MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zimene Tingachite Kuti Ndemanga Zathu Zizikhala Zabwino
Ndemanga zabwino zimalimbikitsa mpingo komanso zimathandiza anthu omwe amazipereka. (Miy. 15:23, 28; Aroma 14:19) N’chifukwa chake tiyenera kumayesetsa kupereka ndemanga pamsonkhano uliwonse. Komabe sikuti tingapatsidwe mwayi woyankha nthawi iliyonse imene takweza mkono. Choncho tingachite bwino kumakonzekera ndemanga zingapo.
Ndemanga yabwino imakhala . . .
yosavuta, yomveka bwino komanso yachidule. Nthawi zambiri ikhoza kukhala yosapitirira masekondi 30
imene mwaifotokoza m’mawu anuanu
imene sikungobwereza zimene anthu ena ayankha kale
Ngati ndinu woyamba kuyankha funso linalake, . . .
mungoyankha funsolo mwachidule popanda kufotokoza zambiri
Ngati funso layankhidwa kale, mukhoza . . .
kusonyeza mmene lemba lina la mundimeyo likugwirizanira ndi mfundo za mundimeyo
kufotokoza mmene mfundozo zingatithandizire
kufotokoza mmene tingagwiritsire ntchito mfundozo
kufotokoza mwachidule chitsanzo chogwirizana ndi mfundo yaikulu ya mundimeyo