu ndi atumwi.​—Maliko 13:10.

6 Kodi inuyo nthawi zonse mumagwira nawo ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba? Ngati mumatero muyenera kudziwa kuti Yehova amasangalala ndi zimene mukuchita. (Ezek. 9:11; Mac. 20:35) Nthawi zina kulalikira kunyumba ndi nyumba kungakhale kovuta. Zimenezi zingachitike chifukwa cha matenda kapena chifukwa choti mumalalikira m’gawo limene anthu ambiri samvetsera uthenga wathu. Mwinanso mukukhala m’dziko limene boma linaletsa ntchito yolalikira kapena mumachita manyazi kuyamba kukambirana zinthu ndi anthu amene simukuwadziwa. Zimenezi zingachititse kuti nthawi zambiri muzikhala ndi nkhawa mukamafuna kukalalikira kunyumba ndi nyumba. Komabe simuyenera kutaya mtima. (Eks. 4:10-12) Ndipo muzikumbukira kuti zimene mukukumana nazo zikuchitikiranso abale anu m’madera ambiri.

7 Yesu analonjeza ophunzira ake kuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:20) Lonjezo limeneli limatilimbikitsa kwambiri tikamagwira ntchito yophunzitsa anthu. Timakhala ngati Paulo amene ananena kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afil. 4:13) Nthawi zonse mpingo ukakonza zoti tikalalikire kunyumba ndi nyumba, tiyenera kuyesetsa kupezekapo. Mukamalalikira ndi anthu ena, adzakulimbikitsani ndiponso adzakuthandizani kuti muzilalikira mogwira mtima. Muzipemphera kuti Mulungu akuthandizeni kulimbana ndi mavuto alionse amene mungakumane nawo komanso muziyesetsa kulalikira mwakhama uthenga wabwino.​—1 Yoh. 5:14.

8 Mukamauza anthu ena uthenga wabwino, mumakhala ndi mwayi wowafotokozera “chiyembekezo chimene muli nacho.” (1 Pet. 3:15) Komanso mungaone bwino kusiyana kwakukulu kumene kulipo pakati pa anthu amene amayembekezera Ufumu ndi amene alibe chiyembekezo. (Yes. 65:13, 14) Mumakhalanso osangalala podziwa kuti mukumvera lamulo la Yesu lakuti “onetsani kuwala kwanu” ndiponso mumakhala ndi mwayi wothandiza anthu kudziwa Yehova ndi choonadi chimene chingawathandize kuti adzapeze moyo wosatha.​—Mat. 5:16; Yoh. 17:3; 1 Tim. 4:16.

9 Kulalikira kunyumba ndi nyumba kumachitika Loweruka ndi Lamlungu komanso mkati mwa mlungu. M’madera amene kumakhala kovuta kupeza anthu pakhomo masana, mipingo ina imakonza zoti azilalikira madzulo. Ndipo amaona kuti anthu amawalandira bwino chifukwa ambiri amasangalala kulandira alendo masana kapena madzulo kusiyana ndi m’mawa.

KUFUFUZA ANTHU OYENERERA

10 Yesu analangiza ophunzira ake kuti ‘azifufuza’ anthu omwe ndi oyenerera. (Mat. 10:11) Pofufuza anthu oyenererawo, iye sankangolalikira kunyumba ndi nyumba kokha. Ankalalikira pa nthawi ili yonse ndipo nthawi zina ankalalikira kwa anthu amene wangokumana nawo iyeyo akuchita zinthu zina. (Luka 8:1; Yoh. 4:7-15) Atumwi nawonso ankalalikira m’malo osiyanasiyana.​—Mac. 17:17; 28:16, 23, 30, 31.

