Lalikirani Uthenga Wabwino Paliponse
1 Akristu oyambirira analalikira uthenga wabwino paliponse. Anali achangu kwambiri kwakuti mkati mwa zaka 30 za kuuka kwa Yesu Kristu, uthenga wa Ufumu unakhala “wolalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.”—Akol. 1:23.
2 Atumiki a Yehova achangu alerolino ali ndi cholinga chimodzimodzicho—kufikira aliyense amene angathe ndi uthenga wabwino wa Ufumu. Kodi nchiyani chimene chingatithandize kukwaniritsa cholinga chimenechi? Anthu omawonjezereka akugwira ntchito tsiku lonse ndipo kaŵirikaŵiri samapezeka panyumba pamene tifika. Pamene sakugwira ntchito, angakhale akuyenda ulendo, amakagula zinthu, kapena kupita kokasanguluka. Kodi ndi motani mmene oyenera pakati pawo akufikidwira ndi uthenga wa Ufumu?—Mat. 10:11.
3 Ena akufikiridwa kumalo awo antchito. Ngakhale matauni aang’ono ali ndi malo amalonda kumene anthu ambiri amatherako tsiku lonse. M’mizinda yaikulu, anthu ogwira ntchito m’maindasitale kapena m’nyumba zazitali za maofesi ndi aja okhala m’nyumba zotetezeredwa kwambiri akulandira umboni—ambiri a iwo kwa nthaŵi yoyamba. Pakutha kwa milungu, ena amene afikiridwa pamene anali kusanguluka m’mapaki, m’malo a zosangulutsa, malo oimikako mahema, kapena m’ma cottage kapena pamene akuyembekezera pamalo oimikapo galimoto kapena pamasitolo apezedwa kukhala ofuna uthenga wabwino.
4 Chiŵerengero chomawonjezereka cha ofalitsa akuyesayesa mwapadera kuchitira umboni pamalo apoyera, kulikonse kumene angapeze anthu. Poyamba, Mboni zimenezi zinali kuzengereza ndi kuchita mantha pang’ono chifukwa cha kuzoloŵera kulalikira kolinganizidwa, monga kwa kukhomo ndi khomo. Kodi tsopano akumva bwanji?
5 “Zaperekanso nyonga pa utumiki wanga!” akunena motero mbale wina wozoloŵera. Wina akuwonjezera kuti: “Umandichititsa kukhala watcheru.” Mpainiya wina wachikulire akuti: “Wandipatsa nyonga mwamaganizo, mwakuthupi, ndi mwauzimu, . . . ndipo ndikali kukula.” Wofalitsa wina akunena kuti tsopano iye akufikira anthu ambiri amene sanakambitsiranepo ndi Mboni za Yehova. Achichepere nawonso akukhala ndi phande mwamphamvu mu ntchito yosangalatsa imeneyi. Wachichepere wina akufotokoza motere: “Nkokondweretsa chifukwa umalankhula ndi anthu ambiri.” Wina akuti: “Ndikugaŵira mabuku ambiri kuposa kale!” Zonsezi zikuchitika m’gawo limene limagwiridwamo ntchito kwambiri.
6 Oyang’anira Oyendayenda Akutsogolera: Pozindikira kuti “mkhalidwe wa dzikoli ukusintha,” posachedwapa Sosaite inapereka lingaliro lakuti oyang’anira oyendayenda azisintha ndandanda yawo ya utumiki wakumunda mlungu ndi mlungu kotero kuti afikire anthu ambiri monga momwe angathere ndi uthenga wabwino. (1 Akor. 7:31, NW) Kwa zaka zambiri, oyang’anira madera apatula nthaŵi mmaŵa masiku a mkati mwa mlungu kuti achite ntchito ya kunyumba ndi nyumba, pamene kuli kwakuti masana anawalinganizira kupanga maulendo obwereza ndi kukachititsa maphunziro a Baibulo apanyumba. M’madera ena, ndandanda imeneyo ingakhalebe yogwira ntchito. M’madera ena, sangachite zambiri mwa kugwira ntchito kunyumba ndi nyumba mmaŵa masiku ena a mkati mwa mlungu. M’mikhalidwe yotero, woyang’anira woyendayenda angasankhe kuti kuchiyambi kwa tsikulo ndi bwino kuti achite ntchito ya kusitolo ndi sitolo kapena umboni wa m’khwalala. Kapena angalinganize timagulu toti tichitire umboni m’nyumba zazitali za maofesi, kumasitolo, moimikamo galimoto, kapena malo ena apoyera. Mwa kugwiritsira ntchito nthaŵi yomwe ali nayo mu utumiki wakumunda bwino lomwe, ofalitsa adzafikira anthu owonjezereka.
7 Malipoti akusonyeza kuti oyang’anira oyendayenda ndi ofalitsa omwe akonda kusintha kumeneku. Mabungwe ambiri a akulu apempha woyang’anira dera kuphunzitsa ofalitsa angapo mbali za ntchito zofunikira chisamaliro kumaloko. Kwakhala kothandiza kwa ofalitsa ameneŵa kuyenda ndi woyang’anira woyendayenda pamene achita imodzi ya ntchito zimenezi. Nawonso, atha kuphunzitsa enanso. (2 Tim. 2:2) Chotero, anthu owonjezereka tsopano akufikiridwa ndi uthenga wabwino.
8 Ndithudi, simufunikira kuyembekezera kuchezetsa kwa woyang’anira dera kuti muyese zina za njira zimenezi za kulalikira. Nawa malingaliro osiyanasiyana amene mungapeze kukhala othandiza m’gawo lanu:
9 Umboni wa m’Khwalala: ‘Kodi anthu onse apita kuti?’ nthaŵi zina timadzifunsa motero pamene tifika m’dera lopanda anthu mmaŵa patsiku la mkati mwa mlungu. Mungapeze ena atatumidwa kapena atapita kukagula zinthu. Kodi mwayesa kuwafikira kupyolera mu umboni wa m’khwalala? Pamene uchitidwa moyenera, mbali imeneyi ya utumiki ingakhale yobala zipatso kwambiri. M’malo mwa kungoima pamalo amodzi ndi magazini, ndi bwino kwambiri kufikira anthu ndi kuyamba kukambitsirana nawo mwaubwenzi. Simufunikira kupereka umboni kwa wodutsa aliyense. Lankhulani kwa anthu amene akuyenda mosafulumira, monga ngati oona zinthu m’masitolo, aja amene akhala m’galimoto zimene zaimikidwa, kapena anthu oyembekezera kukwera zoyendera. Poyamba, mungangopereka moni waubwenzi ndi kuyembekezera yankho. Ngati munthuyo akufuna kukambitsirana, mfunseni lingaliro lake pa nkhani imene mukulingalira kuti ingamkondweretse.
10 Woyang’anira woyendayenda wina anapempha ofalitsa asanu ndi mmodzi kugwirizana naye ndi mkazi wake mu umboni wa m’khwalala. Chotulukapo chake chinali chotani? “Tinasangalala kwambiri mmaŵa!” iyeyo akusimba motero. “Panalibe amene sitinawapeze panyumba. Tinagaŵira magazini 80 ndi matrakiti ambiri. Tinakambitsirana mosangalatsa ndi anthu angapo. Wofalitsa wina, amene anali mu ntchito ya m’khwalala kwa nthaŵi yoyamba, anadzuma kuti: ‘Ndakhala m’choonadi kwa zaka zambiri ndipo sindinazindikire zimene ndinali kuphonya!’ Pakutha kwa mlungu, magazini ounjikana a mpingowo anatha.”
11 Pamene anali kutumikira mpingo wotsatira, woyang’anira woyendayenda mmodzimodziyo anamva kuti ofalitsa angapo anachita nawo umboni wa m’khwalala mmamaŵa wina koma anali ndi chipambano chochepa. Mlongo wina anangolankhula kwa anthu aŵiri okha m’nyengo yonse ya kuchitira umboniyo, popeza kuti aliyense amene anakumana naye anali kuthamangira kuntchito. Woyang’anira woyendayenda anapereka lingaliro lakuti onsewo abwerere kukhwalala limodzimodzilo patapita nthaŵi ina mmaŵawo. Iwo anatero, ndipo anakhalamo kufikira dzuŵa litafika pamutu. Mlongo uja amene analankhula ndi anthu aŵiri okha poyamba mmaŵa anachita bwino kwambiri pamene anabwererako. Anagaŵira magazini 31 ndi mabrosha 15, kulemba maina ndi makeyala a anthu asanu ndi aŵiri, ndipo anayambitsa maphunziro aŵiri a Baibulo apanyumba! Ena a m’gululo mofananamo anali ndi zotulukapo zolimbikitsa.
