PHUNZIRO 34
Khalani Wolimbikitsa
UTHENGA umene tatumidwa kuulalikira ndi uthenga wabwino. Yesu anati: “Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.” (Marko 13:10) Yesu mwiniyo anapereka chitsanzo mwa kulalikira “Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu.” (Luka 4:43) Zimene atumwi analalikira zinalinso “Uthenga Wabwino wa Mulungu” ndi “Uthenga Wabwino wa Kristu.” (1 Ates. 2:2; 2 Akor. 2:12) Uthenga woterowo ndi wolimbikitsa.
Mogwirizana ndi chilengezo cha “Uthenga Wabwino wosatha” wolengezedwa ndi “mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga,” timalimbikitsa anthu kuti: “Opani Mulungu, m’patseni ulemerero.” (Chiv. 14:6, 7) Timauza anthu kulikonse za Mulungu woona, dzina lake, makhalidwe ake abwino, ndi ntchito zake zodabwitsa. Timawauzanso zolinga zake zachikondi, kuti iye adzatifunsa za makhalidwe athu, komanso zimene amafuna kwa ife. Uthenga wabwinowo umaphatikizapo mfundo yakuti Yehova Mulungu adzawononga oipa, omwe amam’nyoza ndi kuvutitsa moyo wa anthu anzawo. Koma si kwa ife kuweruza anthu amene timawalalikira. Mtima wathu umakhumba kuti anthu ambiri alabadire uthenga wa m’Baibulo kotero kuti ukhaledi uthenga wabwino kwa iwo.—Miy. 2:20-22; Yoh. 5:22.
Chepetsani Nkhani Zosakondweretsa. N’zoona kuti moyo uli ndi mbali zake zosakondweretsa. Si bwino kuzipeŵa osazitchula m’pang’ono pomwe ngati kuti zimenezo kulibe. Pofuna kuyamba kucheza ndi munthu, mungatchule vuto limene anthu ambiri akuliganizira m’gawo lanu ndipo kambiranani mwachidule. Koma kulankhula kwambiri za vutolo kulibe phindu lenileni. Nthaŵi zonse anthu amamva nkhani zovutitsa mtima, choncho kulankhula zinthu zosakondweretsa kungawatseke makutu. Musanapite patali m’kukambirana kwanu, loŵetsani nkhani yanu ku mfundo zotsitsimutsa za Mawu a Mulungu. (Chiv. 22:17) Pamenepo, ngakhale kuti munthuyo sakufuna kuti mupitirize kukambirana, mumakhala mutamusiyira nkhani yolimbikitsa yoti aiganizire. Zimenezi zingam’chititse kukhala womvetsera ulendo wina.
Mofananamo, ngati mwapemphedwa kukakamba nkhani, musapanikize omvera mwa kuwafotokozera zinthu zosakondweretsa zokhazokha chifukwa chakuti zilipo zambiri. Ngati wokamba nkhani aima kwambiri pa mfundo ngati zakulephera kwa olamulira aumunthu, malipoti a zaupandu ndi ziwawa, ndi kufalikira komvetsa chisoni kwa chiwerewere, angawafoole omvera ake. Yambani nkhani ndi mfundo yosakondweretsa kokha pamene muli ndi cholinga chabwino. Kuchepetsa mfundo zoterozo kungachititse nkhani yanu kukhala yoyenera nthaŵi iliyonse. Kungasonyezenso mbali zazikulu zochititsa mkhalidwe winawake moti mungazigwiritse ntchito poonetsa chifukwa chake njira ya m’Baibulo ili yothandiza. Ngati n’kotheka, lankhulani molunjika mosaima kwambiri pa mavutowo.
