Lalikirani Ufumu
1 Pa Ahebri 10:23, NW, tikulimbikitsidwa ‘kugwiritsa chilengezo chapoyera cha chiyembekezo chathu.’ Ndipo chiyembekezo chathu nchozikidwa pa Ufumu wa Mulungu. Yesu mosapita m’mbali analamula kuti uthenga wabwino wa Ufumu uyenera kulalikidwa m’mitundu yonse. (Marko 13:10) Tiyenera kukumbukira zimenezi pamene tili mu utumiki wathu.
2 Pamene tikumana ndi anthu, timayesa kuyambitsa makambitsirano a zinthu zimene zimawakondweretsa kapena kuwakhudza. Nthaŵi zambiri timatchula zinthu zimene akudziŵa bwino, monga upandu m’chitaganya, zothetsa nzeru za achichepere, nkhaŵa ponena za kupeza zofunika za moyo, kapena kusokonezeka kwa zinthu m’dziko. Popeza kuti anthu ochuluka asumika maganizo awo pa “zosamalira za moyo” zimenezi, pamene tisonyeza kuti tili odera nkhaŵa ndi achifundo, anthu nthaŵi zambiri adzatiuza zimene akuganiza. (Luka 21:34) Zimenezi zingatsegule njira yowauzira za chiyembekezo chathu.
3 Komabe, ngati sitisamala, kukambitsiranako kungakhale kwa zinthu zosalimbikitsa zokhazokha kwakuti tingalephere kukwaniritsa chifuno cha ulendo wathu—kulalikira uthenga wa Ufumu. Ngakhale kuti timatchula mikhalidwe yoipa imene imadzetsa chisoni chachikulu, cholinga chathu ndicho kuwasonyeza Ufumu, umene udzathetseratu mavuto onse a anthu. Tilidi ndi chiyembekezo chabwino kwambiri chimene anthu afunikira kwambiri kumva. Chotero pamene kuli kwakuti poyamba tingakambitsirane za mbali zina za “nthaŵi zoŵaŵitsa” zimenezi, mwamsanga tiyenera kusumika maganizo pa uthenga wathu wofunikawo, “uthenga wabwino wosatha.” Mwanjira imeneyi tidzakwaniritsa utumiki wathu.—2 Tim. 3:1; 4:5; Chiv. 14:6.