Timauza Ena Chiyembekezo Chathu cha Ufumu
1 M’masiku ovuta otsiriza ano, anthu ambiri m’dzikoli alibe chiyembekezo. (Aef. 2:12) Mopanda nzeru, ena amadalira kwambiri chuma, anthu olamulira, sayansi yamakono, ndi zinthu zina. Ndifetu osangalala kwambiri kuti tili ndi chiyembekezo chenicheni cha m’tsogolo, chiyembekezo chomwe ndi ‘nangula wa miyoyo yathu, chotsimikizika, ndiponso chokhazikika.’—Aheb. 6:19.
2 Mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, dziko lapansi lidzasandutsidwa paradaiso. Okondedwa athu omwe anamwalira adzaukitsidwa. (Mac. 24:15) Sikudzakhalanso umphawi, kupanda chilungamo, matenda, ukalamba, ndi imfa. (Sal. 9:18; Mat. 12:20, 21; Chiv. 21:3, 4) Amenewa ndi ena mwa malonjezo a Yehova amene akwaniritsidwe posachedwapa. Pazinthu zimene tikuyembekezerazi, kodi n’chiyani chimene inuyo mukulakalaka kwambiri?
3 Lengezani Uthenga Wabwino: Chiyembekezo chathu cha Ufumu sitiyenera kungokhala nacho tokha. Kukonda Mulungu ndi anthu anzathu kumatipangitsa kuti titsanzire Yesu ndiponso ‘kuti tilengeze uthenga wabwino kwa osauka, kulalikira za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo, ndi za kuchiritsidwa kwa akhungu. Inde, kumasula oponderezedwa kuti apite monga mfulu.’ (Luka 4:18) Mtumwi Paulo anali kulalikira uthenga wabwino pa msika ndiponso kulikonse kumene anthu ankapezeka. Anali kutanganidwa kwambiri ndi utumiki. (Mac. 18:5) Tikamatsanzira chitsanzo chake cha kukhala achangu mu utumiki, chiyembekezo chathu chachikhristu sichidzazilala chifukwa cha “nkhawa za m’dongosolo lino la zinthu, ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma.”—Maliko 4:19.
4 Chiyembekezo chathu cha Ufumu sichizilala tikamakumana ndi anthu amene safuna kumvetsera uthenga wa Ufumu, kapena amene alibe chidwi, kayanso amene amatitsutsa. Timalimbikira “osagwedezeka pa kulengeza poyera chiyembekezo chathu.” (Aheb. 10:23) Sitichita nawo “manyazi uthenga wabwino.” (Aroma 1:16) Tikamachita zinthu motsimikiza mtima ndiponso tikamalimbikirabe, anthu ena mwina angayambe kumvetsera.
5 Ngakhale kuti nthawi zina timatchula zinthu zimene zikuipiraipira m’dzikoli, zomwe zikukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo, uthenga umene timalalikira si wonena za tsoka. Utumiki wathu umanena za chiyembekezo chathu cha Ufumu. Inde, timanena za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Motero tiyeni tizilalikira uthenga wabwino umenewu motsimikiza mtima ndiponso mwachangu ‘kuti tikhale ndi chitsimikizo chonse cha chiyembekezocho mpaka mapeto.’—Aheb. 6:11.