Ndandanda ya Mlungu wa July 30
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 30
Nyimbo Na. 78 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 9 ndime 19-24 ndi bokosi patsamba 73 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 21–23 (Mph. 10)
Na. 1: Ezekieli 23:35-45 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Chikondi cha Mulungu N’chachikulu Bwanji?—Yoh. 3:16; Aroma 8:38, 39 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Ndi Malemba Ati Omwe Amachititsa Kuti Akhristu Asamamenye Nawo Nkhondo?—rs tsa. 369 ndime 3 mpaka tsa. 370 ndime 1 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 8, chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo, Loweruka loyambirira m’mwezi wa August.
Mph. 25: “Muzifunafuna Anthu Olankhula Chinenero China.” Mafunso ndi mayankho, ndipo ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Fotokozani mmene mungagwiritsire ntchito mfundozo m’dera lanu. Ngati mpingo wanu uli ndi kagulu ka chinenero china kapena ngati umafunikira kufufuza anthu olankhula chinenero cha mpingowo, mukamakambirana ndime yachisanu chitani chitsanzo chosonyeza zimene munganene pofufuza anthuwo.
Nyimbo Na. 92 ndi Pemphero