Kodi Tingatani Kuti Tipewe Imfa Zobwera Chifukwa cha Malungo?
M’nyengo ya mvula ino, m’pofunika kwambiri kuti ifeyo limodzi ndi mabanja athu tidziziteteza ku malungo. Kuchita zimenezi kumasonyeza kuti timaona moyo ngati mmene Yehova amauonera. (Sal. 36:9) Pofuna kusonyeza kuti amayamikira mphatso ya moyo, Akhristu amachita zonse zomwe angathe kuti apewe zinthu zimene zingaike moyo wawo pangozi. Zimenezi zikuphatikizapo kuyesetsa kutsatira malangizo onse owathandiza kupewa matenda, monga malungo.
Anthu mamiliyoni ambiri, makamaka ana osaposa zaka zisanu, amafa ndi malungo. Koma n’zosangalatsa kuti matenda oopsawa akhoza kupewedwa ngati mabanja atamayesetsa kutsatira njira zowapewera. Unduna wa Zaumoyo ndi Chiwerengero cha Anthu umalimbikitsa anthu kuti azigona m’maneti onyikidwa m’mankhwala pofuna kupewa malungo. Maneti amenewa ndi osavuta kupeza ndiponso otsika mtengo poyerekezera ndi kugula mankhwala, kulipira kuchipatala komanso poyerekezera ndi kutaya moyo wa munthu.
Choncho anthu omwe ndi mitu ya mabanja angachite zinthu mwanzeru poonetsetsa kuti ana awo akugona m’maneti komanso poonetsetsa kuti malo onse ozungulira nyumba yawo ndi aukhondo. Pa nyengo ya mvula ino, muzionetsetsa kuti pakhomo panu palibe malo oti udzudzu ukhoza kuswana. Ena mwa malo amenewa ndi maenje, matayala akutha a galimoto ndiponso malo ena alionse amene amasunga madzi. N’chifukwa chiyani kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri? Monga mmene tikudziwira, udzudzu umakonda kuswana pamadzi amene angoima.
Ana osaposa zaka zisanu sachedwa kufa ndi malungo akapanda kulandira chithandizo choyenera. Choncho ndi bwino kuti makolo akangoona kuti ana awo akusonyeza zizindikiro za malungo, monga kutentha thupi, kusafuna kudya, kutseguka m’mimba ndiponso kusanza, NTHAWI YOMWEYO azipita nawo kuchipatala kuti akalandire mankhwala a malungo, monga Kwinini ndi La. (Lonart, Coaterm, Artesanate, Du-cotexin) Dziwani kuti kumwa Khafino yekha kapena Panado yekha sikuchiza malungo. Ngati mutachedwa kupita kuchipatala ndi mwana amene akudwala malungo, zingachititse kuti magazi achepe kwambiri m’thupi lake. Zimenezi zingachititse kuti madokotala aganize zoti mwanayo aikidwe magazi popeza iwo amaona kuti kuika magazi ndi njira yothandizira munthu yemwe akudwala kwambiri malungo.
Makamaka akulu ndi atumiki othandiza ayenera kupereka chitsanzo chabwino pa nkhani yosamalira ana awo. (1 Tim. 5:8) Ngati iwo atamapita mwamsanga kuchipatala ndi mwana wawo amene wadwala malungo, angapereke chitsanzo chabwino kwa makolo ena mumpingo.
Gulu lina la ofalitsa limene lingadwale mosavuta matenda a malungo, ndi amayi oyembekezera. Unduna wa Zaumoyo umalimbikitsa amayi onse oyembekezera kuti azipita kuchipatala akangodziwa kuti ali ndi pakati. Zimenezi zimathandiza kuti apewe mavuto osiyanasiyana, monga kuchepa kwa magazi m’thupi pa nthawi imene ali oyembekezera. Mayi woyembekezera amene sakudwala malungo amabereka mwana wathanzi. (Onani Galamukani! ya November, 2009, masamba 26-29)
Pomaliza, ofalitsa onse akulimbikitsidwa kudziwitsa akulu ngati munthu aliyense wa m’banja mwawo wapita kuchipatala. Ngati pabuka nkhani yokhudza magazi, akulu ayenera kudziwitsa abale a m’Komiti Yolankhulana ndi Achipatala n’cholinga choti awathandize.
Mafunso
1. Kodi malungo ndi oopsa bwanji, makamaka kwa ana?
2. Kodi tingatani kuti titeteze anthu a m’banja mwathu ku malungo?
3. Kodi makolo achikhristu ayenera kuchita chiyani mwamsanga munthu wa m’banja mwawo akayamba kusonyeza zizindikiro za malungo?