Cholinga chathu n’choti munthu aliyense amve uthenga wa Ufumu

11 Masiku anonso cholinga chathu n’choti munthu aliyense amve uthenga wa Ufumu. Kuti zimenezi zitheke tiyenera kutsanzira mmene Yesu ndi ophunzira ake ankachitira pogwira ntchito yolalikirayi. Tiyeneranso kuganizira mmene zinthu zikusinthira m’dzikoli komanso pa moyo wa anthu a m’gawo lathu. (1 Akor. 7:31) Mwachitsanzo,ofalitsa ena amalalikira m’malo a malonda ndipo zinthu zimawayendera bwino kwambiri. M’mayiko ambiri kulalikira mumsewu, m’malo oimika magalimoto komanso kulikonse komwe kumapezeka anthu, kwakhala ndi zotsatira zabwino. Mipingo ina imagwiritsa ntchito matebulo kapena timashelefu tamateyala polalikira. Komanso ofesi ya nthambi ingakhazikitse njira yapadera yolalikira m’malo opezeka anthu ambiri m’mizinda ikuluikulu ndipo imasankha anthu ochokera m’mipingo yosiyanasiyana kuti azilalikira pogwiritsa ntchito njira imeneyi. Njira zimenezi zimathandiza kuti anthu amene sapezeka pakhomo akhale ndi mwayi womva uthenga wabwino.

12 Tikakumana ndi anthu achidwi m’malo opezeka anthu ambiri, tikhoza kuwapatsa mabuku athu ogwirizana ndi anthuwo. Kuti tiwathandize kukhalabe ndi chidwi, tingawapatse dzina komanso nambala yathu ya foni n’kukonza zoti tidzachite ulendo wobwereza. Tikhozanso kuwasonyeza webusaiti ya jw.org, kapena kuwauza malo apafupi kumene misonkhano yampingo imachitikira. Ngati mukufuna kuwonjezera utumiki wanu, yesani kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri ndipo mudzasangalala kwambiri.

13 Komabe ntchito imene Akhristu apatsidwa si yongokambirana ndi anthu za uthenga wabwino kamodzi kokha. Kuti zinthu zitiyendere bwino pothandiza anthu kudziwa choonadi chomwe chingawathandize kudzapeza moyo wosatha, tiyenera kukambirana ndi anthuwo mobwerezabwereza kuti apite patsogolo n’kudzakhala Akhristu okhwima mwauzimu.

KUPANGA MAULENDO OBWEREZA

14 Yesu anauza otsatira ake kuti: “Mudzakhala mboni zanga . . . mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Koma anawauzanso kuti: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.” (Mat. 28:19, 20) Kubwerera kwa anthu omwe anasonyeza chidwi kungatithandize kuti tizisangalala potumikira Yehova. Nthawi zambiri anthu amene anasonyeza chidwi mutakumana nawo koyamba, angasangalale kukuonani mutabweranso kudzakambirana nawo uthenga wabwino. Kukambirana nawo mfundo zina za m’Baibulo kungawathandize kuti ayambe kukhulupirira kwambiri Mulungu komanso kuti azindikire zosowa zawo zauzimu. (Mat. 5:3) Ngati mwakonzekera bwino komanso ngati mwafika pa nthawi imene iwowo akuona kuti ndi yabwino, mukhoza kukhala ndi mwayi woyambitsa phunziro la Baibulo. Muzikhala ndi cholinga chimenechi mukamapanga maulendo obwereza. Sitiyenera kungodzala mbewu za choonadi n’kuzisiya. Tiyenera kumazithirira.​—1 Akor. 3:6.

15 Kupanga maulendo obwereza kungakhale kovuta kwa ena. N’kutheka kuti munazolowera kukambirana ndi anthu mwachidule uthenga wabwino ndipo kuchita zimenezi kumakusangalatsani. Koma mukaganizira zopitanso kwa munthuyo kuti mukakambirane naye mofatsa mfundo za m’Baibulo, mumaona kuti n’zovuta kwambiri. Koma ngati mutakonzekera bwino mukhoza kuona kuti mungakwanitse. Muzigwiritsa ntchito zimene timaphunzira pamsonkhano wa mkati mwa mlungu. Mukhozanso kupempha wofalitsa waluso kuti muyende naye limodzi.

