Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • be tsamba 66-tsamba 70 ndime 3
  • Dziŵani Mayankhidwe Oyenera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziŵani Mayankhidwe Oyenera
  • Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zindikirani Maganizo a Wofunsayo
  • Maganizo a Wofunsayo pa Malemba
  • ‘Mawu Anu Akhale Achisomo Nthaŵi Zonse’
  • Zosankha za Munthu Mwini Ndiponso Nkhani za Chikumbumtima
  • Kuyankhapo pa Misonkhano ya Mpingo
  • Kuwongolera Mayankho Anu
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Zimene Tingachite Kuti Ndemanga Zathu Zizikhala Zabwino
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Tizilimbikitsana Pamisonkhano ya Mpingo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
Onani Zambiri
Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
be tsamba 66-tsamba 70 ndime 3

Dziŵani Mayankhidwe Oyenera

MAFUNSO ena ali ngati namkholowa. Mbatata yofunikayo imabisala pansi m’nthaka. Chimodzimodzinso funso. Kaŵirikaŵiri, nkhani yake ndiyo imakhala yofunika kwambiri kuposa funsolo.

Ngakhale pamene wofunsayo ali wofunitsitsa kuti adziŵe yankho, mukadziŵa mayankhidwe oyenera mungazindikirenso kuchuluka kwa zimene muyenera kunena komanso mbali ya nkhaniyo imene muyenera kuyankha. (Yoh. 16:12) Monga momwe Yesu anasonyezera kwa atumwi ake, nthaŵi zina munthu amafunsa nkhani imene safunikira kudziŵapo kanthu, kapena imene singam’pindulitse kwenikweni.—Mac. 1:6, 7.

Malemba amatilangiza kuti: “Mawu anu akhale m’chisomo, okoleretsa, kuti mukadziŵe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.” (Akol. 4:6) Choncho, tisanayankhe, tiganizire zimene tikufuna kunena ndi mmene tiyenera kuzinenera.

Zindikirani Maganizo a Wofunsayo

Asaduki anayesa kum’kola Yesu ndi funso lonena za kuuka kwa mkazi amene anakwatiwapo nthaŵi zambiri. Komabe, Yesu anadziŵa kuti Asadukiwo sanali kukhulupirira za kuuka. Choncho poyankha, anayankha funso lawo m’njira yowongolera maganizo awo olakwika omwe anali gwero la funsolo. Polingalira mwaluso ndi powasimbira nkhani ya m’Malemba, Yesu anaunika mbali ina imene iwo sanailingalirepo m’mbuyo monsemo—umboni woonekeratu wakuti Mulungu akaukitsadi akufa. Yankho lake linawathetsa mankhalu otsutsawo ndipo anachita mantha moti sanam’funsenso.—Luka 20:27-40.

Kuti mudziŵe mayankhidwe oyenera, inunso muyenera kuzindikira maganizo ndi nkhaŵa za ofunsawo. Mwachitsanzo, mnzanu wam’kalasi kapena wakuntchito angakufunseni chimene simukondwerera Khirisimasi. Kodi akufunsiranji zimenezo? Kodi akufunadi kudziŵa chifukwa, kapena angofuna adziŵe ngati mumaloledwa kukhala ndi nthaŵi yosangalala? Kuti mudziŵe, mungafunikire kufunsa chimene wafunsira zimenezo. Ndiyeno yankhani moyenerera. Mungatengereponso mwayi wosonyeza mmene kutsatira malangizo a m’Baibulo kumatitetezera ku zotsatira za chikondwererocho zimene zakhumudwitsa anthu ambiri ndi kuwaloŵetsa m’mavuto.

Tinene kuti mwapemphedwa kulankhula za Mboni za Yehova pamaso pa gulu la ophunzira kusukulu. Mutamaliza kulankhula, iwo angakufunseni mafunso. Ngati mafunsowo akuoneka kukhala ochokera pansi pa mtima komanso osapita m’mbali, perekani mayankho osavuta ndi olunjika. Koma ngati mafunsowo akuonetsa maganizo olakwika omwe anthu ali nawo ponena za Mboni, musanapereke mayankho, mungachite bwino kulankhulapo mawu achidule amene angawongolere maganizo a ena pankhanizo, ndi chifukwa chake Mboni za Yehova zimatsatira miyezo ya Baibulo. Nthaŵi zambiri, ndi bwino kuona mafunso amenewo ngati nkhani zowadetsa nkhaŵa, osati ngati makani—ngakhale kuti angawafunse ndi mzimu umenewo. Mukatero, mayankho anu adzapereka mwayi wotsegula maganizo a omvera anu, mudzawapatsa chidziŵitso cholondola, ndipo mudzafotokoza maziko a m’Malemba a zimene timakhulupirira.

