Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Mmene Tingayambire Ulaliki Wamwamwayi
N’chifukwa Chiyani Kuchita Zimenezi N’kofunika? Nthawi zina tikamalalikira kunyumba ndi nyumba, timapeza kuti anthu ambiri sali pakhomo. Koma tingathe kukumana ndi anthu amenewa m’basi, kuchipatala, pa nthawi yopuma kusukulu ndi kuntchito komanso m’malo ena. Yehova akufuna kuti anthu onse amve uthenga wa Ufumu. (1 Tim. 2:3, 4) Kuti tilalikire anthu, nthawi zambiri tiyenera kuyamba ndifeyo kulankhula nawo.
Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno:
Mlungu uliwonse, yesetsani kuyamba kulankhula ndi munthu n’cholinga choti muthe kuchita ulaliki wamwamwayi.