12 Pamene mupeza munthu amene akusonyeza chidwi, yesani kulemba dzina la munthuyo, keyala, ndi nambala ya telefoni. M’malo mwa kumpempha zimenezo, munganene kuti: “Ndasangalala pa kukambitsirana kumeneku. Kodi pali njira iliyonse imene tingapitirize kukambitsiranaku panthaŵi ina?” Kapena funsani kuti: “Kodi pali njira iliyonse imene ndingakupezereni kwanu?” Ambiri amene amafikiridwa motere amavomera za kudzaonana nawonso.
13 Ngati mulankhula kwa munthu wokondwerera amene amakhala m’gawo la mpingo wina, muyenera kudziŵitsa a mpingowo kotero kuti abale kumeneko apite kwa wokondwererayo. Kodi umboni wa m’khwalala ungakhale njira yogwira mtima ya kuwanditsira uthenga wabwino m’dera lanu? Ngati ndi choncho, pendani nkhani yakuti “Kupeza Okondwerera Kupyolera mu Umboni wa m’Khwalala Wogwira Mtima” m’kope la Utumiki Wathu Waufumu wa July 1994. Ndiyeno linganizani kuchita umboni wa m’khwalala panthaŵi yoyenera ya tsiku imene idzakukhozetsani kufikira anthu ambiri monga momwe kungathekere.
14 Kuchitira Umboni m’Zoyendera za Onse: Mmaŵa wina apainiya angapo anasankha kuchitira umboni kwa anthu amene anali kuyembekezera basi pafupi ndi koleji ina ya kumaloko. Ngakhale kuti ankakambitsirana ndi anthuwo mokondweretsa, panali vuto. Pamene makambitsirano anali kupitiriza mokoma, basi inali kufika, zikumachititsa makambitsiranowo kuduka. Apainiyawo anathetsa vutolo mwa kukwera nawo basi ndi kupitiriza kuchitira umboni kwa okweramowo pamene anali kudutsa m’tauni. Atafika kolekezera basiyo, apainiyawo anali kubwerera ndi basiyo, akumachitira umboni pamene anali kupita. Atayenda maulendo angapo a kupita ndi kubwera, anaonkhetsa zogaŵira zawo pa kuyesayesa kwawo: Anagaŵira magazini oposa 200 ndipo anayambitsa maphunziro a Baibulo asanu ndi limodzi. Okwera basi ena anawapatsa makeyala ndi nambala zawo za telefoni modzifunira kuti aziwafikira kwawo. Sabata lotsatira, apainiyawo anabwerera poimira basi natsatira njira imodzimodziyo monga poyamba. Anagaŵira magazini 164 nayambitsa phunziro linanso la Baibulo. Pokwerera basi pena munthu wina analoŵa m’basi nakhala pa mpando umodzi wokha umene unatsala—moyandikana ndi mpainiya. Iyeyo anayang’ana mbaleyo nati momwetulira: “Ndikudziŵa kuti mwandisungira Nsanja ya Olonda.”
15 Ofalitsa ambiri amapereka umboni wogwira mtima pamene ali paulendo wa pabasi, pasitima, kapena wa pandege. Kodi mungayambe motani kukambitsirana ndi pasinjala wokhala moyandikana nanu? Wofalitsa wina wazaka 12 anangoyamba kuŵerenga kope la Galamukani! m’basi, akumayesa kudzutsa chidwi cha msungwana wachichepere amene anakhala moyandikana naye. Zimenezi zinagwiradi ntchito. Msungwanayo anamfunsa zimene anali kuŵerenga, ndipo mnyamatayo anayankha kuti anali kuŵerenga za chothetsera mavuto amene achichepere amayang’anizana nawo. Anawonjezera kuti iyeyo anali atapindula kwambiri kale ndi nkhaniyo ndi kuti nayenso msungwanayo ingamthandize. Analandira magaziniwo mokondwera. Achichepere ena aŵiri amene anamva kukambitsirana kwawo anapemphanso makope a magaziniwo. Pa zimenezi, woyendetsa basi anaima pambali pa msewu nafunsa chifukwa chake ochuluka anali ndi chidwi ndi magaziniwo. Pamene anadziŵa, nayenso analandira makopewo. Ndithudi, zonsezi sizikanatheka ngati wofalitsa wachichepereyo analibe mtokoma wokwanira wa magazini oti apatse aliyense amene anasonyeza chidwi!
16 Kuchitira Umboni m’Mapaki ndi Moimikamo Galimoto: Kuchitira umboni m’mapaki ndi moimikamo galimoto kuli njira yabwino koposa yofikira anthu. Kodi mwayesa kuchitira umboni m’madera oimikamo galimoto akumasitolo? Nthaŵi zonse patulani nthaŵi ya kupenda malowo. Funani munthu amene akuyenda mosafulumira kapena amene akuyembekezera m’galimoto loimikidwa ndipo yesani kuyambitsa makambitsirano aubwenzi. Ngati makambitsiranowo apitiriza, loŵetsanimo uthenga wa Ufumu. Yesani kugwira ntchito panokha komano muli ndi wofalitsa wina m’malowo. Peŵani kunyamula chikwama chachikulu, chokhuta kapena kuchititsa ena kunyumwa ndi ntchito yanu m’njira ina. Khalani waluntha. Mwina ndi bwino kwambiri kuthera nthaŵi yaifupi m’malo amodzi oimikamo galimoto ndiyeno kumka m’malo ena. Ngati ena sakufuna kukambitsirana nanu, chokani mwaulemu ndi kukafunafuna wina womfikira. Akumagwiritsira ntchito njira zimenezi, mbale wina anagaŵira magazini 90 m’mwezi umodzi pamene anali kuchitira umboni m’malo oimikamo galimoto.
17 Anthu ena amamka ku paki kukatsitsimuka; ena amapita kumeneko kukaseŵera maseŵero kapena kukathera nthaŵi kumeneko ndi ana awo. Funafunani mpata wa kupereka umboni popanda kudodometsa zochita zawo kosafunikira. Mbale wina anayambitsa makambitsirano ndi woyang’anira kapinga wa m’paki ndi kupeza kuti anali ndi nkhaŵa ponena za anamgoneka ndi mtsogolo mwa ana ake. Phunziro la Baibulo lapanyumba linayambidwa ndipo linali kuchitidwa mokhazikika m’paki.
18 Kuchitira Umboni Wamwamwaŵi m’Malo a Masitolo: Pamene kuli kwakuti nthaŵi zina nkosatheka kulalikira kusitolo ndi sitolo m’malo a masitolo chifukwa cha ziletso zakumaloko pantchito zotero, ofalitsa ena amapanga mipata ya kuchitira umboni kumeneko mwamwaŵi. Amakhala pa benchi ndi kuyambitsa makambitsirano aubwenzi ndi ena amene amaima kuti apume. Pamene asonyeza chidwi, iwo amagaŵira trakiti kapena magazini mochenjera ndi kuyesayesa kupanga makonzedwe a ulendo wobwereza. Atathera mphindi zingapo akumachitira umboni ku chigawo chimodzi, amapita ku china nayamba kukambitsirana ndi munthu wina. Zoonadi, tifunikira kusamala kuti tisachititse ena kunyumwa pamene tikuchitira umboni mwamwaŵi m’njira imeneyi.
19 Popereka moni kwa munthu, yambani makambitsirano mwaubwenzi. Ngati womvetsera wanu ayankha, funsani funso, ndiyeno mvetserani mosamalitsa pamene akufotokoza malingaliro ake. Sonyezani chikondwerero pa zimene akunena. Sonyezani kuti mukuyamikira lingaliro lake. Ngati kuli kotheka, vomerezanani naye.
20 Mlongo wina anali ndi makambitsirano okondweretsa ndi mkazi wina wokalamba mwa kutchula mmene zinthu zakwerera mtengo. Mkaziyo anavomereza, ndipo anayamba kukambitsirana mwaumoyo. Mlongoyo anatha kulemba dzina ndi keyala ya mkaziyo, ndipo anapanga ulendo wobwereza mlungu umodzimodziwo.
21 Kugwira Ntchito Kusitolo ndi Sitolo: Mipingo ina ili ndi zigawo zamalonda monga mbali yawo ya gawo logaŵiridwa. Mbale wosamalira gawo angakonze makhadi a mapu apadera a zigawo zamalonda zambiri zimenezi. Pamakhadi a mapu alionse a malo a anthu amene amadutsa m’malo azamalonda payenera kusonyezedwa kuti malo azamalondawo sayenera kugwiridwa ntchito monga mbali ya gawo. M’magawo ena, tingagwire ntchito m’malo azamalonda pamodzi ndi malo okhalamo anthu. Akulu angapemphe ofalitsa okhoza kukagwira ntchito m’magawo azamalonda nthaŵi zonse kotero kuti ntchito ya kusitolo ndi sitolo isanyalanyazidwe.
22 Ngati mwapemphedwa kukachita nawo ntchito imeneyi ndipo simunaichitepo ndi kale lonse, njira yabwino ya ‘kulimbika’ ndiyo kugwira ntchito m’masitolo angapo aang’ono choyamba; ndiyeno, pamene mukukhala ndi chidaliro chowonjezereka, gwirani ntchito m’masitolo aakulu. (1 Ates. 2:2) Pamene mukugwira ntchito kusitolo ndi sitolo, valani monga mmene mukanavalira popita ku msonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Ngati nkotheka, loŵani m’sitolo pamene mulibe ogula oyembekezera kuthandizidwa. Pemphani kulankhula ndi manijala kapena mkulu wa ntchito. Khalani waubwenzi, ndipo koposa zonse, wachidule. Simufunikira kupepesa. Amalonda ambiri amakonda ogula ndipo amalolera kudodometsedwa.
23 Mutapereka moni kwa wogulitsa m’sitolo, munganene motere: “Anthu amalonda ali ndi zochita zambiri kwakuti kaŵirikaŵiri sitimawapeza panyumba, chotero takufikirani pantchito panu pano kudzakusiyirani nkhani ina yosonkhezera maganizo kuti muŵerenge.” Ndiyeno tchulani mfundo imodzi kapena ziŵiri za magazini amene mukugaŵira.
24 Kapena mungayese kafikidwe aka kwa manijala: “Tapeza kuti anthu amalonda amafuna kudziŵa zambiri. Kope latsopano la Nsanja ya Olonda (kapena Galamukani!) lili ndi nkhani imene ikukhudza ife tonse patokha.” Longosolani nkhaniyo, ndipo malizani mwa kunena kuti: “Tikukhulupirira kuti mudzakondwera kuliŵerenga.”
25 Ngati pali olembedwa ntchito, ndipo zichita ngati kuti nzoyenera, mungawonjezere kuti: “Kodi mungandilole kupereka ulaliki wachidule umodzimodziwu kwa antchito anu?” Ngati akulolani, kumbukirani kuti mwalonjeza kukhala wachidule, ndipo manijalayo adzayembekezera kuti mudzasunga lonjezo lanu. Ngati wantchito wina aliyense akufuna kuti mukambitsirane kwa nthaŵi yaitali, ndi bwino kwambiri kukamfikira kunyumba.
26 Posachedwapa, ofalitsa angapo m’tauni ina anagwirizana ndi woyang’anira dera mu ntchito ya kusitolo ndi sitolo. Ena a ofalitsawo poyamba anali amantha, pokhala asanachitepo ntchitoyo; komano posakhalitsa iwo anamasuka nayamba kusangalala nayo. M’nyengo yochepera pa ola limodzi, analankhula kwa anthu 37 ndi kugaŵira magazini 24 ndi mabrosha 4. Mbale wina ananena kuti nthaŵi zambiri samaonana ndi anthu ambiri m’mwezi umodzi wa ntchito ya kunyumba ndi nyumba monga momwe anachitira pogwira ntchito kusitolo ndi sitolo m’nyengo yaifupi imeneyo.
27 Kupanga Mipata ya Kulalikira: Yesu sanangolalikira molinganizidwa chabe. Anawanditsa uthenga wabwino pa nthaŵi iliyonse yoyenera. (Mat. 9:9; Luka 19:1-10; Yoh. 4:6-15) Onani mmene ofalitsa ena amapangira mipata ya kulalikira.
28 Ena amapanga chizoloŵezi cha kuchitira umboni kwa makolo amene akuyembekezera ana awo pafupi ndi khomo la sukulu. Popeza kuti makolo ambiri amafika mwamsanga patatsala mphindi 20, pamakhala nthaŵi yakukambitsirana nawo nkhani ina yosangalatsa ya m’Malemba.
29 Apainiya ambiri amadziŵa kufikira anthu amene ali ndi chidwi pankhani ina imene ikufotokozedwa m’magazini athu. Mwachitsanzo, mlongo wina analandiridwa bwino pamene anafikira sukulu zisanu ndi imodzi m’gawo la mpingo wake ndi mpambo wa nkhani zakuti “Sukulu Zili m’Mavuto,” zimene zinatuluka mu Galamukani! wa January 8, 1996, masamba 19-29. Anafikiranso malo olangizirako mabanja ndi magazini onena za moyo wabanja ndi kuchitira nkhanza ana ndipo anapemphedwa kubwererako ndi makope ena amtsogolo osimba nkhani zofananazo. Anafotokozanso kuti anamlandira “bwino koposa” ku ofesi ya osoŵa ntchito ndi Galamukani! wa March 8, 1996 wosimba za ulova.
30 Woyang’anira chigawo wina akusimba kuti iye ndi mkazi wake amachitira umboni wamwamwaŵi nthaŵi zonse pamene akugula zogulagula zawo. Amakagula zinthu panthaŵi imene sitolo ilibe anthu ambiri, ndi pamene anthu akuyendayenda m’tinjira ta mkati mwa sitolo mosathamanga. Akusimba za kukambitsirana bwino ndi anthu ambiri.
31 M’mizinda ina, ofalitsa amasimba za zotulukapo zabwino pamene akuchitira umboni kwa anthu m’malo ochapira zovala a onse. Samangosiya chabe magazini pamene palibe munthu wina aliyense. Cholinga chawo ndicho kufikira anthu ndi uthenga wabwino, chotero amayesetsa kulankhula mwachindunji ndi awo amene akugwiritsira ntchito malowo.
32 M’malo ena, ofalitsa osankhidwa ndiwo amene amaloledwa kuchitira umboni pamabwalo a ndege. Nthaŵi zina, apeza chimwemwe cha kuchitira umboni kwa apaulendo amafuko onse amene amakhala m’maiko mmene anthu a Yehova ali oŵerengeka. Pamene apeza munthu wokondwerera, amamgaŵira trakiti kapena magazini.
33 Ngati saloledwa kuchitira umboni mwachindunji kwa anthu okhala m’malo otetezeredwa kwambiri m’gawo la mpingo, ena apanga chizoloŵezi cha kuchitira umboni mwaluso kwa alonda apanthaŵiyo kapena kwa oyang’anira a nyumbazo. Njira imodzimodziyo imagwiritsiridwa ntchito m’nyumba zokhala mu mpanda. Woyang’anira dera wina ndi ofalitsa angapo anafika panyumba zisanu ndi ziŵiri mwa njira imeneyi. Pa iliyonse, anauza woyang’anira wake kuti ngakhale kuti sanali ololedwa kufika panyumbazo m’njira yathu yozoloŵereka, sanafune kuti iye aphonye chidziŵitso chimene chili m’magazini atsopano. Oyang’anira a nyumba zisanu ndi ziŵiri zonsezo analandira mokondwa magazini napemphanso kuwabweretsera makope otsatira! Ndiyeno anthu okhala m’nyumba zimenezo amawafikira mwa kuwaimbira telefoni.
34 Yesetsani Kulalikira Paliponse: Kuchita mogwirizana ndi kudzipatulira kwathu kumaphatikizapo kuchita mofulumira ntchito yathu ya kulalikira uthenga wa Ufumu. Kuti tifikire anthu panthaŵi imene ili yabwino kwa iwo, tifunikira kuika pambali zokonda zathu ‘kuti paliponse tikapulumutse ena.’ Atumiki onse odzipatulira a Yehova akufuna kukhala okhoza kunena monga momwe mtumwi Paulo ananenera kuti: “Ndichita zonse chifukwa cha uthenga wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nawo.”—1 Akor. 9:22, 23.
35 Paulo anawonjezera kulemba kuti: “Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m’maufooko anga, kuti mphamvu ya Kristu ikhale pa ine [monga hema, NW]. . . . Pakuti pamene ndifooka, pamenepo ndili wamphamvu.” (2 Akor. 12:9, 10) Mwa mawu ena, palibe aliyense wa ife amene angachite ntchito imeneyi m’nyonga za ife eni. Tifunikira kupemphera kwa Yehova kuti atipatse mzimu wake woyera wamphamvu. Ngati tipemphera kwa Mulungu kaamba ka nyonga, tingakhale ndi chidaliro chakuti adzayankha mapemphero athu. Pamenepo chikondi chathu pa anthu chidzatisonkhezera kufunafuna mipata ya kulalikira uthenga wabwino kwa iwo, kulikonse kumene angapezeke. Bwanji osayesa limodzi la malingaliro ofotokozedwa mu mphatika ino, mlungu umene ukudzawu?