Bokosi la Mafunso
◼ Kodi ngati munthu akufuna magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! angawapeze bwanji?
Popeza kuti makonzedwe olembetsa makaseti ndi magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! m’zinenero zonse analekeka, ofalitsa onse ayenera kupeza magazini ndi makaseti ku mpingo wakwawo, kupatulapo magazini ndi makaseti a anthu akhungu amene amatumizidwa monga zinthu zaulere kwa okhawo amene ali oyenerera. Chonde dziŵani kuti mipingo ingathe kuitanitsa magazini a pakaseti pa fomu ya Zofunsira za Mpingo (M-202). Mungaitanitse makope a zinenero za kumayiko ena ndi azilembo zikuluzikulu pafomu yomweyi.
Ngati wina m’gawo lanu wapempha kuti muzikam’patsa magazini nthaŵi zonse, chonde yambani kuchita zimenezo mwamsanga ndipo onetsetsani kuti sakuphonya ndi imodzi yomwe. Ochotsedwa angapeze magazini kapena mabuku awo oti azigwiritsa ntchito pa malo amene timalandirira magazini ndi mabuku pa Nyumba ya Ufumu. Ochotsedwa sakuphatikizidwa pa anthu amene timakawapatsa magazini. Choncho sitiyenera kukawapatsa magazini.
Okhawo amene ofalitsa a mpingo sangakwanitse kumakawapatsa magazini, ndi amene nthambi ya Malawi idzawasunga pa ndandanda ya olembetsa magazini. Ngati Komiti ya Utumiki ya Mpingo itumiza fomu yolembetsera magazini ya munthu wina amene sangathe kupeza magazi m’njira ina iliyonse, mlembi ayenera kuphatikizapo kalata yachidule yosonyeza kuti Komiti ya Utumiki ya Mpingo yapenda kulembetsako bwinobwino ndipo yavomereza zimenezo.
Zimenezi zikutanthauza kuti ofalitsa sayenera kulembera ofesi ya nthambi kuiuza kuti akufuna kulembetsa magazini. Ngati ofalitsa kapena anthu achidwi apempha kulembetsa magazini mwa njira imeneyi, ofesi ya nthambi idzabweza zimenezo ku mpingo.
◼ Kodi akaidi angapeze bwanji magazini awo?
Ngati mpingo umene umalalikira m’ndende ungathe kugaŵira magazini kwa akaidiwo, ndiye kuti mkaidi angapeze magazini ake a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwa ofalitsa amene amapita kumeneko. Ngati zimenezi n’zosatheka, mkaidiyo ayenera kulemba yekha kalata ku ofesi ya nthambi kuwauza kuti akufuna kulembetsa magazini. Chonde dziŵani kuti akaidi ochotsedwa angapeze magazini awo kudzera m’njira imene yafotokozedwa m’ndimeyi.