Kodi mungayankhe motani kwa bwana wanu kuntchito amene akukana kukupatsani nthaŵi yoti mukapezeke kumsonkhano? Choyamba, lingalirani nkhaniyo mmene iye akuionera. Kodi angalole kuti nthaŵi imene mukupemphayo mudzaigwirire ntchito nthaŵi ina? Ngati mum’fotokozera kuti malangizo omwe amaperekedwa kumisonkhano yathu amatithandiza kukhala antchito oona mtima ndi okhulupirika, kodi zingathandize? Ngati muonetsa kuti mukuganizira za nkhaŵa yake, mwina iyenso adzakuganizirani pa zimene waona kuti n’zofunika kwambiri pa moyo wanu. Koma bwanji ngati akufuna kuti muchite chinthu cholakwika? N’zoona kuti kukana kosapita m’mbali mwa kutchula chifukwa cha m’Malemba kungaonetse maganizo anu. Koma kodi sizingachite bwino koposa ngati choyamba mum’fotokozera kuti munthu amene angalole kunena bodza kapena kuba motumidwa ndi bwanayo, akhozanso kudzanena bodza kapena kudzam’bera bwanayo?

Komanso, mwina ndinu wophunzira amene simufuna kutenga mbali m’zochitika zina za pasukulu zotsutsana ndi Malemba. Kumbukirani, mwina mphunzitsi wanuyo sakugwirizana ndi malingaliro anu, komanso ndi udindo wake kuonetsetsa kuti kalasilo likukhala lomvera. Zikatero, mumayang’anizana ndi zinthu zovuta izi: (1) kuonetsa kuti mukumvetsa nkhaŵa ya mphunzitsiyo, (2) kufotokoza chikhulupiriro chanu mwaulemu, ndi (3) kulimbikira chimene mukudziŵa kuti Yehova adzakondwera nacho. Kuti zithe bwino, simuyenera kungotchula zimene mumakhulupirira ndi kuthera pomwepo. (Miy. 15:28) Ngati ndinu wam’ng’ono, mosakayika atate kapena amayi anu adzakuthandizani kukonzekera zoti mukanene.

Nthaŵi zina mungafunikire kutsutsa mlandu umene munthu waudindo m’boma angakuimbeni. Wapolisi, mkulu wa boma, kapena woweruza angalamule kuti muyankhe mafunso okhudza kumvera lamulo lakutilakuti, kusatenga mbali kwanu m’ndale monga Mkristu, kapena maganizo anu pa kutenga nawo mbali m’zochitika za mwambo winawake wosonyeza kukonda dziko lanu. Kodi muyenera kuyankha motani? Baibulo limalangiza kuti, “ndi chifatso ndi mantha.” (1 Pet. 3:15) Ndiponso, dzifunseni chifukwa chake nkhani zimenezi zili zofunika kwa iwo, ndipo mwaulemu vomerezani kufunika kwake. Ndiyeno muyenera kuchitanji? Mtumwi Paulo anadziteteza mwa kutchula ufulu wachibadidwe woperekedwa ndi malamulo a boma la Roma. Inunso mungadziteteze potchula ufulu wanu wachibadidwe woperekedwa ndi malamulo a boma. (Mac. 22:25-29) Mwinanso kutchula mmene Akristu oyambirira anachitira pankhani yofananayo, komanso Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse, kungathandize woimira bomayo kukhala ndi chithunzi chokwanira. Kapena mungafotokoze mmene kuzindikira ulamuliro wa Mulungu kumathandizira anthu kumvera kwambiri malamulo oyenera a ulamuliro wa anthu. (Aroma 13:1-14) Pomveketsa mfundo ngati zimenezi, chifukwa chanu cha m’Malemba chokanira mlanduwo chingalandiridwe.

Maganizo a Wofunsayo pa Malemba

Poganizira za mmene mungayankhire, muyeneranso kulingalira za maganizo a wofunsayo pa Malemba Oyera. N’zimene Yesu anachita poyankha funso la Asaduki pankhani ya kuuka kwa akufa. Yesu podziŵa kuti iwo anali kukhulupirira zolemba za Mose zokha, anakambirana nawo pankhani zolembedwa m’mabuku asanu oyambirira a m’Baibulo, akumayamba ndi mawu onena kuti: “Koma za kuti anthu akufa auka, anasonyeza ngakhale Mose.” (Luka 20:37) Kungakhalenso kothandiza kwa inu kugwira mawu kuchokera m’mbali za Baibulo zimene womvera wanu amazivomereza ndipo amazidziŵa.

Bwanji ngati womvera wanuyo Baibulo saliona kukhala lodalirika? Taonani zimene mtumwi Paulo anachita polankhula ku Areopagi, zolembedwa pa Machitidwe 17:22-31. Iye anawafotokozera mfundo za m’Malemba popanda kugwira mawu mwachindunji m’Baibulo. Kutakhala kofunikira, inunso mukhoza kutero. Nthaŵi zina, mungafunikire kucheza ndi munthu kangapo konse musanatchule Baibulo. Podzatchula Baibulo, kungakhale kwanzeru poyamba kungopereka zifukwa zina zoonetsa mmene kungakhalire koyenera kuliŵerenga. Musanene motsindika kuti ndi Mawu a Mulungu. Komabe, cholinga chanu chiyenera kukhala kupereka umboni womveka bwino wonena za chifuniro cha Mulungu, ndipo m’kupita kwanthaŵi, mudzapereka mwayi kwa womverayo kuti adzaone yekha zimene Baibulo limanena. Baibulo palokha limakhala lokopa kwambiri koposa chilichonse chimene ifeyo tinganene.—Aheb. 4:12.

‘Mawu Anu Akhale Achisomo Nthaŵi Zonse’

M’pake ndithu kuti atumiki a Yehova, Mulungu wachisomoyo, akuuzidwa kuti mawu awo ‘azikhala achisomo ndi okoleretsa.’ (Akol. 4:6; Eks. 34:6) Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kulankhula mokoma mtima, ngakhale pamene kukuoneka kukhala kosafunikira. Mawu athu azimveka okoma, osati achiwawa kapena osasamala.

Anthu ambiri ali pa chipsinjo chachikulu, ndipo tsiku ndi tsiku amazaziridwa. Pamene tifikira anthu oterowo, angatilankhule mwaukali. Kodi ifeyo tikayenera kuyankha motani? Baibulo limati: “Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo.” Mayankhidwe otero angafeŵetsenso munthu wokhala ndi maganizo otsutsa. (Miy. 15:1; 25:15) Kwa anthu amene amalankhulidwa mwachiwawa tsiku ndi tsiku, kuwaonetsa mkhalidwe ndi mawu osonyeza kukoma mtima kungakhale chinthu chosangalatsa kwambiri moti akhoza kumvetsera uthenga wabwino umene tadza nawo.

Tilibe chidwi chotsutsana ndi anthu osalemekeza choonadi. M’malo mwake, timafuna kukambirana za m’Malemba ndi anthu amene angatilole. Ngakhale titakumana ndi mkhalidwe wotani, tikumbukire kuti tikayenera kuyankha mokoma mtima komanso ndi chidaliro chakuti malonjezo okoma a Mulungu alidi odalirika.—1 Ates. 1:5.

Zosankha za Munthu Mwini Ndiponso Nkhani za Chikumbumtima

Pamene wophunzira Baibulo kapena wokhulupirira mnzathu akufunsani zimene ayenera kuchita pankhani inayake, kodi muyenera kuyankha motani? Inuyo mungadziŵe zimene mukanachita. Koma munthu aliyense ayenera kuyankha pa zimene angasankhe pamoyo wake. (Agal. 6:5) Mtumwi Paulo anafotokoza kuti analimbikitsa anthu amene anawalalikira ‘kumvera mwa chikhulupiriro.’ (Aroma 16:26) Tiyenera kutengera chitsanzo chabwino chimenechi. Munthu amene amasankha zochita makamaka pofuna kukondweretsa amene amam’phunzitsa Baibulo kapena munthu aliyense, amatumikira anthu, ndipo sakukhala mwa chikhulupiriro. (Agal. 1:10) Choncho, yankho lapafupi ndi lolunjika lingakhale losam’thandiza kwenikweni wofunsayo.

Nangano mungayankhe motani m’njira yogwirizana ndi malangizo a m’Baibulo? Mungam’fotokozere mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo ndi zitsanzo. Nthaŵi zina, mungam’sonyeze mmene angafufuzire kuti adzipezere yekha mfundo za makhalidwe abwino ndi zitsanzo zimenezo. Mukhozanso kukambirana mfundo za makhalidwe abwinozo ndi mapindu a zitsanzozo, koma musazigwiritse ntchito pa nkhani imene wafunsayo. Tam’funsani munthuyo ngati akuonapo mbali imene ingam’thandize kusankha chinthu mwanzeru. M’limbikitseni kuti aganize mmene mfundo za makhalidwe abwino ndi zitsanzozo zingam’thandizire kusankha njira imene ingakondweretse Yehova. Mukatero, mudzam’thandiza ‘kuzoloŵeretsa malingaliro ake kusiyanitsa chabwino ndi choipa.’—Aheb. 5:14.

Kuyankhapo pa Misonkhano ya Mpingo

Kaŵirikaŵiri, misonkhano ya mpingo imapereka mpata wakuti tilengeze poyera za chikhulupiriro chathu. Njira imodzi imene timachitira zimenezi ndiyo kuyankha mafunso. Kodi tiyenera kuyankha motani? Tizikhala ndi cholinga cha kutamanda Yehova, ndi kum’thokoza. N’zimene wamasalmo Davide anachita “m’masonkhano.” (Sal. 26:12) Tiyeneranso kuyankha m’njira yolimbikitsa okhulupirira anzathu, kuwafulumiza “ku chikondano ndi ntchito zabwino,” monga analangizira mtumwi Paulo. (Aheb. 10:23-25) Kuŵerenga nkhanizo nthaŵi ikalipo kungatithandize kuchita zimenezo.

Mukapatsidwa mwayi woyankhapo, perekani yankho losavuta, lomveka bwino, ndi lalifupi. Musafotokoze ndime yonse; yankhani mfundo imodzi yokha basi. Ngati muyankha mbali imodzi ya yankho, mumapereka mwayi kwa ena kuti ayankhepo mbali zinazo. N’kofunika kwambiri kulankhulapo pa malemba osagwidwa mawu pandimepo. Pamene mukutero, yesetsani kumveketsa mbali ya lembalo imene ikuchirikiza mfundo ya pa ndimepo. Phunzirani kuyankha m’mawu anuanu m’malo moŵerenga zonse pa ndime. Musakhumudwe ngati ndemanga imene mwakonzekera simunaiyankhe bwino kwenikweni. Zimenezo zimachitika kwa aliyense amene amayankhapo.

N’kwachidziŵikire kuti kudziŵa mayankhidwe oyenera kumafuna zoposa kungodziŵa yankho lenilenilo. Kumafuna kuzindikira. Koma mukapereka yankho lochokera pansi pa mtima, limenenso limakhudza mitima ya ena, zimakhala zokhutiritsa kwabasi!—Miy. 15:23.

MUSANAYANKHE, LINGALIRANI IZI

  • Mmene mungalankhulire mwaubwino komanso mwachidaliro

  • Kaya muyenera kupereka yankho lachindunji, kaya mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo, kapena zitsanzo zimene zingam’thandize kusankha yekha zimene ayenera kuchita

MMENE MUNGAYANKHIRE PA MISONKHANO

  • Ngati ndinu woyamba, perekani yankho losavuta ndi lolunjika pa funsolo

  • Powonjezera mfundo zina poyankha, (1) sonyezani mmene lemba losagwidwa mawu limachirikizira mfundo imene mukukambirana, (2) tchulani mmene nkhaniyo imakhudzira miyoyo yathu, (3) fotokozani mmene tingagwiritsire ntchito mfundozo, kapena (4) tchulani chochitika chachidule chimene chimaunika mfundo yaikulu

  • Mvetserani mosamala mayankho amene ena akupereka kuti mukhoze kuwonjezera pa zimene zanenedwa

  • Yesani kuyankha m’mawu anuanu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena