Khalani Womangirira
1 Popeza kuti tikukhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa,” tonsefe timafuna chilimbikitso. (2 Tim. 3:1) Podziŵa bwino lomwe za chofunika chimenechi m’tsiku lake, Paulo anali wolakalaka kugwiritsira ntchito mpata wa kuonana ndi abale ake kuti ‘alimbikitsane wina ndi mnzake.’ Iye anasonkhezera abale ake ‘kulondola zinthu . . . zakulimbikitsana wina ndi mnzake.’ (Aroma 1:11, 12, NW; 14:19) Zoyesayesa zimenezi zinakhala ndi chipambano pa ‘kulimbikitsa mitima ya akuphunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m’chikhulupiriro.’ (Mac. 14:22) Timafunikira kwambiri chilimbikitso cha mtundu umenewo lerolino.
2 Tingakhale omangirira kwa ena mwa zimene tinena. Pamene tigwiritsira ntchito bwino mawu athu, angakhale monga “zipatso zagolidi m’nsengwa zasiliva.” (Miy. 25:11) Mwa kukhala ndi phande pamisonkhano, ‘timalimbikitsana wina ndi mnzake.’ (Aheb. 10:25, NW ) Lilime lathu lingagwiritsiridwe ntchito mwa njira yabwino pamene tisimba zokumana nazo, kuthokoza ena, kapena mwa kukambitsirana zinthu zauzimu. Kugwiritsira ntchito lilime kwabwino koteroko kuli ‘komangirira . . . . kopatsa chisomo kwa iwo akumva.’—Aef. 4:29.
3 Lankhulani za Zinthu Zomangirira: Pa Afilipi 4:8, Paulo anapereka zitsogozo zothandiza pa malankhulidwe athu. Iye anati tiyenera kulingalira pa zinthu zoona, zolemekezeka, zolungama, zoyera, zokongola, zomveka zokoma, ndi zotamandika. Tingakhale otsimikiza nthaŵi zonse kuti zimene timanena zidzakhala zoona ndi zopindulitsa ena ngati zili zozikidwa pa Mawu a Mulungu. (Yohane 17:17) Kudzipatulira kwathu Kwachikristu, zimene timaphunzira pamisonkhano yampingo, mmene timachitira utumiki wathu, ndi zina zotero zili zolemekezeka. Makambitsirano abwino onena za miyezo ndi zitsogozo za Mawu a Mulungu adzatithandizadi kukhala ‘a nzeru yofikira chipulumutso.’ (2 Tim. 3:15) Tingasonyeze chiyamikiro chathu pa makhalidwe oyera osonyezedwa ndi awo amene ali m’gulu la Yehova loyera. Tingathokoze machitidwe okongola a kukoma mtima kwa abale athu. (Yoh. 13:34, 35) Zinthu zimene zili zomveka zokoma zimaphatikizapo mikhalidwe Yachikristu ya chikhulupiriro, chimwemwe, mtendere, ndi kuleza mtima zimene timaona mwa abale athu. Kukambitsirana za zinthu zoyera ndi zotamandika zoterozo kuli ‘kwabwino ndi kolimbikitsa’ ena.—Aroma 15:2.
4 Tsiku lililonse, timayang’anizana ndi nkhaŵa zolefula za dzikoli. Kumakhala kotsitsimula chotani nanga kukankhira pambali zinthu zoterozo ndi kumayanjana mwachikondi ndi abale athu! Nthaŵi yabwino imene timakhala nawo pamodzi ili chuma choyenera kuchisamalira bwino. Ngati nthaŵi zonse tikhala olimbikitsa ndi omangirira, ena adzanenadi za ife kuti: “Anatsitsimutsa mzimu wanga.”—1 Akor. 16:18.