Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzilalikira Anthu Oyankhula Chinenero China
N’chifukwa Chiyani Kuchita Zimenezi N’kofunika? Yehova amafuna kuti anthu ‘ochokera mu mtundu uliwonse’ aphunzire za iye. (Mac. 10:34, 35) Komanso Yesu ananena kuti uthenga wabwino uyenera kulalikidwa “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu” ndiponso “ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14) Zekariya nayenso analosera kuti anthu “ochokera m’zilankhulo zonse” adzayamba kulambira Yehova. (Zek. 8:23) Komanso masomphenya amene mtumwi Yohane anaona amasonyeza kuti anthu amene adzapulumuke pa chisautso chachikulu, adzakhala ochokera “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.” (Chiv. 7:9, 13, 14) Choncho, tikamalalikira n’kukumana ndi munthu woyankhula chinenero china, tiziyesetsa kumulalikira.
Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno:
Pa Kulambira kwa Pabanja yesererani mmene mungalalikirire munthu woyankhula chinenero china.