KUCHITITSA MAPHUNZIRO A BAIBULO

16 Pamene ankalankhula ndi munthu wolowa Chiyuda yemwe ankawerenga Mawu a Mulungu, Filipo anam’funsa kuti: “Kodi mukumvetsa zimene mukuwerengazo?” Munthuyo anayankha kuti: “Ndingamvetse bwanji popanda wondimasulira?” Nkhani imeneyi yomwe imapezeka muchaputala 8 cha buku la Machitidwe, imasonyeza kuti kuyambira ndi lemba limene munthuyo ankawerenga, Filipo anamufotokozera “uthenga wabwino wonena za Yesu.” (Mac. 8:26-36) Sitikudziwa kuti Filipo anakambirana ndi munthuyo kwa nthawi yaitali bwanji, komabe anafotokoza uthenga wabwino mokwanira mpaka munthuyo anakhala wokhulupirira ndiponso anapempha kuti abatizidwe n’kukhala wophunzira wa Yesu Khristu.

17 Masiku ano anthu ambiri amene timawapeza tikamalalikira, amakhala oti salidziwa Baibulo kwenikweni. Choncho pangafunike kuphunzira nawo mobwerezabwereza ndipo zimenezi zingatenge milungu ingapo, miyezi, chaka ngakhalenso kuposa asanafike pokhala ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso kuyenerera kubatizidwa. Koma ngati mutayesetsa kuthandiza moleza mtima ndi mwachikondi anthu oona mtima amenewa kuti akhale ophunzira, mudzapeza madalitso mogwirizana ndi zimene Yesu ananena kuti: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”​—Mac. 20:35.

18 Mungachite bwino kuphunzira Baibulo ndi anthu pogwiritsa ntchito mabuku amene anakonzedwa kuti tizichititsira maphunziro. Mukamatsatira malangizo amene timalandira pamsonkhano wa mkati mwa mlungu komanso kuyenda ndi ofalitsa amene amaphunzitsa bwino, mungathe kumachititsa maphunziro a Baibulo ogwira mtima ndipo mungathandize anthu ena kuti akhale ophunzira a Yesu Khristu.

19 Ngati mukufuna kuthandizidwa mmene mungayambitsire komanso kuchititsa phunziro la Baibulo, mukhoza kupempha mkulu kapena wofalitsa wina amene ali ndi luso lochititsa maphunziro. Malangizo a mu Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu omwe amafotokozedwa bwino pamsonkhanowu, angakuthandizeninso kwambiri. Ndiponso muzipemphera ndi kudalira Yehova kuti akuthandizeni. (1 Yoh. 3:22) Choncho ngati n’kotheka, yesetsani kuti muzichititsa phunziro la Baibulo ngakhale limodzi lokha, kuwonjezera pa phunziro limene mumachita ndi banja lanu. Mukamachititsa maphunziro a Baibulo, mudzasangalala kwambiri ndi utumiki wanu.

KUTHANDIZA ANTHU ACHIDWI KUTI ADZIWE GULU LA YEHOVA

20 Anthu amene tawathandiza kudziwa Yehova Mulungu komanso kukhala ophunzira a Yesu Khristu, amabwera mu mpingo. Ophunzira Baibulo angapite patsogolo ngati timawathandiza kudziwa gulu la Yehova komanso kuwathandiza kuti azichita zinthu mogwirizana ndi gululo. Kuwaphunzitsa mmene angachitire zimenezi n’kofunika kwambiri. Zinthu monga mavidiyo komanso kabuku kakuti Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano? zinakonzedwa kuti zitithandize pokwaniritsa cholinga chimenechi. Mfundo zina zothandiza zikupezeka m’Mutu 4 wa bukuli.

21 Mukangoyamba kuphunzira Baibulo ndi munthu, muthandizeni kudziwa kuti Yehova ali ndi gulu limene akuligwiritsa ntchito polalikira padziko lonse lapansi. Mufotokozereni kufunika kwa zinthu zosiyanasiyana zimene timagwiritsa ntchito pophunzira Baibulo, mmene zimapangidwira ndiponso mmene zimatumizidwira m’madera osiyanasiyana padziko lonse lapansi. Ntchito imeneyi imagwiridwa ndi atumiki a Mulungu ongodzipereka. Mulimbikitseni kuti tsiku lina mudzapitire limodzi ku misonkhano ya ku Nyumba ya Ufumu. Mufotokozereni mmene misonkhano imachitikira komanso akabwera kumisonkhanoko, muthandizeni kuti adziwane ndi abale ndi alongo. Mungachitenso bwino kumuthandiza kuti adziwane ndi abale ndi alongo ena pa misonkhano ikuluikulu. Pa nthawi ya misonkhano komanso pa zochitika zina, muthandizeni kuti aone mmene atumiki a Yehova amasonyezera chikondi, womwe ndi umboni woti ndi Akhristu oona. (Yoh. 13:35) Munthu wachidwi akayamba kukonda gulu la Yehova, adzayesetsa kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehovayo.

KUGWIRITSA NTCHITO MABUKU OTHANDIZA POPHUNZIRA BAIBULO

22 Akhristu oyambirira ankafalitsa Mawu a Mulungu mwakhama. Ankakopera Malemba oti aziwerenga paokha komanso oti azigwiritsa ntchito pophunzira ndi mpingo. Ankalimbikitsanso ena kuti azikonda Mawu a Mulungu omwe ndi choonadi. Ankalemba zinthu zimenezi pamanja ndipo ankaziona kukhala za mtengo wapatali chifukwa zinali zochepa. (Akol. 4:16; 2 Tim. 2:15; 3:14-17; 4:13; 1 Pet. 1:1) Masiku ano, Mboni za Yehova zimagwiritsa ntchito njira zamakono pofalitsa mamiliyoni ambirimbiri a Mabaibulo komanso zinthu zothandiza pophunzira Baibulo. Zinthu zimenezi zikuphatikizapo timapepala, mabuku, magazini komanso zinthu zina zimene zimafalitsidwa m’zinenero zambirimbiri.

23 Mukamalalikira uthenga wabwino, onetsetsani kuti mukugwiritsa ntchito bwino zinthu zothandiza pophunzira Baibulo zomwe gulu la Yehova limapereka. Poona mmene mwapindulira chifukwa chowerenga ndi kuphunzira mabuku a Mboni za Yehova, nanunso mudzafunitsitsa kuuzako ena zimene mwaphunzirazo.​—Aheb. 13:15, 16.

24 Masiku ano anthu ambiri amagwiritsa ntchito intaneti pofufuza zinthu. Choncho kuwonjezera pa mabuku othandiza pophunzira Baibulo, njira ina yothandiza kwambiri pofalitsa uthenga wabwino ndi webusaiti yathu ya jw.org. Anthu padziko lonse angathe kuwerenga kapena kumvetsera nkhani za m’Baibulo ndi za m’mabuku othandiza pophunzira Baibulo m’zinenero zambirimbiri pogwiritsa ntchito kompyuta. Anthu amene amaopa kukambirana nafe kapena amene amakhala m’madera omwe n’zovuta kukambirana ndi Mboni za Yehova, amakhala ndi mwayi wofufuza zimene timakhulupirira pogwiritsa ntchito webusaiti yathu ya jw.org, ali m’nyumba zawo.

25 Poganizira zimenezi timayesetsa kufotokozera anthu ambiri za webusaiti imeneyi. Ngati munthu wafunsa zokhudza zimene timakhulupirira, tikhoza kumusonyeza yankho nthawi yomweyo pogwiritsa ntchito foni kapena kompyuta. Tikakumana ndi munthu amene amalankhula chinenero china, kuphatikizapo chamanja, tingamusonyeze webusaiti imeneyi. Pa webusaitiyi akhoza kuwerenga Baibulo ndiponso mabuku othandiza pophunzira Baibulo mu chinenero chake. Ofalitsa ambiri ayambitsa maphunziro a Baibulo pogwiritsa ntchito mavidiyo omwe ali pa webusaiti imeneyi.

KULALIKIRA MWAMWAYI

26 Yesu anauza anthu amene ankamvetsera zimene ankaphunzitsa kuti: “Inu ndinu kuwala kwa dziko. . . . Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wakumwamba.” (Mat. 5:14-16) Ophunzirawo ankasonyeza makhalidwe a Mulungu potengera chitsanzo cha Yesu, yemwe ananena kuti: “Ine ndine kuwala kwa dziko.” Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwa Akhristu chifukwa ankayesetsa kuti “kuwala kwa moyo” kuziwalira ndiponso kupindulitsa anthu onse amene ankamumvetsera.​—Yoh. 8:12.

27 Nayenso mtumwi Paulo ndi chitsanzo chabwino. (1 Akor. 4:16; 11:1) Ali ku Atene, tsiku lililonse ankalalikira kwa anthu amene ankawapeza pamsika. (Mac. 17:17) Akhristu a ku Filipi anatengera chitsanzo chake ndipo n’chifukwa chake Paulo anawalembera kuti mukukhala “pakati pa m’badwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhota, umene mukuwala pakati pawo monga zounikira.” (Afil. 2:15) Nafenso tikhoza kuthandiza kuti choonadi chonena za Ufumu chiwalire anthu kudzera m’zimene timalankhula komanso kuchita. Tingachite zimenezi nthawi iliyonse imene tapeza mwayi wofotokozera ena uthenga wabwino. N’zoona kuti chitsanzo chathu chabwino chochita zinthu moona mtima komanso kuyesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino chingapangitse anthu kuzindikira kuti ndife osiyana ndi dzikoli. Komabe ngati titawafotokozera uthenga wabwino akhoza kudziwa chifukwa chake timasiyana ndi dzikoli.

28 Anthu a Yehova ambiri amalalikira kwa anthu amene amakumana nawo kuntchito, kusukulu, akakhala pa ulendo, kapena amene amakumana nawo akamachita zinthu zina. Tikakhala pa ulendo tingakhale ndi mwayi wokambirana mfundo za m’Baibulo ndi anthu amene tayandikana nawo. Tonse tiyenera kukhala tcheru kuti tiziona mmene tingasinthire nkhani zimene tikucheza kuti tiyambe kulalikira. Tizikhala okonzeka kulalikira kwa anthu nthawi iliyonse imene mwayi wapezeka.

29 Tingamayesetse kuchita zimenezi ngati nthawi zonse timakumbukira kuti kuchita zimenezi kumalemekezetsa dzina la Mlengi wathu. Komanso tikhoza kuthandiza anthu oona mtima kudziwa Yehova kuti nawonso ayambe kumutumikira n’kukhala ndi chiyembekezo cha moyo chimene chimabwera chifukwa chokhulupirira Yesu Khristu. Yehova amasangalala tikamayesetsa kumutumikira ndipo amaona kuti zomwe tikuchitazo ndi utumiki wopatulika.​—Aheb. 12:28; Chiv. 7:9, 10.

GAWO

30 Yehova amafuna kuti uthenga wa Ufumu ulalikidwe padziko lonse, kaya ndi m’mizinda kapena m’midzi. Kuti zimenezi zitheke, ofesi ya nthambi imapatsa mipingo komanso anthu amene amatumikira m’madera akutali magawo oti azilalikira. (1 Akor. 14:40) Izi ndi zogwirizana ndi malangizo amene Mulungu anapereka kwa Akhristu oyambirira. (2 Akor. 10:13; Agal. 2:9) Ntchito ya Ufumu ikuwonjezeka kwambiri masiku otsiriza ano. Choncho, kuti ntchitoyi iyende bwino pamafunika kuti magawo agawidwe bwino.

31 Woyang’anira utumiki ndi amene amatsogolera ntchito yolalikira m’gawo la mpingo. Mtumiki wothandiza akhoza kumagwira ntchito yogawira anthu magawo. Pali magulu awiri a magawo, ena ndi a timagulu, pomwe ena amaperekedwa kwa munthu payekha. M’mipingo imene ili ndi gawo laling’ono, oyang’anira timagulu ndi amene amapatsidwa magawo oti ofalitsa a m’kagulu kawo azilalikiramo. Koma m’mipingo yomwe ili ndi gawo lalikulu, wofalitsa aliyense angathenso kupatsidwa gawo lakelake.

32 Wofalitsa amene ali ndi gawo lakelake sasowa kolalikira masiku amene kagulu kawo sikakhala ndi misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda kapena pamene sangathe kulowa limodzi mu utumiki ndi kagulu kawo. Mwachitsanzo, ofalitsa ena amapatsidwa gawo la kufupi ndi kuntchito kwawo ndipo amatha kulalikira m’gawolo pa nthawi yopuma kapena akaweruka. Mabanja ena amapempha gawo la kufupi ndi kumene amakhala n’cholinga choti azitha kulalikira ngakhale madzulo. Wofalitsa akakhala ndi gawo lomwe sangavutike kufikako, amatha kulalikira kwa nthawi yaitali m’malo moti nthawi izingothera kuyenda. Komabe, magulu a utumiki wakumunda angalalikirenso m’magawo amene anaperekedwa kwa ofalitsa. Ngati mukufuna kukhala ndi gawo lanulanu, mungapemphe kwa mtumiki wa magawo.

33 Woyang’anira kagulu amene wapatsidwa gawo la kagulu kake kapena wofalitsa amene ali ndi gawo lakelake, ayenera kuyesetsa kuti alalikire nyumba iliyonse m’gawolo. Dongosolo lolalikira m’gawo lonselo limene mungakonze liyenera kugwirizana ndi zimene malamulo a m’dziko lanulo amanena pa nkhani yosunga chinsinsi cha anthu ena. Woyang’anira kagulu aliyense kapena wofalitsa amene wapatsidwa gawo, ayenera kuyesetsa kulimaliza miyezi 4 isanathe. Akangomaliza kulalikira gawolo ayenera kudziwitsa mtumiki wa magawo. Mogwirizana ndi mmene zinthu zilili, woyang’anira kagulu kapena wofalitsa akhoza kusungabe gawolo kuti adzalalikiremonso kapena angalibweze kwa mtumiki wa magawo.

34 Aliyense mumpingo akamayesetsa kutsatira dongosolo limeneli, gawo la mpingowo limalalikidwa mokwanira. Zingathandizenso kuti anthu kapena magulu awiri asamalalikire m’gawo limodzi pa nthawi yofanana, zomwe zingakhumudwitse anthu a m’deralo. Tikamalalikira m’gawo limene tinapatsidwa timasonyeza kuti timaganizira abale athu komanso anthu a m’gawolo.

KULALIKIRA ANTHU AZINENERO ZONSE

35 Anthu onse akufunika kuphunzira za Yehova Mulungu, Mwana wake ndiponso Ufumu. (Chiv. 14:6, 7) Timafunitsitsa kuthandiza anthu azinenero zonse kuti aziitana pa dzina la Yehova kuti adzapulumuke ndiponso kuti aphunzire makhalidwe achikhristu. (Aroma 10:12, 13; Akol. 3:10, 11) Koma kodi pamakhala mavuto otani munthu akamalalikira m’dera limene anthu amalankhula zinenero zosiyanasiyana? Kodi tingalalikire bwanji m’madera amenewa m’njira yoti aliyense amve uthenga wa Ufumu m’chinenero chomwe angamve mosavuta?​—Aroma 10:14.

36 Magawo olalikiramo amagawidwa potengera chinenero cha mpingo. Choncho m’madera amene anthu amalankhula zinenero zosiyanasiyana, ofalitsa a m’mipingo yosiyana amalalikira m’dera limodzi. Zikatere ndi bwino kuti ofalitsa a mipingo yonse aziyesetsa kulalikira kwa anthu achinenero cha mpingo wawo okha. Njira imeneyi iyenera kutsatiridwanso pa nthawi yoitanira anthu kumisonkhano yosiyanasiyana. Koma pamene ofalitsa akulalikira m’malo opezeka anthu ambiri kapena kulalikira mwamwayi, angathe kulalikira kwa munthu aliyense komanso kugawira mabuku kapena magazini achinenero chilichonse.

37 Nthawi zina mipingo ya zinenero zina ingamalephere kulalikira pafupipafupi kugawo lawo lakutali. Zikatere, oyang’anira utumiki a m’mipingo imene imalalikira m’gawo limodzi ayenera kukambirana n’kugwirizana mmene angamalalikirire m’madera oterowo. Zimenezi zingathandize kuti aliyense akhale ndi mwayi womva uthenga wa Ufumu komanso zingathandize kuti magulu awiri asamalalikire m’gawolo nthawi imodzi.​—Miy. 15:22.

