Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/12 tsamba 4-7
  • Muzifunafuna Anthu Olankhula Chinenero China

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzifunafuna Anthu Olankhula Chinenero China
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Yehova Wawalitsa Nkhope Yake pa Iwo’
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Muziona Kuti Abale ndi Alongo Anu Osamva Ndi Ofunika Kwambiri
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Chinenero Chochita Kuona ndi Maso!
    Galamukani!—1998
  • Kumvetsera ndi Maso Anu
    Galamukani!—1998
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
km 7/12 tsamba 4-7

Muzifunafuna Anthu Olankhula Chinenero China

1. N’chifukwa chiyani mipingo imagawiridwa magawo olalikira mogwirizana ndi chinenero chawo?

1 Pa Pentekosite mu 33 C.E., ophunzira a Yesu atalandira mzimu woyera, “anayamba kulankhula zinenero zosiyanasiyana” kwa anthu ochokera m’madera akutali. (Mac. 2:4) Chifukwa cha zimenezi, anthu pafupifupi 3,000 anabatizidwa. N’zochititsa chidwi kuti ambiri mwa anthu amene anabwera ku Yerusalemu ankatha kulankhula Chiheberi kapena Chigiriki. Koma Yehova anafuna kuti anthu amenewa amve uthenga wa Ufumu m’chinenero chawo. N’zosakayikitsa kuti Yehova anachita zimenezi chifukwa anthu amasangalala kumvetsera uthenga wabwino ukakhala kuti uli m’chinenero chawo. N’chifukwa chake masiku ano, mipingo imagawiridwa magawo olalikira mogwirizana ndi chinenero chawo. (Onani buku la Gulu tsamba 107, ndime 2 ndi 3) Timagulu ta chinenero china sitikhala ndi gawo lakelake lolalikirako, koma timalalikira m’gawo la mpingo wa m’deralo kwa anthu olankhula chinenero chawo.

2. (a) Kodi tingatani ngati m’gawo lathu muli anthu olankhula zinenero zosiyanasiyana? (b) Kodi mipingo ingathandizane bwanji polalikira m’gawo la anthu olankhula zinenero zosiyanasiyana? (c) Kodi tingatani ngati tapeza munthu wachidwi koma wa chinenero china?

2 Ngati mumakhala m’dera limene anthu ake amalankhula chinenero chimodzi, mukhoza kumangolalikira mosaganizira za chinenero. Koma sizingakhale choncho ngati mumakhala m’dera limene anthu ake amalankhula zinenero zosiyanasiyana, chifukwa n’kutheka kuti mipingo ya chinenero china ikhoza kumalalikiranso m’gawo lomwelo. Mipingo ya chinenero chosiyana ndi chanu ikhoza kukuuzani za anthu amene anawapeza olankhula chinenero chanu, koma inuyo ndi amene muli ndi udindo wofunafuna anthu olankhula chinenero chanuwo. (Onani bokosi lakuti, “Muzithandizana.”) Choncho, mungafunike kufunafuna anthu amene amalankhula chinenero chanu. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

3. Kodi muyenera kuthera nthawi yaitali bwanji pofufuza anthu olankhula chinenero chanu, ndipo mungawafufuze kuti?

3 Ntchito Yofufuza Anthu Olankhula Chinenero China: Nthawi imene mungathere kufufuza anthu olankhula chinenero china ingadalire mmene zinthu zilili m’gawolo. Mwachitsanzo, kodi m’gawo lanu muli anthu angati olankhula chinenero chanu? Kodi muli ndi ofalitsa angati? Kodi mpingo kapena gulu lanu lili ndi mayina angati a anthu amene mukudziwa kuti amalankhula chinenero chanu? Sikuti mpingo wanu ufunika kufufuza paliponse, koma ungasankhe m’madera okhala anthu ambiri a m’gawo lanu. Komabe, ntchito yofufuzayi iyenera kuchitidwa mwadongosolo n’cholinga chakuti anthu ambiri apeze mwayi woitanira pa dzina la Yehova.—Aroma 10:13, 14.

4. (a) Kodi ntchito yofufuza iyenera kuchitidwa bwanji? (b) Kodi ndi njira zina ziti zimene mungatsatire pofufuza anthu olankhula chinenero chanu?

