Ndandanda ya Mlungu wa January 28
MLUNGU WOYAMBIRA JANUARY 28
Nyimbo Na. 11 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 18 ndime 6-11 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Mateyu 16-21 (Mph. 10)
Na. 1: Mateyu 17:22–18:10 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Ndi ‘Mawu Abwino’ ati a Yehova Amene Yoswa Anaona Akukwaniritsidwa?—Yos. 23:14 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Ndi Maulosi Ena ati Apadera a M’Baibulo Amene Sanakwaniritsidwebe?—rs tsa. 389 ndime 2–tsa. 390 ndime 2 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Yambitsani Phunziro la Baibulo Loweruka Loyambirira. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 4, chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo, Loweruka loyambirira m’mwezi wa February. Limbikitsani ofalitsa onse kuti adzayesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo.
Mph. 25: “Kodi Tingatani Kuti Tipewe Imfa Zobwera Chifukwa cha Malungo?” Nkhani yokambirana ndi omvera yokambidwa ndi mkulu woyenerera. Pomaliza nkhaniyi bwerezani mfundo zimene mwakambirana pogwiritsa ntchito mafunso atatu amene ali kumapeto kwa nkhaniyi. Limbikitsani makolo kufunika kopita mwachangu kuchipatala ndi ana awo akayamba kuona zizindikiro za malungo.
Nyimbo Na. 53 ndi Pemphero