Limbikitsanani Mukakhala mu Utumiki
1 Tonsefe timasangala wina akatiuza mawu olimbikitsa “a pa nthawi yake.” (Miy. 25:11) Tikakhala ndi anzathu muutumiki, kodi tingatani kuti nkhani zathu zizilimbikitsa ena?
2 Kambiranani Nkhani Zolimbikitsa: Zimakhala zolimbikitsa kukambirana zinthu zauzimu tikamalalikira. (Sal. 37:30) Tingakambirane za mmene tinalalikirira munthu wina kapena tingakambe za zinthu zosangalatsa zimene tinakumana nazo posachedwapa muutumiki wa kumunda. (Mac. 15:3) Tikhozanso kunena mfundo yosangalatsa imene tinaipeza powerenga Baibulo, magazini atsopano kapena pamsonkhano wa mpingo. Tinganenenso mfundo zosangalatsa zimene zinakambidwa m’nkhani ya onse imene tinamvetsera posachedwapa ku Nyumba ya Ufumu.
3 Nthawi zina tingakhumudwe mwininyumba akayambitsa nkhani yotitsutsa imene sitingathe kuyankhapo bwinobwino. Tikachoka pa nyumbapo, zingakhale bwino kwambiri kukambirana ndi mnzathu amene tili naye muutumiki, zimene tingadzachite ulendo wina tikadzakumananso ndi zoterozo. Tikhoza kukambirana mfundo zimene zili m’buku la Kukambitsirana. Tikasangalala ndi mfundo ina imene mnzathu ananena polalikira, kunena mochokera pansi pamtima mawu omuyamikira, kungamulimbikitse.
4 Yambani Ndinu: Kodi pagulu lathu la phunziro la buku pali anthu ena amene tatenga nthawi tisanayende nawo muutumiki? ‘Tingalimbikitsane’ ngati titapempha anthu oterowo kuti tiyende nawo limodzi. (Aroma 1:12) Apainiya okhazikika ndi othandiza amayamikira kukhala ndi wina woti ayende naye, makamaka m’mamawa kapena madzulo kwambiri pamene ofalitsa ambiri sakonda kulowa mu utumiki. Tikamalowa mu utumiki ndi apainiya panthawi imeneyi, timawalimbikitsa. Kodi muli ndi wofalitsa wathanzi lofooka amene amalephera kuchita zambiri muutumiki? Kukonza zoyenda ndi wofalitsa wotere, mwinamwake pokachititsa phunziro la Baibulo, kungalimbikitse nonse.—Miy. 27:17.
5 Nthawi zonse kuyamikira ndi kunena mawu osonyeza kuti mnzathu amachita bwino, ngakhale pazinthu zazing’ono, kumalimbikitsa. Tiyenera kukumbukira mfundo imeneyi tikakhala ndi ena muutumiki, chifukwa cholinga chathu ndi ‘kupitiriza . . . kulimbikitsana wina ndi mnzake.’—1 Ates. 5:11.