Mmene Tingalalikirire M’gawo la Malonda
1. Kodi kulalikira m’gawo la malonda kuli ndi phindu lanji?
1 Kodi mukufuna kukalalikira kugawo limene anthu amalandira bwino alendo ndiponso kumene sikaŵirikaŵiri kupeza anthu kulibe? Mungathe kuchita zimenezi m’gawo la mpingo wanu lomwelo. Motani? Mwa kupita ku malo amalonda opezeka kwanuko. Ofalitsa amene amalalikira sitolo ndi sitolo amakhala ndi zotsatirapo zosangalatsa.
2. Kodi ulaliki wa kumalo a malonda ungalinganizidwe motani?
2 Mipingo ina ili ndi malo a malonda m’gawo lawo. Mbale amene amasamalira za magawo angakonze makadi apadera a mapu a malo ameneŵa, kumene anthu ambiri amapezekako. Makadi a mapu alionse a gawo limene kuli nyumba za anthu ndipo gawolo laloŵererana ndi gawo la malonda, afunika kusonyeza bwino kuti gawo la malonda siliyenera kulalikidwa monga gawo lomwe si lamalonda. M’madera ena, malo amalonda angalalikidwe pamodzi ndi magawo amene si amalonda. Ngati simunayambe mwachitapo ulaliki wa m’gawo la malonda, mungayese mwa kuyamba ndi kulalikira m’masitolo aang’ono oŵerengeka chabe.
3. Kodi chidzatithandiza n’chiyani kuti tikhale ogwira mtima tikamachita ulaliki wa sitolo ndi sitolo?
3 Gwiritsani Ntchito Mafikidwe Osavuta: Polalikira sitolo ndi sitolo, ndi bwino kuvala ngati momwe mumavalira mukamapita ku misonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Ndi bwinonso kusankha nthaŵi imene sali otanganidwa m’sitolo. Ngati n’kotheka loŵani panthaŵi imene mulibe ogula. Pemphani kuti mulankhule ndi bwana kapena wina amene ali woyang’anira. Lankhulani mwachidule koma molunjika pa mfundo yeniyeni. Kodi munganene kuti chiyani?
4-6. Kodi tinganene kuti chiyani ngati tikulalikira kwa wogulitsa m’sitolo kapena bwana wake?
4 Pamene mukulankhula kwa wogulitsa m’sitolo kapena bwana munganene kuti: “Anthu amalonda amakhala otanganidwa moti nthaŵi zambiri sitiwapeza panyumba, ndiye tafika kudzacheza ndi inu kuno kuntchito. Magazini anthuŵa akusonyeza zimene zikuchitika padziko lonse.” Kenako sonyezani mfundo imodzi mwachidule kuchokera m’magaziniyo.
5 Kapena mungayese mafikidwe ena aŵa osavuta: “Anthu ambiri amafuna kudziŵa zambiri za Baibulo koma amakhala ndi nthaŵi yochepa kwambiri. Thirakiti ili likufotokoza za pulogalamu ya phunziro laulere imene ilipo kuti ikuthandizeni kupeza mayankho a mafunso amene mumawapeza kuchokera m’Baibulo.” Mukatero musonyezeni masamba 4-5 a thirakiti lakuti, Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo?
6 Ngati bwanayo akuoneka kuti ndi wotanganidwa, mukhoza kungopereka thirakitilo ndiyeno n’kumuuza kuti: “Ndibweranso nthaŵi ina ndikaona kuti simuli otanganidwa kwambiri. Ndikufuna kudziŵa maganizo anu pa zimene thirakitili likunena.”
7. Kodi tingakulitse motani chidwi chimene timapeza m’gawo la malonda?
7 Kukulitsa Chidwi Chimene Anasonyeza: N’zothekanso kuchititsa phunziro la Baibulo m’gawo la malonda. Mpainiya wina wapadera anali ndi chizoloŵezi chopatsa magazini mwamuna wina wa malonda. Pamene mwamunayo anaonetsa chidwi pa zimene anali kuŵerenga, mpainiyayo anamusonyeza mwamunayo mmene phunziro la Baibulo limachitikira pogwiritsa ntchito bulosha la Mulungu Amafunanji. Phunziro linayambika ndipo limachitikira pomwepo pamalo pamene amagulitsira malondapo. Poganizira mmene malo a malonda amakhalira, mpainiyayo amachititsa phunzirolo kwa mphindi 10 kapena 15 zokha nthaŵi zonse. Mofananamo, tiyeni nafenso tipitirizebe kufunafuna oyenerera mwa kulalikira m’gawo la malonda.