Kaŵirikaŵiri zimakhala zosatheka kupeŵeratu mfundo zosakondweretsa zonse m’nkhani, komanso si bwino kutero. Vuto limakhala kulinganiza bwino mfundo zosangalatsa ndi zosasangalatsa kotero kuti zipange nkhani imodzi yolimbikitsa. Pofuna kuchita zimenezo, dziŵani zofunika kulankhula, zofunika kusalankhula, ndi zofunika kugogomeza. Mu Ulaliki wa pa Phiri, Yesu analangiza omvera ake kupeŵa njira zadyera zofuna kudzikondweretsa za alembi ndi Afarisi ndipo anatchula zitsanzo zingapo pofuna kumveketsa mfundo yakeyo. (Mat. 6:1, 2, 5, 16) Komabe, m’malo mongolankhula za zitsanzo zoipa za atsogoleri achipembedzowo, Yesu anagogomeza kufunika kozindikira njira zoona za Mulungu ndi kuzitsatira. (Mat. 6:3, 4, 6-15, 17-34) Zimenezo zinali zolimbikitsa kwambiri kwa omvera.
Mawu Anu Azimveka Olimbikitsa. Ngati mwapatsidwa nkhani mu mpingo wanu yokhudza mbali ina ya utumiki wachikristu, yesani kulankhula molimbikitsa osati mosuliza. Onetsetsani kuti inunso mumachita zimene mukulimbikitsa anzanu. (Aroma 2:21, 22; Aheb. 13:7) Mphamvu yanu ya kulankhula izichokera m’chikondi, osati m’kukhumudwa. (2 Akor. 2:4) Ngati muli ndi chidaliro chakuti okhulupirira anzanu amafunadi kum’kondweretsa Yehova, zimene munena zimasonyeza chidalirocho, ndipo zimenezo zimakhala zolimbikitsa kwambiri. Taonani mmene mtumwi Paulo anasonyezera chidaliro chimenecho pa 1 Atesalonika 4:1-12; 2 Atesalonika 3:4, 5; ndi Filemoni 4, 8-14, 21.
Nthaŵi zina akulu amafunikira kupereka chenjezo pa makhalidwe osayenera. Koma kukhala odzichepetsa n’kumene kungawathandize kuchita ndi abale awo mwa mzimu wa chifatso. (Agal. 6:1) Mmene anenera zinthu ayenera kusonyeza kuti amaona ena mu mpingo mwa ulemu. (1 Pet. 5:2, 3) Baibulo limalangiza amuna achinyamata makamaka kuti azisamala mfundo imeneyi. (1 Tim. 4:12; 5:1, 2; 1 Pet. 5:5) Kutakhala kofunikira kudzudzula, kulangiza, kuwongola zinthu, akuchite motsatira zimene Baibulo limanena. (2 Tim. 3:16) Wokamba nkhani asakokere Malemba kapena kuwakhotetsa kuti aoneke ngati akuvomereza maganizo amene iye amawalimbikitsa kwambiri. Ngakhale uphungu utakhala wofunikira, kamvekedwe ka nkhani kakhoza kukhalabe kolimbikitsa ngati atsindika kwambiri za mmene tingapeŵere cholakwa, njira zothetsera kusiyana maganizo, mmene tingathanire ndi zovuta, mmene tingawongolere cholakwa, ndi mmene kuchita zimene Yehova amafuna kumatitetezera.—Sal. 119:1, 9-16.
Pokonzekera nkhani yanu, ganizirani mosamala mmene mungamalizire mfundo yaikulu iliyonse komanso nkhani yonseyo. Zimene mumatsirizira kunena n’zimene zimakumbukika kwa nthaŵi yaitali. Kodi zidzakhala zolimbikitsa?
Pocheza ndi Okhulupirira Anzathu. Atumiki a Yehova amasangalala kukhala ndi mpata wolimbikitsana pa misonkhano yachikristu. Zimenezi ndi nthaŵi za chitsitsimutso chauzimu. Baibulo limati tizikumbukira “kulimbikitsana wina ndi mnzake” pamene tisonkhana m’malo athu olambirira. (Aheb. 10:25, NW) Timachita zimenezo, si mwa nkhani zokha ndi ndemanga pamisonkhano, komanso mwa kucheza misonkhano isanayambe ndi pambuyo pake.