4 Pofuna kuti zinthu zichitike mwadongosolo, bungwe la akulu, makamaka woyang’anira utumiki, ndi amene ayenera kuyang’anira ntchito yofufuzayi. (1 Akor. 9:26) M’madera amene muli timagulu tolankhula chinenero chakunja, mkulu kapena mtumiki wothandiza, amene bungwe la akulu la mpingo umene umayang’anira kaguluko linamusankha, ndi amene ayenera kutsogolera pa ntchitoyi. Anthu a m’magulu ena ndiponso mipingo amakonzekera kaye asanayambe kufufuza. Iwo amagwiritsa ntchito buku la manambala a telefoni kapena Intaneti kuti adziwe mayina a anthu amene amalankhula chinenero chawo omwe ali m’gawo lawo. Kenako amayamba kuimbira anthu mafoni kapena kupita kumene anthuwo amakhala n’cholinga choti awaike m’gulu la anthu amene aziwayendera. Ngati mukuona kuti njira imeneyi ndi yothandiza, bungwe la akulu la mpingo umene umayang’anira kagulu, lingakonze zoti nthawi zina mpingo wonse uzigwira nawo ntchito yofufuzayi.—Onani bokosi lakuti, “Kodi Mungafufuze Bwanji Anthu Olankhula Chinenero Chanu?”

5. (a) Kodi ofalitsa amene akugwira ntchito yofufuza angatsatire malangizo ati? (b) Kodi tinganene chiyani pofufuza anthu olankhula chinenero chathu?

5 Nthawi zonse pamene tikugwira nawo ntchito yofufuzayi, tiyenera kukhala ndi cholinga. Popeza kuti ntchitoyi ndi mbali ya utumiki wathu, tiyenera kuvala ngati mmene timavalira tikamalalikira. Ena amaona kuti kukonzekera mawu omwe angakanene komanso kulankhula chinenero chawo pa nthawi yofufuzayi kumawathandiza kuti alalikire mogwira mtima. Tikhoza kuwerengera nthawi imene tathera pofufuza anthu achinenero chathu, koma sitiyenera kuwerengera nthawi yomwe tathera polemba mapu komanso polemba mayina a anthu amene tikuwafufuza. Tikapeza munthu amene amalankhula chinenero chathu, tiyenera kumuuza uthenga wabwino kenako tiyenera kuuza woyang’anira utumiki kapena wina aliyense amene anasankhidwa kuti alembe zimenezo m’mafaelo a magawo. Ayenera kuchita zimenezi kaya munthuyo anasonyeza chidwi kapena ayi. Ngakhale kuti ntchito yofufuzayi ndi yofunika kwambiri, tiyenera kuchita nawo mbali zonse za utumiki wathu.—Onani bokosi lakuti, “Zimene Munganene Pofufuza Anthu Olankhula Chinenero Chanu.”

6. N’chifukwa chiyani ntchito yofufuza ogontha ili yovuta kwambiri?

6 Kufufuza ogontha: Ntchito yofufuza anthu ogontha ndi yovuta ndipo imafunika khama komanso kudzipereka. Simungadziwe kuti munthuyu ndi wogontha pongoona mmene akuonekera, mmene wavalira kapena mmene amalembera dzina lake. Komanso, achibale kapena azinzake akhoza kumabisa kapena kunyalanyaza kuti akuthandizeni kupeza munthuyo. Mfundo zotsatirazi zingathandize kufunafuna anthu ogontha komanso zingathandize pofunafuna anthu olankhula chinenero china.

7. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene mungafunse anthu a m’dera lanu pofufuza ogontha? (b) Kodi tingatani kuti anthu amene tikuwafunsawo asatikayikire?

7 Mipingo kapena magulu a chinenero chamanja akhala akupeza anthu ogontha pofunsa anthu okhala m’gawolo. N’kutheka kuti munthu wina akhoza kuona mnzake woyandikana naye nyumba, amene amagwira naye ntchito kapena mnzake wakusukulu akulankhula chinenero chamanja, kapena angaone chikwangwani cha mumsewu chochenjeza madalaivala kuti m’deralo muli ana ogontha. Komanso n’kutheka kuti ali ndi wachibale wake yemwe ndi wogontha. Nthawi zonse muzikumbukira kuti anthu ena angakayikire cholinga chanu pofufuza anthu ogontha. Komabe, mukhoza kuyesetsa kuchita zinthu zoti anthu asamakuopeni kwambiri. Mungachite zimenezi powalankhula mwansangala, mwaulemu, moona mtima komanso mwachidule. Ena amaona kuti zimawathandiza kunyamula m’manja Baibulo kapena DVD ya chinenero chamanja akamafunsa anthu ngati akudziwa aliyense wogontha. Kenako amawauza anthuwo kuti cholinga chawo akufuna kuthandiza anthu ogonthawo kuti aphunzire Baibulo. Ngati munthuyo sakufuna kukuuzani za munthu wogontha amene akumudziwa, mwina angalole kulandira kapepala koitanira wogonthayo kumisonkhano.

8. Kodi mpingo wapafupi ungathandize bwanji mpingo wa chinenero chamanja?

8 Ngati mpingo wa chinenero chamanja uli ndi gawo lalikulu, mpingowo ungapemphe mpingo wapafupi wa chinenero china kuti uziwathandiza kufufuza ogontha m’dera lawo, kamodzi kapena kawiri pachaka. Pokonzekera ntchito imeneyi, mpingo wa chinenero chamanja ungapereke malangizo komanso kuchita chitsanzo chosonyeza mmene angagwirire ntchitoyi. Gulu lililonse lingakhale ndi wofalitsa mmodzi wa mpingo wa chinenero chamanja ndipo akhale ndi mapu osonyeza dera limene akuyenera kukafufuza.

9. Kodi tingafufuze bwanji anthu ogontha kumalo amene amakonda kucheza kapena kulandilirako chithandizo?

9 Mungakafufuzenso kumene anthu ogontha amakonda kucheza kapena kumene amakalandirako chithandizo. Ofalitsa ayenera kuvala mwaulemu, mogwirizana ndi kumalo kumene akupitako. Mukafika, mungachite bwino kulankhula ndi munthu mmodzi kapena awiri m’malo molankhula ndi chigulu chonse nthawi imodzi. Ngati anthuwo alola kuti mukambirane, mungawapemphe kuti akuuzeni kumene amakhala komanso mayina awo.

10. Kodi ofalitsa angafufuze bwanji anthu ogontha m’malo a bizinezi?

10 Njira ina yofufuzira ndi kulemba mapu a malo ochitira malonda kenako n’kupitako nthawi yoyenera. Mapu ena angasonyeze malo angapo omwe magalimoto amakathira mafuta, pomwe ena angasonyeze malo ena a bizinezi ngati malesitanti ndi mahotela. Ngati mapu onse akusonyeza malo omwe anthu amachitira bizinezi yofanana, ofalitsa angagwiritse ntchito malangizo ofanana komanso angapeze luso lina akamagwira ntchitoyi. Nthawi zina anthu ogontha amagona m’mahotela ndipo tikhoza kulankhula mwachidule ndi wolandira alendo n’kumupatsa ma DVD angapo komanso timapepala toitanira kumisonkhano kuti apereke kwa ogonthawo. M’malo ena ochitira malonda tingangofunsa ngati pali ogwira ntchito kapena makasitomala amene amalankhula chinenero cha manja. Ngati m’dera lanu muli sukulu ya anthu ogontha, mungakapereke ma DVD kuti aike mu laibulale yawo.

11. N’chifukwa chiyani ntchito yofufuza anthu a chinenero chathu ili yofunika kwambiri?

11 Ntchito Yofunika Kwambiri: Kunena zoona, ntchito yofufuza anthu olankhula chinenero chanu m’magawo a chinenero china imafuna khama ndiponso nthawi yambiri. Komanso chifukwa cha kusamukasamuka kwa anthu zingakhale zovuta kusunga maadiresi olondola m’faelo ya gawo. Komabe, m’madera ambiri ntchito yofufuza anthu a chinenero china ikuthandiza kwambiri. Dziwani kuti Yehova, yemwe watipatsa ntchito yolalikirayi, ndi wopanda tsankho. (Mac. 10:34) Ndipo “chifuniro chake n’chakuti anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:3, 4) Choncho, tiyeni timvere Yehova komanso kuchita zinthu mothandizana ndi Akhristu anzathu pa ntchito yofufuza anthu a zinenero zonse omwe ali ndi “mtima woona komanso wabwino.”—Luka 8:15.

[Bokosi patsamba 5]

Muzithandizana

Woyang’anira dera adzadziwitsa mpingo wanu za mipingo kapena magulu a chinenero china amene ali m’dera lanu. Mukakhala mu utumiki, n’kupeza munthu wachidwi wa chinenero china, muyenera kulemba adiresi komanso chinenero chake. Ngati n’zotheka mungalembenso dzina lake n’kuzipereka kwa woyang’anira utumiki kapena aliyense amene anasankhidwa kuti aziyang’anira zimenezi. Woyang’anira utumikiyo ayenera kulemba munthuyo pamndandanda wa anthu a chinenero china. Ngati gulu kapena mpingo wa chinenero chimenecho utafunsa ngati mwapeza anthu olankhula chinenero chawo, mungawapatse mayinawo. Abale oyang’anira utumiki m’mipingo iwiriyi angakonze dongosolo labwino lolalikirira komanso lothandizira anthu achidwi. Ngati mwapeza munthu wachidwi wa chinenero china (kapena wogontha), muzilemba fomu yakuti Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu (S-43) mwamsanga n’kukaipereka kwa mlembi. Zimenezi zidzathandiza kuti munthuyo athandizidwe mwamsanga.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 2011, tsamba 3.

[Bokosi patsamba 6]

Kodi Mungafufuze Bwanji Anthu Olankhula Chinenero Chanu?

• Muzifunsa anthu ena monga amene mumaphunzira nawo Baibulo, achibale anu kapena anzanu akuntchito.

• Muzigwiritsa ntchito buku la manambala a telefoni kuti mupeze mayina a anthu a chinenero chanu. Mabuku ena a manambala a telefoni amasonyeza dzina komanso adiresi ya kumene munthuyo amakhala. Mabuku amenewa mungawapeze pa Intaneti kapena kukampani ya matelefoni.

• Mukhoza kufufuza mwanzeru malo ngati kulaibulale, maofesi a boma komanso m’makoleji.

• Muziyang’ana m’nyuzipepala kuti mudziwe ngati kuli msonkhano uliwonse wa anthu olankhula chinenero chakunja.

• Mungafufuze m’mashopu komanso m’malo a bizinezi omwe anthu olankhula chinenero chakunja amakonda kupitako.

• Mungapemphe kuti akuloleni kuti mukhale ndi malo amene mungaikepo mabuku athu kumalo a bizinezi, kumene ana asukulu amakonda kupita kapenanso pamalo ena ngati kokwerera basi kapena ndege, kumene anthu olankhula chinenero chakunja amapezeka.

• Ngati n’zololeka m’dziko lanu, mungagule pulogalamu ya pakompyuta imene imatha kufufuza malo a pa Intaneti omwe anthu amakonda kupitapo.

[Bokosi patsamba 7]

Zimene Munganene Pofufuza Anthu Olankhula Chinenero Chanu

Kulankhula anthu mwansangala, mwaulemu, moona mtima komanso mwachidule kungathandize kuti asakukayikireni. Nthawi zina ndi bwino kuwasonyeza mabuku a chinenero chanu.

Pambuyo powapatsa moni munganene kuti: “Tikufufuza anthu omwe amalankhula chinenero cha ․․․․․ kuti tikambirane nawo zimene Baibulo limalonjeza. Kodi mukudziwa aliyense amene amalankhula chinenero chimenechi?”

Mukamafufuza anthu ogontha munganene kuti: “Muli bwanji? Ndimafuna ndikusonyezeniko zinazake. [Pogwiritsa ntchito wailesi ya DVD ya m’manja, asonyezeni ndime imodzi m’kabuku kakuti Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu.] Zimene takusonyezanizi zili mu DVD yofotokoza nkhani za m’Baibulo ya chinenero chamanja cha ku America. Tilinso ndi ma DVD ena omwe sitilipiritsa ndipo cholinga chake ndi kuthandiza anthu ogontha kuti aphunzire Baibulo. Kodi mukudziwa aliyense amene ndi wogontha kapena amavutika kumva ndipo amalankhula chinenero chamanja?” Ngati mwininyumbayo sakukumbukira kalikonse, mungachite bwino kumufunsa za malo amene mwina anaonapo anthu ogontha. Malo amenewa ndi monga kuntchito, kusukulu kapena kumene amakhala.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena