Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 124
  • Kodi Ndingakulitse Bwanji Luso Lolankhulana Ndi Anthu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingakulitse Bwanji Luso Lolankhulana Ndi Anthu?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa chiyani ndiyenera kulankhulana ndi anthu pamasom’pamaso?
  • Ndingayambe bwanji kukambirana ndi anthu?
  • Mmene Mungakulitsire Luso la Kucheza ndi Anthu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Mmene Tingayambire Ulaliki Wamwamwayi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Makambirano Olimbikitsa
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kuchita Chidwi ndi Anthu
    Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 124
Mnyamata akucheza ndi anzake akusukulu pa nthawi yopuma.

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingakulitse Bwanji Luso Lolankhulana Ndi Anthu?

Munkhaniyi muli

  • N’chifukwa chiyani ndiyenera kulankhulana ndi anthu pamasom’pamaso?

  • Ndingayambe bwanji kukambirana ndi anthu?

  • Zimene anzanu amanena

N’chifukwa chiyani ndiyenera kulankhulana ndi anthu pamasom’pamaso?

Anthu ena amaona kuti ndi zovuta komanso zochititsa mantha kulankhulana ndi anthu pamasom’pamaso poyerekezera ndi kulemberana mameseji.

“Zimakhala zovuta kusintha zomwe wanena ukamalankhulana ndi anthu pamasom’pamaso chifukwa sungakonze kapena kufufuta chilichonse pa zomwe wanena.”​—Anna.

“Kulemberana mameseji kuli ngati kuonera pulogalamu yojambulidwa kale pomwe kulankhulana pamasom’pamaso kuli ngati kuonera pulogalamu yomwe ikuchitika nthawi yomweyo. Nthawi zonse ndikamalankhulana ndi munthu pamasom’pamaso ndimadziuza kuti, ‘Bwinotu ndisalakwitsepo apa!’”​—Jean.

Komabe, pa nthawi ina, mudzafunikabe kukhala ndi luso lolankhulana ndi anthu pamasom’pamaso. Mwachitsanzo, mudzafunika kukhala ndi luso limeneli kuti mupeze mabwenzi atsopano, ntchito komanso kuti mukhalitse pa ntchitopo, kapenanso mukamadzafuna kuyamba chibwenzi nthawi yanu ikadzakwana.

Komabe, simukufunika kuchita mantha kuti muyamba bwanji kukambirana ndi munthu pamasom’pamaso. Mukhoza kuphunzira kuchita zimenezi ngakhale kuti ndinu wamanyazi.

Kachizindikiro ka getsi.

Zimene zingakuthandizeni: Musamadandaule kwambiri ngati mwalakwitsa. Tingayerekezere kukulitsa luso la kulankhulana ndi kuphunzira kupalasa njinga. Mukhoza “kugwa” maulendo angapo, koma mukapitiriza kuphunzira, mungayambe kupalasa bwino kwambiri n’kumasangalala.

“Tonsefe nthawi zina timalakwitsa polankhula ndipo timachita manyazi. Choncho, musamayembekezere kuti simukufunika kulakwitsa chilichonse.”​—Neal.

Ndingayambe bwanji kukambirana ndi anthu?

  • Muzifunsa mafunso. Ganizirani nkhani imene ingasangalatse anthu kenako yambani kukambirana nawo za nkhaniyo. Mwachitsanzo:

    “Kodi holide yapitayi anzathu munapita kuti?”

    “Webusaitiyi ndi yabwino kwambiri. Kodi munaionapo?”

    “Kodi mwamva zomwe zachitika . . . ?”

    Kuti musavutike kuyamba kukambirana ndi munthu, ganizirani zinthu zina zimene mumachitira limodzi ndi munthuyo. Mwachitsanzo, kodi mumaphunzira sukulu limodzi kapenanso kugwirira ntchito limodzi? Mungagwiritse ntchito zimenezi kuti mupeze poyambira.

    Anyamata akucheza uku akudya chakudya pa nthawi yopuma. Kachithunzi komwe kali pakatipo kakusonyeza kuti akukambirana nkhani zampira.

    “Muziganizira mafunso amene inuyo mumawaona kuti ndi ochititsa chidwi komanso amene mungakonde kumva mayankho ake kuchokera kwa anthu ena.”​—Maritza.

    Kachizindikiro ka getsi.

    Zimene zingakuthandizeni: Kufunsa mafunso ngati omwe ali pamwambapa kungakuthandizeni kuti muyambe kukambirana ndi anthu. Koma ngati mungathe, muzifunsa mafunso omwe angathandize munthu kufotokoza maganizo ake, osati kungokuyankhani kuti inde kapena ayi. Mwachitsanzo, mungamufunse kuti, “Ndi mbali iti imene yakusangalatsani pa filimu taonera ija?” M’malo mofunsa kuti, “Filimu ija yakusangalatsani?”

