Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb21 January tsamba 13
  • N’zotheka Kulalikira kwa Aliyense

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’zotheka Kulalikira kwa Aliyense
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzilalikira Anthu Oyankhula Chinenero China
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Kukhazikitsa Gawo la Chinenero China
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Muzilalikira Munthu Aliyense wa M’gawo Lanu
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Tizichita Zinthu Mogwirizana Tikamalalikira M’gawo la Zinenero Zambiri
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21 January tsamba 13
M’bale akugwiritsa ntchito pulogalamu ya ‘JW Language’ patabuleti yake.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

N’zotheka Kulalikira kwa Aliyense

Mofanana ndi mmene Yehova ankathandizira Aisiraeli, masiku anonso iye akuthandiza anthu ake kuti azichita chifuniro chake. Padziko lonse maofesi a nthambi, madera, mipingo komanso magulu a utumiki amagwira ntchito mogwirizana kuti uthenga wabwino uzilalikidwa. Timalalikira kwa aliyense ngakhalenso anthu achilankhulo china.​—Chv 14:​6, 7.

Kodi munaganizirapo zophunzira chilankhulo china kuti muthandize munthu wina kuphunzira choonadi? Ngati mulibe nthawi yokwanira kuphunzira chilankhulo china, mukhoza kugwiritsa ntchito pulogalamu ya JW Language kuti mungophunzira ulaliki wachidule. Mukatero mukhoza kusangalala ngati mmene abale a m’nthawi ya atumwi anasangalalira anthu a m’madera ena atamva “zinthu zazikulu za Mulungu” m’chilankhulo chawo.​—Mac 2:​7-11.

ONERANI VIDIYO YAKUTI, KHALANI BWENZI LA YEHOVA​—MUZILALIKIRA ANTHU OLANKHULA CHINENERO CHA DZIKO LINA NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti ‘Khalani Bwenzi la Yehova​—Muzilalikira Anthu Olankhula Chinenero cha Dziko Lina.’ Kalebe akuganizira mmene zikanakhalira pakanakhala loboti imene ingamuthandize kulalikira kwa mayi amene si wachilankhulo chake.

    Kodi ndi pa nthawi iti pamene mungagwiritse ntchito pulogalamu ya JW Language?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti ‘Khalani Bwenzi la Yehova​—Muzilalikira Anthu Olankhula Chinenero cha Dziko Lina.’ Tsamba lophunzirira Kupatsana Moni ndi Kudziwana la mupulogalamu ya ‘JW Language.’

    Tchulani zinthu zina zimene pulogalamuyi ili nazo.

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti ‘Khalani Bwenzi la Yehova​—Muzilalikira Anthu Olankhula Chinenero cha Dziko Lina.’ Mayi yemwe uja akusangalala Sofiya ndi Kalebe atamupatsa moni m’Chitchainizi.

    Anthu a zilankhulo zonse akufunika kumva uthenga wabwino

    Kodi anthu a m’gawo lanu amalankhula zilankhulo ziti?

  • Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mwakumana ndi munthu wachidwi amene amalankhula chilankhulo china?​—od 101 ¶39-​41.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena