Ndandanda ya Mlungu wa January 21
MLUNGU WOYAMBIRA JANUARY 21
Nyimbo Na. 40 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 18 ndime 1-5, bokosi patsamba 142, 144. (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Mateyu12-15 (Mph. 10)
Na. 1: Mateyu 14:23–15:11 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Ngati Wina Wanena Kuti, ‘Ngati Mukufuna Kundilalikira Uthenga Wanu, Mupemphere Kaye’—rs tsa. 342 ndime 7-8 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani pa Chitsanzo cha Isaki Chokonda Kuchita Zinthu Mwamtendere?—Gen. 26:19-22 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Lengezani Uthenga Wabwino Mwakhama. (Mac. 5:42) Funsani wofalitsa m’modzi kapena awiri amene amadziwika kuti amalalikira mwakhama. N’chiyani chimawathandiza kuti aziona utumiki kukhala wofunika? Kodi amachita zotani pokonzekera utumiki? Kodi utumiki wawathandiza bwanji kuti akhale paubwenzi wolimba ndi Yehova?
Mph. 10: Khalidwe Lathu Labwino Limapereka Umboni. (1 Pet. 2:12) Nkhani yokambirana ndi omwera yochokera m’buku lakuti Khalanibe M’chikondi cha Mulungu mutu 14, ndime 15 mpaka 19. Pemphani omvera kunena zimene zinawachitikira chifukwa chokhala oona mtima pa zinthu zonse.
Mph. 10: “Kodi Mungapemphe Gawo Lanulanu?” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 96 ndi Pemphero