    Chenjezo: Muzipewa kufunsa mafunso ambirimbiri nthawi imodzi moti mpaka munthu kuchita kuvutika kukuyankhani. Komanso musamafunse mafunso omwe angachititse munthu manyazi. Mafunso monga akuti, “Mudzakwatira liti?” kapenanso “N’chifukwa chiyani nthawi zonse mumavala chovala chomwechomwecho?” angachititse kuti munthu amangike. Funso lachiwirilo lingachititse munthu kuona ngati mukumuimba mlandu.

    Muyeneranso kupewa kufotokoza maganizo anu munthu wina asanayambe kuyankha funso lomwe mwamufunsa kapenanso akangomaliza kumene. Choncho, njira yabwino ndi yoti muzikambirana ndi munthu m’malo momupanikiza ndi mafunso.

    Anyamata akucheza uku akudya chakudya pa nthawi yopuma. Kachithunzi komwe kali pakatipo kakusonyeza kuti akukambirana nkhani zampira.

    Kodi mumakonda kufunsa mafunso opanikiza anthu ena?

    Mfundo ya m’Baibulo: “Maganizo amumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya, koma munthu wozindikira ndi amene amawatunga.”​—Miyambo 20:5.

  • Muzimvetsera mwatcheru. Kuti mukwanitse kumalankhulana bwino ndi anthu, muzimvetsera mwatcheru m’malo momalankhula kwambiri.

    “Ndimayesetsa kuphunzira chinachake chatsopano chokhudza munthu amene ndikulankhula naye. Kenako, sindimaiwala zimene wandifotokozera ndipo zimenezi zimandithandiza kuti ndipeze funso lomwe ndingadzamufunse tikamadzachezanso ulendo wina.”​—Tamara.

    Kachizindikiro ka getsi.

    Zimene zingakuthandizeni: Musamadandaule mukaona kuti mukusowa zoti munene. M’malo mwake muziganizira malo omwe muli. Kodi muli kusukulu, kuntchito kapena pamalo ena? Mwina mungayambe kufotokoza za zinthu zina zomwe zili pamalo omwe muli. Mwachitsanzo, mutha kufunsa mnzanu yemwe mumagwira naye ntchito kuti, “Kodi mumayenda maola angati kudzafika kuntchito kuno?”

    Chenjezo: Musadere nkhawa kuti ulendo wotsatira mudzanena zotani. Muzingomvetsera mwatcheru basi, ndipo simungavutike kunena zinazake kuchokera pa zimene munthu wina wakufotokozerani.

    Mfundo ya m’Baibulo: “Munthu aliyense azikhala wokonzeka kumvetsera, aziganiza kaye asanalankhule komanso asamafulumire kukwiya.”​—Yakobo 1:19.

  • Muzichita chidwi ndi ena. Mukamachita chidwi ndi anthu, m’pamene mungamasangalale kwambiri kucheza nawo.

    Anyamata akucheza uku akudya chakudya pa nthawi yopuma. Kachithunzi komwe kali pakatipo kakusonyeza kuti akukambirana nkhani zampira.

    “Mukamamvetsera mwatcheru zimene munthu wina akufotokoza, mumasonyeza kuti mukuchita naye chidwi ndipo zimathandiza kuti muzisangalala kucheza naye ngakhale kuti nthawi zina mukhoza kumachita manyazi.”​—Marie.

    Kachizindikiro ka getsi.

    Zimene zingakuthandizeni: Muzimuyamikira mochokera pansi pa mtima kenako muzimufunsa funso. Mwachitsanzo, “Mwavalatu juzi yokongola. Zinthu zabwinozi mumazipeza kuti anzathu?”

    Chenjezo: Musamalankhule mopitirira malire. Mwachitsanzo, kunena kuti, “Mwavalatu juzi yokongola. Ndiye munaigula ndalama zingati? kungakhale kupitirira malire.

    Mfundo ya m’Baibulo: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”​—Afilipi 2:4.

Kodi mungalankhule mawu otani pomaliza zimene mukukambirana? Mnyamata wina dzina lake Jordan ananena kuti, “Muziyesetsa kumaliza ndi mawu osangalatsa. Mwina munganene kuti, ‘Ndasangalala kwambiri kucheza nanu’, kapena ‘Ndikufunirani tsiku labwino.’ Zimenezi zingathandize kuti mudzapeze poyambira ulendo wina mukadzakumananso.”

Zimene anzanu amanena

  • Bethel.

    “Kuphunzira kucheza ndi anthu kuli ngati kuphunzira chinenero chatsopano. Poyamba zimakhala zovuta, koma mukachita khama simumavutikanso kuyamba kulankhulana ndi anthu.”​—Bethel.

  • Isaac.

    “Muzimvetsera mwatcheru munthu wina akamalankhula. Muziyang’anizana. Ngati mukufunika kuvomereza zinazake, muzigwedezera mutu. Muzimwetulira. Anthu amayamikira kwambiri mukamachita zinthu zosonyeza kuti mukuwamvetsera akamalankhula.”​—Isaac.

  • Kate.

    “Poyamba ndinkachita mantha ndikamalankhulana ndi anthu ena. Nthawi zina ndimachitabe mantha. Koma zimene zimandithandiza kwambiri ndi kuchita chidwi ndi anthu ena m’malo moganizira kwambiri mantha angawa.”​—Kate.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena