Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/09 tsamba 3-5
  • Kukhazikitsa Gawo la Chinenero China

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukhazikitsa Gawo la Chinenero China
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Tingachite Tikapeza Mwininyumba Wolankhula Chinenero China
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzilalikira Anthu Oyankhula Chinenero China
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Njira Zolalikirira Uthenga Wabwino
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Kodi Mumalankhula Bwino “Chinenero Choyera”?
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 11/09 tsamba 3-5

Kukhazikitsa Gawo la Chinenero China

1. Kodi ndi mwayi wotani umene wayamba kupezeka tikamalalikira m’gawo la mpingo wathu?

1 Yesu Khristu analosera kuti uthenga wabwino udzalalikidwa padziko lonse lapansi “kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.” Mtumiki aliyense amene amagwira ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira amadziwa kuti mawu a Yesu amenewa ndi ofunika kwambiri. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Tikamalalikira ndi kupanga ophunzira, tingapeze anthu ochokera m’mayiko ena olankhula chinenero chosiyana ndi chathu. Anthu amenewanso ndi oyenera kupatsidwa mwayi woti amve uthenga wa Ufumu ndi kukhulupirira choonadi tsiku loopsa la Yehova lisanafike. (Mal. 3:18) Kodi tingakhazikitse bwanji gawo la chinenero china m’gawo la mpingo wathu?

2. Kodi timatsanzira Yehova m’njira iti tikamalalikira anthu a chinenero china?

2 Muziona Anthu a Chinenero China Mmene Yehova Amawaonera: Kuti tisonyeze kuti timakonda munthu aliyense wa m’gawo lathu mosakondera monga mmene Yehova amachitira, tiyenera kukhala ofunitsitsa kuthandiza anthu a chinenero china chilichonse kuti adziwe Mulungu woona, Yehova molondola. (Sal. 83:18; Mac. 10:34, 35) Ngakhale kuti tikamalalikira, maganizo athu amakhala kwa anthu amene amalankhula chinenero chimene mpingo wathu umagwiritsa ntchito, tiyeneranso kuganizira anthu amene amalankhula chinenero china ndi kufufuza njira zimene tingawauzire uthenga wa Ufumu wa Mulungu. Kunyalanyaza anthu a chinenero china n’kosagwirizana ndi cholinga cha Yehova chakuti anthu a mitundu yonse amve uthenga wa Ufumu. Ndiyeno, tingawathandize bwanji anthu a chinenero china?

3. Kodi tili ndi kabuku kati kotithandiza, ndipo tingatani kuti tizikagwiritsa ntchito?

3 Gwiritsirani Ntchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse: Kabuku kameneka kanakonzedwa kuti tizikagwiritsira ntchito tikakumana ndi anthu a chinenero chosiyana ndi chathu. Muziyenda ndi kabuku kameneka nthawi zonse, mudziwe zimene zili m’kabukuka, ndipo muzikhala okonzeka kukagwiritsira ntchito. Kuti musamavutike kupeza pamene mukufuna, ikani zizindikiro pamene pali zinenero zimene zimalankhulidwa ndi anthu omwe mumakumana nawo m’gawo lanu. Ngati mabuku a m’zinenero zimenezi alipo, mwina zingakhale bwino kupeza ochepa oti muzigawira munthu amene mwakambirana naye uthenga umene uli m’kabukuka.

4. Kodi tingagwiritse ntchito motani kabuku ka Mitundu pamene tili mu utumiki?

4 Mukakumana ndi munthu mu utumiki wolankhula chinenero chimene simukuchidziwa, muonetseni kaye chikuto cha kabukuka. Kenako muonetseni mapu a dziko lonse amene ali mkati mwa kabukuka kuchikuto, dzilozeni nokha, lozani dziko limene mumakhala, ndipo sonyezani ndi manja kuti mukufuna kudziwa dziko limene mwininyumbayo anachokera ndiponso chinenero chimene amalankhula. Mukadziwa chinenero chake, pitani pa za m’katimu, pezani tsamba loyenera, sonyezani mwininyumbayo chiganizo cholembedwa m’zilembo zakuda kwambiri pamwamba pa tsambalo, ndipo mumuuze ndi manja kuti awerenge uthengawo. Mwininyumbayo akamaliza, m’patseni kapepala ka m’chinenero chake kapena m’sonyezeni chiganizo chimene achidetsa ndi inki yotuwacho, chimene chikunena zoti mukhoza kudzamubweretsera buku la m’chinenero chake. Ndiyeno lozani mawu akuti “dzina langa” amene ali m’zilembo zakuda kwambiri, ndipo tchulani dzina lanu momveka bwino. Kenako lozani mawu akuti “dzina lanu” amene ali m’zilembo zakuda kwambiri, ndipo dikirani kuti ayankhe. Tsimikiziranani zoti mudzabweranso.

5. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tithandize moyenerera anthu a chinenero china amene achita chidwi ndi uthenga wa Ufumu?

5 Dongosolo Lothandiza Achidwi: Tiyenera kuchita chilichonse chimene tingathe kuti tiyendere anthu a chinenero chilichonse amene achita chidwi ndi uthenga wa Ufumu. Tikadziwa kuti munthuyo akufuna kudziwa za Mulungu ndi Mawu ake, Baibulo, tiyenera kudzaza fomu yakuti Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu (S-43) ndi kuipereka mwansanga kwa mlembi wa mpingo kuti iye aitumize ku ofesi ya nthambi. Cholinga chochitira zonsezi n’chakuti munthu wachidwiyo adzayenderedwe ndi munthu wodziwa chinenero chake. Zikatero, a ku ofesi ya nthambi adzatumiza fomuyi kumene kuli kagulu kamene kamalankhula chinenero cha munthu wachidwiyo. Fomuyi ikafika kumeneko, munthu wachidwiyo adzayenderedwa mwansanga. Mlembi angapereke kope la fomuyi kwa woyang’anira utumiki kuti adziwe za anthu achinenero china amene akusonyeza chidwi. Muyenera kugwiritsira ntchito fomu imeneyi pokhapokha ngati mwapeza munthu amene alidi ndi chidwi.

6. Kodi tiyenera kuchita chiyani tikakumana ndi munthu wachidwi wa chinenero china?

6 Kuchokera pa nthawi imene munthu angapereke fomu ya S-43 mpaka kufika poti munthu wachidwi adzayenderedwe, nthawi ingadutse ndithu. Choncho, pofuna kuthandiza kuti chidwi cha munthuyo chisathe, wofalitsa amene watumiza fomu ya S-43 angathe kumamuthandizabe mpaka atayenderedwa ndi wofalitsa wodziwa chinenero chake. Nthawi zina, zingatheke kumachita phunziro la Baibulo ndi munthu wachidwiyo. Koma kodi wofalitsa angatani kuti azipeza mabuku a m’chinenero cha munthuyo pa nthawi yoyembekezera kuti wofalitsa wodziwa chinenerocho afike kwa munthu wachidwiyo?

7. Kodi pali makonzedwe otani otithandiza kupeza mabuku a zinenero za anthu amene tingakumane nawo?

7 Mabuku a Zinenero Zina: Mipingo siyenera kusunga mabuku a zinenero zina ochuluka. Komabe, ngati woyang’anira utumiki watsimikizira kuti pali anthu a chinenero china amene akuchita chidwi ndi choonadi, angasankhe zosunga mabuku ochepa a chinenerocho kuti ofalitsa azigwiritsa ntchito. Ngati mpingo ulibe mabuku a chinenerocho, ungaitanitse. Nthawi yaitali ingadutse kuti mabuku a chinenero china afike. Choncho, n’zotheka kupurinta mabukuwa kuchokera pa malo athu a pa Intaneti, omwe adiresi yake ndi www.jw.org. Pa malo amenewa pali mabuku ambiri a m’zinenero zambiri ndipo wofalitsa kapena munthu wachidwi angathe kuwapeza mwansanga. Tikukhulupirira kuti makonzedwe amenewa ndi othandiza kwambiri pofuna kuthandiza anthu achidwi a zinenero zina.

8. Kodi mpingo uli ndi udindo wotani polimbikitsa anthu a chinenero china amene asonyeza chidwi?

8 Udindo wa Mpingo: Nthawi zina, zingachitike kuti anthu achinenero china akuchuluka m’dera lina, koma palibe mpingo wapafupi umene umachita misonkhano yawo m’chinenerocho. Choncho, muyenera kuitanira kumisonkhano yanu anthu achidwi a chinenerocho. Kuwalandira mwansangala kungawalimbikitse kuti azisonkhana mokhazikika. Poyamba, zingakhale zovuta chifukwa cha kusiyana kwa chinenero ndiponso chikhalidwe, komabe chikondi chenicheni chachikhristu chimene chimapezeka m’gulu lapadziko lonse la Mboni za Yehova chilibe malire. (Zef. 3:9; Yoh. 13:35) Kodi mumadziwa kulankhula bwino chinenero china? Ngati mumadziwa ndipo mukufunitsitsa kumapita kwa anthu achidwi olankhula chinenerocho, dziwitsani mlembi wa mpingo wanu kuti adziwitse a ku ofesi ya nthambi. Kuchita zimenezi ndi kothandiza ngati a ku ofesi ya nthambi akufunafuna wofalitsa amene angakalimbikitse munthu wachidwi wa chinenerocho.

9. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingapangitse kuti kukhale koyenera kukhazikitsa kalasi yophunzitsa chinenero, ndipo kodi ziyenera kuchitidwa motani?

9 Kalasi Yophunzitsa Chinenero: Mukamathandiza anthu a chinenero china, ndi bwino kuwalimbikitsa kuti ngati angakwanitse azikachita misonkhano ndi mpingo umene umagwiritsira ntchito chinenero chawo. Komabe, ngati sangakwanitse kuchita zimenezi, ofalitsa ena angasankhe kuphunzira chinenerocho kuti athandize bwino anthu achidwiwo. Ngati palibe mpingo wa chinenerocho pafupi, a ku ofesi ya nthambi angasankhe kukhazikitsa kalasi yophunzitsa chinenerocho chifukwa pali anthu ambiri obwera kapena nzika za m’deralo zolankhula chinenerocho. Ngati zinthu zili chonchi, a ku ofesi ya nthambi angadziwitse mipingo yozungulira derali za kusowa kumene kulipo, ndipo angakonze zoti pakhale chilengezo chofotokoza za kalasi yophunzitsa chinenero. Amene angalembetse kuti alowe m’kalasi limeneli ayenera kukhala ndi cholinga chosamukira ku kagulu kapena mpingo wa chinenerochi kuti athandize kukhazikitsa gawo la chinenerocho.

10. Kodi kagulu ka chinenero china kangakhazikitsidwe ngati pakwaniritsidwa zinthu zofunikira ziti?

10 Kukhazikitsa Kagulu ka Chinenero China: Kagulu kachinenero china kangakhazikitsidwe ngati zinthu zinayi zofunikira zitakwaniritsidwa. Zinthu zake ndi izi: (1) Anthu achidwi olankhula chinenerocho ayenera akhalepo ambiri. (2) Payenera kukhala ofalitsa ochulukirapo odziwa kapena amene akuphunzira chinenerocho. (3) Payenera kukhala mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenerera amene angathe kutsogolera ndi kuchititsa msonkhano umodzi kapena ingapo ya mpingo m’chinenerocho. (4) Bungwe la akulu liyenera kukhala lofunitsitsa kuthandiza kaguluko. Zinthu zimenezi zikakwaniritsidwa pafupifupi zonse, bungwe la akulu lingalembere a ku ofesi ya nthambi kalata yofotokoza za kaguluka, ndipo liyenera kupempha kuti mpingo wawo uzidziwika kuti ndi umene ukuthandiza kagulu ka chinenero china. (Onani m’buku la Gulu, masamba 106 ndi 107.) Mkulu kapena mtumiki wothandiza amene akutsogolera kaguluka azionedwa kuti ndiye “woyang’anira kagulu” kapena “mtumiki wa kagulu” wosamalira kagulu ka chinenero china.

11. N’chifukwa chiyani ndi mwayi waukulu kukhazikitsa gawo la chinenero china m’gawo la mpingo wathu?

11 Kukhazikitsa gawo la chinenero china m’gawo la mpingo wathu ndi mbali yofunika kwambiri ya ntchito yathu yapadziko lonse yolalikira imene inayambitsidwa ndi Yesu Khristu, yemwe ndi chitsanzo chathu. Tiyeni tichite mbali yathu mwakhama ndi kuona mmene Yehova akupitirizira kugwedeza mitundu ya anthu ndi kubweretsa m’gulu lake anthu amene iye akuwaona kuti ndi amtengo wapatali. (Hag. 2:7) Kuchita nawo zonse zimene tingathe kuti zimenezi zitheke n’kosangalatsa kwambiri. Tikupempha Yehova kuti adalitse zonse zimene tikuchita mogwirizana kuti tikhazikitse magawo a zinenero zina m’magawo a mipingo yathu podziwa kuti Mulungu angathe kuwakulitsa ngakhale patakhala vuto la chinenero cha anthu.—1 Akor. 3:6-9.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena