Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be tsamba 62-tsamba 65 ndime 4
  • Mmene Mungakulitsire Luso la Kucheza ndi Anthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungakulitsire Luso la Kucheza ndi Anthu
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yambirani Panyumba
  • Kucheza ndi Munthu Wosam’dziŵa
  • Mmene Mungapitirizire Kucheza Kwanu
  • Pamene Muli ndi Okhulupirira Anzanu
  • Makambirano Olimbikitsa
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Mmene Tingayambire Ulaliki Wamwamwayi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Kodi Ndingakulitse Bwanji Luso Lolankhulana Ndi Anthu?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kusiya Kukambirana ndi Munthu
    Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be tsamba 62-tsamba 65 ndime 4

Mmene Mungakulitsire Luso la Kucheza ndi Anthu

KODI zimakhala zosavuta kwa inu kucheza ndi anthu? Kwa anthu ambiri, kungoganiza zoyamba kucheza, makamaka ndi munthu amene sakum’dziŵa, ndi chinthu chodetsa nkhaŵa kwambiri. Anthu otero angakhale amanyazi. Iwo amavutika kuti: ‘Ndikamba nkhani yanji? Kodi ndiiyamba bwanji? Nanga ndiipitiriza bwanji?’ Koma anthu achidaliro ndi okonda kucheza amachita dyera ndi kulankhula. Vuto lawo limakhala kulephera kulimbikitsa anzawo kulankhula, komanso sadziŵa kumvetsera zimene zikulankhulidwa. Choncho tonsefe, kaya ndife amanyazi kapena okonda kulankhula, tiyenera kupitiriza kukulitsa luso la kucheza ndi anthu.

Yambirani Panyumba

Kuti mukulitse luso lanu locheza ndi anthu, bwanji osayambira panyumba? Kucheza nkhani zolimbikitsana kumawonjezera chimwemwe m’banja.

Chinsinsi chachikulu cha kucheza koteroko ndicho kuganizirana kochokera pansi pa mtima. (Deut. 6:6, 7; Miy. 4:1-4) Ngati tiganizirana wina ndi mnzake, timalankhulana, timamvetsera pamene wina afuna kunena kanthu. China chofunika ndicho kukhala ndi nkhani yonena yopindulitsa. Ngati tiŵerenga Baibulo ndi kuliphunzira nthaŵi zonse, timakhala ndi zambiri zouzako ena. Kugwiritsanso ntchito bwino kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku kungalimbikitsenso makambirano. Mwina patsikulo takumana ndi chochitika chosangalatsa mu utumiki wa kumunda. Kapena tingaŵerenge nkhani ina yopindulitsa kapena yoseketsa. Tikhale ndi chizoloŵezi chomasimba zinthu ngati zimenezo pocheza ndi a pabanja pathu. Zimenezi zidzatithandizanso kumacheza ndi anthu a kunja kwa banja lathu.

Kucheza ndi Munthu Wosam’dziŵa

Anthu ambiri amaopa kuyamba kucheza ndi munthu amene sakum’dziŵa. Koma chifukwa cha chikondi chawo kwa Mulungu ndi mnansi wawo, a Mboni za Yehova amayesetsa kuphunzira machezedwe pofuna kuti azikambirana za choonadi cha Baibulo ndi anthu ena. Kodi chingakuthandizeni n’chiyani kupita patsogolo pambali imeneyi?

Mfundo yotchulidwa pa Afilipi 2:4 ndi yopindulitsa kwabasi. Pamenepo akutilimbikitsa ‘kusapenyerera zathu zokha, koma yense apenyererenso za mnzake.’ Titere kunena kwake: Mwakumana ndi munthu amene simunamuonepo chikhalire. Iyenso sakukudziŵani. Kodi mungatani kuti akhale womasuka? Kumwetulira mwachikondi ndi kupereka moni waubwenzi kungathandize. Koma pali mbali zinanso zofunika kuziganizira.

Mwina mwadodometsa malingaliro ake. Ngati muyamba kukambirana naye za m’maganizo mwanu, osasamala zimene angakhale nazo m’maganizo mwake, kodi adzalabadira mokondwa? Kodi Yesu anachitanji pamene anakumana ndi mkazi pachitsime ku Samariya? Maganizo a mkaziyo anali pa kutunga madzi. Yesu anayamba kucheza naye pankhani ya madzi yomweyo, kenako anasinthira nkhaniyo ku makambirano ochititsa chidwi a zinthu zauzimu.—Yoh. 4:7-26.