Ngakhale kuti n’kwabwinonso kucheza nkhani zokhudza moyo wathu wa tsiku ndi tsiku, timalimbikitsana kwambiri pamene ticheza nkhani zauzimu. Nkhani zimenezo zingaphatikizepo zokumana nazo zosangalatsa mu utumiki wopatulika. Kukhalanso ndi chidwi kulinga kwa wina ndi mnzake kumakhalanso kolimbikitsa.
Koma chifukwa cha makhalidwe oipa a dziko lotizingali, m’pofunika kukhala osamala. Mtumwi Paulo, polembera Akristu a ku Efeso anati: “Mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake.” (Aef. 4:25) Kulankhula zoona m’malo mwa zonama kumaphatikizapo kusapereka ulemerero ku zinthu ndi anthu amene dziko limapembedza. Mofananamo, Yesu anachenjeza za “chinyengo cha chuma.” (Mat. 13:22) Choncho, tizisamala pocheza kuti tisalimbikitse chinyengo chimenecho mwa kukokomeza ubwino wokhala ndi chuma chakuthupi.—1 Tim. 6:9, 10.
Polangiza zokhala olimbikitsana, mtumwi Paulo akutichenjeza kuti tisaweruze kapena kusuliza mbale amene angakane kuchita zinthu zina chifukwa chokhala “wofooka m’chikhulupiriro,” kutanthauza wosazindikira mokwanira ufulu wa Mkristu pankhaniyo. Koma pofuna kuti kucheza kwathu kukhale kolimbikitsa ena, tiyenera kuganizira mmene analili m’mbuyomu ndi msinkhu wake wauzimu. Kungakhale komvetsa chisoni kwambiri, ‘kuika pa njira ya mbale [kapena mlongo], chokhumudwitsa kapena chopunthwitsa’!—Aroma 14:1-4, 13, 19.
Mwachitsanzo, aja amene akulimbana ndi mavuto aakulu ngati matenda osatheratu, amayamikira kucheza nawo nkhani zolimbikitsa. Munthu wotero angayesetse zolimba kuti afike ku misonkhano. Ena odziŵa za moyo wake angafunse kuti: “Kaya mukupezako bwanji?” Ndithudi, adzayamikira nkhaŵa yawo. Komabe, kukambirana za moyo wake sangakuone kukhala kolimbikitsa. Chimene chingam’sangalatse ndi kumuyamikira ndi kumuthokoza. Kodi pali zinthu zoonetsa kuti akupitirizabe kum’konda Yehova ndi kuti amatha kupirira pokumana ndi zovuta? Kodi amakulimbikitsani akamapereka ndemanga? Kodi sikungakhale kom’limbikitsa kum’thokoza pa zinthu zimene amachita bwino ndi mmene amathandizira mpingo, kusiyana n’kulankhula pa zofooka zake?—1 Ates. 5:11.
Kuti macheza athu azikhala olimbikitsa, m’pofunika kwambiri kukumbukira mmene Yehova amaonera zimene tikukambirana. Mu Israyeli wakale, anthu amene analankhula motsutsana ndi oimira Yehova ndi kudandaula za mana, anakumana ndi mkwiyo woopsa wa Mulungu. (Num. 12:1-16; 21:5, 6) Ngati tilemekeza akulu ndi kuyamikira chakudya chauzimu chogaŵiridwa kudzera ku gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, tidzasonyeza kuti tapinduladi ndi zitsanzo zimenezo.—1 Tim. 5:17.
Siliyenera kukhala vuto kupeza nkhani za phindu zokambirana pamene tili ndi abale athu achikristu. Komabe, ngati wina ayamba kusuliza kwambiri, tsatirani nzeru yoloŵetsapo nkhani ina yolimbikitsa.
Kaya tikulalikira anthu, kulankhula pa pulatifomu, kapena kucheza ndi okhulupirira anzathu, tichite mosamala kuti titulutse m’chuma cha m’mitima yathu, ‘nkhani yabwino yomangirira monga kufunika kuti ipatse chisomo iwo akumva.’—Aef. 4:29.