38 Tikakumana ndi munthu wachinenero china pamene tikulalikira, sitiyenera kungomusiya kuti mpaka ofalitsa a mpingo wa chinenero chake adzamupeze. Ofalitsa ena aphunzira ulaliki wachidule m’chinenero cha anthu amene nthawi zambiri amakumana nawo m’gawo lawo. Tingasonyeze munthuyo mmene angawerengere kapena kuchita dawunilodi mabuku ndi magazini a m’chinenero chake pa webusaiti yathu ya jw.org, kapenanso tingakonze zoti tizikamupatsa mabuku ndi magazini a chinenero chake.

39 Ngati munthu wasonyeza chidwi chenicheni, tiyenera kuyesetsa kupeza munthu woyenerera amene angamamuphunzitse mu chinenero chimene amamva. Tingamufotokozerenso kumene kuli mpingo wachinenero chake m’deralo. Ngati akufuna kuti munthu wina azimuphunzitsa m’chinenero chake, tingamusonyeze mmene angalembere adiresi yake ndi zinthu zina zofunikira pa webusaiti ya jw.org. Ofesi ya nthambi idzayesetsa kufufuza wofalitsa, kagulu kapena mpingo umene ungapitirize kumuthandiza.

40 Tiyenera kupitirizabe kuthandiza munthu wachinenero china mpaka patapezeka munthu wachinenero chake woti apitirize kuphunzira naye. Nthawi zina ofesi ya nthambi ingadziwitse akulu kuti kudera limene munthuyo amakhala kulibe ofalitsa amene amalankhula chinenero cha munthuyo. Zikatero, tiyenera kuyesetsa kupitiriza kumuthandiza kuti chidwi chake chisathe. Ngati n’kotheka tingamaphunzire naye Baibulo pogwiritsa ntchito mabuku a m’chinenero chake. Ngati titagwiritsa ntchito bwino zithunzi komanso kumulimbikitsa kuwerenga malemba omwe ali mu nkhaniyo, akhoza kumvetsa mfundo zofunika za m’Baibulo. Ngati m’banja lawo muli munthu amene amadziwa chinenero cha munthuyo komanso cha m’deralo, mukhoza kumupempha kuti azimasulira zimene mukukambirana.

41 Kuti munthu wachidwiyu adziwe gulu la Mulungu tiyenera kumuitanira ku misonkhano yathu ngakhale kuti mwina sangamamve zinthu zina. Pamene lemba likuwerengedwa, tingamuthandize kupeza lembalo m’Baibulo lachinenero chake ngati ali nalo. Kusonkhana ndi anthu ena mu mpingo pakokha kungamulimbikitse kupitiriza kupita patsogolo mwauzimu.

42 Timagulu. Kagulu kangakhazikitsidwe ngati pali ofalitsa angapo omwe amatha kulalikira m’chinenero china chosakhala cha mpingo womwe ali. Izi zingachitike ngakhale kuti palibe mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenerera amene angamachititse misonkhano mlungu uliwonse m’chinenerocho. Ofesi ya nthambi ingavomereze kuti mpingowo uzithandiza kaguluko ngati kakukwaniritsa mfundo zotsatirazi:

  1. (1) Ngati pali anthu ambiri amene amalankhula chinenerocho m’deralo.

  2. (2) Ngati pali ofalitsa angapo amene akudziwa kapena akuphunzira chinenerocho.

  3. (3) Ngati bungwe la akulu lili lokonzeka kutsogolera pokonza ndondomeko yogwirira ntchito yolalikira m’chinenerocho.

Ngati bungwe la akulu lili lokonzeka kuthandiza kagulu ka chinenerocho, akuluwo adzakambirana ndi woyang’anira dera. M’baleyo akhoza kukhala kuti akudziwa mipingo ina imene ikufunanso kumalalikira kwa anthu a chinenerocho ndipo akhoza kupereka malangizo omwe angathandize kudziwa mpingo umene uli woyenera kuthandiza kaguluko. Mpingowo ukasankhidwa, akulu ayenera kulemba kalata ku ofesi ya nthambi yopempha kuti aloledwe kuti aziyang’anira kagulu ka chinenero china.

43 Magulu: Ofesi ya nthambi ingavomereze mpingo kuti uzithandiza gulu la chinenero china ngati likukwaniritsa mfundo zotsatirazi:

  1. (1) Pali anthu ambiri achidwi olankhula chinenerocho ndipo zikuoneka kuti anthu ambiri angayambe kutumikira Yehova.

  2. (2) Pali ofalitsa angapo amene amadziwa chinenerocho kapena amene akufunitsitsa kuchiphunzira.

  3. (3) Pali mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenerera amene angamatsogolere pochititsa msonkhano ngakhale umodzi wokha mlungu uliwonse, monga nkhani ya onse kapena Phunziro la Nsanja ya Olonda m’chinenerocho.

Ngati mfundozi zikukwaniritsidwa, bungwe la akulu lingalembe kalata ku ofesi ya nthambi yofotokoza bwinobwino zimenezi, n’kupempha kuti aloledwe kuti aziyang’anira gulu la chinenerocho. Mkulu amene akutsogolera gululo amadziwika kuti “woyang’anira kagulu,” ngati ndi mtumiki wothandiza amadziwika kuti ndi “mtumiki wa kagulu.”

44 Gululo likakhazikitsidwa, bungwe la akulu la mpingo umene uzithandiza gululo limaona ngati angawonjezerenso mbali zina za misonkhano zoti zizichitika m’chinenerocho komanso kuti misonkhano ya chinenerocho izichitika kangati pa mwezi. Lingakonzenso kuti gululo lizichita misonkhano yokonzekera utumiki m’chinenero cha gululo. Anthu onse a m’gululo amayang’aniridwa ndi bungwe la akulu la mpingo umene umathandiza gululo. Akulu ayenera kupereka malangizo oyenerera mwamsanga ku gululo ngati patafunika kutero. Woyang’anira dera amachezeranso gululo pamene akuchezera mpingo umene umalithandiza ndipo amapereka lipoti lachidule ku ofesi ya nthambi lofotokoza mmene gululo likupitira patsogolo komanso ngati pali mavuto ena. M’kupita kwa nthawi gululo likhoza kuyenerera kukhala mpingo. Yehova amasangalala kwambiri anthu onse omwe akutumikira m’dera la chilankhulo chinacho akamayesetsa kutsatira malangizo a gulu.​—1 Akor. 1:10; 3:5, 6.

KULALIKIRA M’MAGULU

45 Mkhristu aliyense amene anadzipereka kwa Mulungu ali ndi udindo wouza ena uthenga wabwino. Pali njira zambiri zimene tingauzire ena uthenga wabwino, koma njira imene timaikonda kwambiri ndi yokalalikira limodzi ndi anthu ena. (Luka 10:1) Chifukwa cha zimenezi, mipingo imakumana kuti ikonzekere utumiki mkati mwa mlungu komanso Loweruka ndi Lamlungu. Masiku a holide amakhalanso nthawi yabwino kulalikira m’magulu chifukwa abale ambiri sapita kuntchito. Komiti ya Utumiki ya Mpingo imakonza misonkhano yokonzekera utumiki kuti izichitika pa nthawi ndi malo oyenera, m’mawa ndiponso chakumadzulo.

46 Kulalikira m’magulu kumathandiza ofalitsa kuti azilowera limodzi mu utumiki ‘n’kumalimbikitsana.’ (Aroma 1:12) Ofalitsa atsopano angayende limodzi ndi ofalitsa aluso amene akhala akulalikira kwa nthawi yaitali kuti aziwathandiza. Madera ena ndi oopsa moti pangafunike kuti ofalitsa awiri kapena angapo azilalikirira limodzi. Ngakhale tsiku limene mukufuna kuyenda nokha mu utumiki, mungalimbikitse ena ngati mutayamba mwapezeka kaye pa msonkhano wokonzekera utumiki. Kudziwa kuti enanso akulalikira m’dera lomwelo kungakulimbikitseni. Apainiya ndiponso anthu ena sayenera kukakamizika kupezeka pa misonkhano yonse yokonzekera utumiki, makamaka ngati misonkhanoyo imachitika tsiku lililonse. Komabe angachite bwino kuyesetsa kupezeka pa misonkhano ingapo mlungu uliwonse.

47 Tonsefe tiyenera kutsatira chitsanzo cha Yesu ndi atumwi ake. Tikamayesetsa kugwira ntchito yofunika kwambiri imeneyi yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu, tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzatidalitsa.​—Luka 9:57-62.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena