Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira November 12
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Chitani zitsanzo za mmene tingagawirire Nsanja ya Olonda ya November 15 ndi Galamukani! ya November pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 4 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu. M’zitsanzo zonse, gawirani magazini onse awiri ngakhale kuti mwachita chitsanzo cha magazini imodzi yokha.
Mph.15: “Siliva Ndi Wanga, Golidi Ndi Wanga.” Nkhani yokambidwa ndi mkulu yochokera mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2007, patsamba 17 mpaka 21.
Mph.20: “Yendani Monga Anthu Anzeru.”a Ngati nthawi ilipo, pemphani omvera kuti apereke ndemanga pa malemba osagwidwa mawu.
Mlungu Woyambira November 19
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Tchulani buku logawira mu December, ndipo chitani chitsanzo cha momwe tingagawirire bukuli.
Mph.15: Zosowa za pampingo.
Mph.20: “Musalephere Kuchititsa Phunziro la Baibulo.”b Pokambirana ndime 5, pemphani anthu amene ophunzira awo panopa ali m’choonadi kuti apereke ndemanga. Kodi kuchititsa phunziro la Baibulo lopita patsogolo n’kosangalatsa motani? Mungauziretu wofalitsa mmodzi kapena awiri kuti adzalankhulepo.
Mlungu Woyambira November 26
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la ndalama za mpingo wanu ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa sitetimenti. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa November. Chitani zitsanzo za mmene tingagawirire Nsanja ya Olonda ya December 1 ndi Galamukani! ya December pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 4 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu.
Mph.15: Kodi Mungafutukule Chikondi Chanu? Nkhani yokambidwa ndi mkulu yochokera mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 2007, patsamba 9 mpaka 11.
Mph.20: Kodi Achinyamata Mungatamande Bwanji Yehova? Kambiranani nkhani ya mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2005, patsamba 26 mpaka 28, ndime 15 mpaka 19 pogwiritsa ntchito mafunso a mu nkhaniyo. Pokambirana ndime 18, pemphani achinyamata mwa omverawo kunena zimene amachita kuti alalikire kwa anzawo akusukulu kapena aphunzitsi awo.
Mlungu Woyambira December 3
Mph.15: Zilengezo za pampingo. Musankhe zilengezo zina mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Kambiranani Bokosi la Mafunso.
Mph.15: Sukulu Imene Ophunzira Ake Amathandiza Anthu Padziko Lonse. Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 2006, patsamba 10 mpaka 13. Phatikizanipo ndemanga zachidule za mkulu kapena mtumiki wothandiza wina aliyense mu mpingomo amene anapita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki. Kodi sukuluyi inawathandiza bwanji kukhala alaliki, abusa, ndi aphunzitsi abwino? Limbikitsani abale amene akuyenerera kuganizira zokhala ndi cholinga chopita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki.
Mph.15: “Timauza Ena Chiyembekezo Chathu cha Ufumu.”c Ngati nthawi ilipo, pemphani omvera kuti apereke ndemanga pa malemba osagwidwa mawu.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.