Ngati mukhala tcheru, inunso mutha kuzindikira zimene anthu angamalingalire. Kodi munthuyo akuoneka wosangalala kapena wachisoni? Kodi ndi wokalamba, mwina wolemalanso? Kodi mukuona zizindikiro zakuti panyumbapo pali ana? Kodi munthuyo akuoneka kuti akupeza bwino m’zachuma kapena akuoneka kuti zimam’vuta kupeza zofunika za moyo? Kodi zokongoletsa panyumbapo ndi zokoloŵekakoloŵeka m’thupi zikuonetsa chipembedzo cha munthuyo? Ngati mukhudza zinthu ngati zimenezi polonjerana naye, munthuyo adzaona kuti mukulingalira zimene iyenso amadziŵa.

Ngati simuonana ndi mwininyumba pamasom’pamaso, mwina mungomva mawu ake kumbuyo kwa chitseko chokhoma, kodi mungaganize chiyani? Mwina munthuyo ali ndi mantha. Kodi mungayambe kucheza naye pamfundo yokhudza mantha kudzera pachitseko chokhomacho?

M’madera ena zimatheka kukopa chidwi cha munthu ndi kuyamba kucheza naye mwa kum’fotokozera za inu mwini—kumene mukuchokera, chimene mwafikira pakhomo pake, chifukwa chake mumakhulupirira Mulungu, chimene chinakuyambitsani kuphunzira Baibulo, ndi mmene Baibulo lakuthandizirani. (Mac. 26:4-23) Komatu m’pofunika kusamala pochita zimenezi, ndipo kumbukirani bwino lomwe cholinga chanu. Mukatero, munthuyo angakhale ndi chidwi chokufotokozerani kanthu kena kokhudza iye ndi maganizo ake pankhaniyo.

M’mayiko ena, kuchereza alendo ndi mwambo wa chikhalidwe chawo. Anthu angakupempheni mwaulemu kuti muloŵe m’nyumba ndi kukhala pansi. Mutakhala pansi, ngati polonjerana nawo mufunsa za moyo wa banja ndi kumvetsera mwachidwi pamene akuyankha, mwininyumbanso amamvetsera mwachidwi zimene mwam’tengera. Anthu ena amakhala ndi chidwi chachikulu ndi alendo, choncho kulonjerana kwanu kungakhale kotalikirapo. M’kulonjeranako, angapeze kuti amafanana nanu m’zinthu zina. Zimenezi zingatsogolere ku makambirano opindulitsa pa zinthu zauzimu.

Bwanji ngati kudera kwanuko kuli anthu olankhula zinenero zina? Kodi anthu otero mungawafikire motani? Ngati mungaphunzire ngakhale moni wosavuta m’zinenero zawo, anthuwo adzaona kuti mumawaganizira. Zimenezi zingatsegule mpata wakumacheza nawo.

Mmene Mungapitirizire Kucheza Kwanu

Kuti mupitirize kuchezako, khalani ndi chidwi pa malingaliro a munthu winayo. M’limbikitseni kunena maganizo ake ngati akufuna kutero. Mafunso osankhidwa bwino angathandize. Mafunso opempha malingaliro ali bwino kwambiri chifukwa kaŵirikaŵiri amapangitsa munthu kunena zambiri, m’malo mongoyankha kuti inde kapena ayi. Mwachitsanzo, mutatchula vuto lokhudza ambiri m’deralo, mungafunse kuti: “Mukuganiza kuti n’chiyani chachititsa zimenezi?” kapena kuti “Kodi mukuganiza kuti njira yothetsera vutoli n’chiyani?”

Pamene mwafunsa funso, mvetserani yankho. Sonyezani chidwi chanu chenicheni mwa kulabadira ndi mawu, ndi mutu, kapena ndi manja. Musamudule. Lingalirani moona mtima zimene akunenazo. Khalani “wotchera khutu, wodekha polankhula.” (Yak. 1:19) Pamene muyankha, onetsani kuti munali kumveradi zimene anali kulankhula.

Komabe, dziŵani kuti si aliyense amene angayankhe mafunso anu. Anthu ena angangolabadira ndi maso kapena mwa kumwetulira. Ena angangoyankha kuti inde kapena ayi. Musagwe mphwayi. Lezani mtima. Musayese kumuumiriza kucheza. Ngati munthuyo akufuna kumvetsera, gwiritsani ntchito mwayiwo kugaŵana naye malingaliro olimbikitsa a m’Malemba. M’kupita kwa nthaŵi, munthuyo angakuoneni kukhala bwenzi lake. Mwina pamenepo angakhale womasukirapo kukuuzani maganizo ake.

Polankhulana ndi anthu, ganizirani za m’tsogolo. Ngati munthuyo afunsa mafunso angapo, yankhani ena a iwo koma siyani limodzi kapena aŵiri odzakambirana ulendo wina. M’pempheni kuti mukafufuze, kenako mudzam’fotokozere zimene muti mukapeze. Ngati safunsa mafunso, mungatsirize kucheza kwanu ndi funso limene muganiza kuti lingam’patse chidwi. Lonjezani kudzakambirana funsolo ulendo wotsatira. Mfundo zopindulitsa mungazipeze m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba, bulosha lakuti Mulungu Amafunanji kwa Ife?, ndi magazini aposachedwa a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!

Pamene Muli ndi Okhulupirira Anzanu

Pamene mwakumana ndi mnzanu wa Mboni za Yehova kwa nthaŵi yoyamba, kodi mumayamba kum’lankhula kuti mudziŵane naye? Kapena mumangoima pambali pake duu osalankhula chilichonse? Chikondi cha ubale chiyenera kutipatsa chidwi chakuti tidziŵane naye. (Yoh. 13:35) Nanga mungayambe bwanji? Mungatchule dzina lanu kenako kum’funsa lake. Kum’funsa mmene anaphunzirira choonadi kaŵirikaŵiri kumayambitsa kucheza kosangalatsa ndipo mumadziŵana bwino. Ngakhale simukulankhula mwaluso kwenikweni, khama lanulo limaonetsa munthuyo kuti mukusamala za iye, ndipo chimenecho ndiye chofunika kwambiri.

Kodi n’chiyani chingathandize kucheza bwino ndi munthu wa mumpingo wanu? Onetsani chidwi chenicheni pa munthuyo ndi banja lake. Kodi mwangotha kumene msonkhano? Lankhulani mfundo zimene mwaziona kukhala zothandiza. Zimenezi zingakhale zothandiza kwa nonse aŵiri. Mungatchule mfundo yochititsa chidwi ya m’magazini ya posachedwa ya Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Musachite zimenezi modzionetsera kapena kuyesa chidziŵitso cha mnzanu. Cholinga chanu chizikhala kugaŵirako mnzanuyo mfundo yosangalatsa imene mwaipeza. Mungalankhule za nkhani imene mmodzi wa inu ali nayo m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndi kupatsana maganizo za kakambidwe kake. Mungasimbiranenso zokumana nazo za mu utumiki wa kumunda.

N’zoona kuti chidwi chathu pa anthu kaŵirikaŵiri chimatipangitsa kucheza nkhani zokhudza anthu—zimene amanena ndi kuchita. Timalankhulanso zoseka. Kodi zimene tilankhule zidzakhala zomangirira? Ngati tilabadira uphungu wa Mawu a Mulungu ndipo ngati tilimbikitsidwa ndi chikondi chaumulungu, zolankhula zathu zizikhala zomangirira.—Miy. 16:27, 28; Aef. 4:25, 29; 5:3, 4; Yak. 1:26.

Tisanaloŵe mu utumiki wa kumunda, timakonzekera choyamba. Bwanji osakonzekera kankhani kosangalatsa kokauzako anzanu? Pamene muŵerenga ndi kumvera zinthu zosangalatsa, sungani mfundo zimene mungafune kuuzako ena. M’kupita kwa nthaŵi, mudzakhala ndi nkhokwe yosankhamo. Kuchita zimenezo kudzakuthandizani kukhala ndi nkhani zambiri zocheza kuwonjezera pa zochitika za tsiku ndi tsiku. Choposa zonse, onetsetsani kuti malankhulidwe anu akupereka umboni wakuti Mawu a Mulungu ndi amtengo wapatali kwa inu!—Sal. 139:17.

NJIRA ZOYAMBIRA KUCHEZA NDI ANTHU

  • Tsatirani chikhalidwe cha kumaloko

  • Yamikirani moona mtima

  • Funsani mafunso opempha malingaliro

MAKHALIDWE OTHANDIZA

  • Khalani wosangalala

  • Waubwenzi ndi woona mtima

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena